የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ

At-Târiq

external-link copy
1 : 86

وَٱلسَّمَآءِ وَٱلطَّارِقِ

Ndikulumbilira ku mwamba ndi Nyenyezi imene imadza usiku, info
التفاسير:

external-link copy
2 : 86

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلطَّارِقُ

Chitakudziwitse nchiyani za Nyenyezi yodza usikuyo? info
التفاسير:

external-link copy
3 : 86

ٱلنَّجۡمُ ٱلثَّاقِبُ

Imeneyo ndi nyenyezi yowala kwambiri (mu mdima). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 86

إِن كُلُّ نَفۡسٖ لَّمَّا عَلَيۡهَا حَافِظٞ

Ndithudi palibe mzimu uliwonse koma uli ndi msungi wake (amene akuuyang’anira ndikulemba zonse zochita zake). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 86

فَلۡيَنظُرِ ٱلۡإِنسَٰنُ مِمَّ خُلِقَ

Aganizire munthu, kodi adalengedwa kuchokera kuchiyani? info
التفاسير:

external-link copy
6 : 86

خُلِقَ مِن مَّآءٖ دَافِقٖ

Adalengedwa kuchokera ku madzi ofwamphuka. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 86

يَخۡرُجُ مِنۢ بَيۡنِ ٱلصُّلۡبِ وَٱلتَّرَآئِبِ

Amatuluka kuchokera pakati pa mafupa a msana (wa mwamuna) ndi chifuwa (cha mkazi). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 86

إِنَّهُۥ عَلَىٰ رَجۡعِهِۦ لَقَادِرٞ

Ndithu Iye ndiwakutha, kumbwezeranso (ku moyo pa mbuyo pa imfa). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 86

يَوۡمَ تُبۡلَى ٱلسَّرَآئِرُ

Tsiku limene zobisika zonse zidzaonekera poyera. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 86

فَمَا لَهُۥ مِن قُوَّةٖ وَلَا نَاصِرٖ

Munthu sadzakhala ndi mphamvu (tsiku limenelo zodzitetezera iye mwini) ndiponso sadzakhala ndi mtetezi. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 86

وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلرَّجۡعِ

Ndikulumbiliranso mitambo yobweretsabweretsa mvula. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 86

وَٱلۡأَرۡضِ ذَاتِ ٱلصَّدۡعِ

Ndi nthaka imene imang’ambika (potulutsa m’mera), info
التفاسير:

external-link copy
13 : 86

إِنَّهُۥ لَقَوۡلٞ فَصۡلٞ

Ndithudi iyi (Qur’an) ndi mawu olekanitsa (Haqq ndi Bâtwil - choona ndi chonama). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 86

وَمَا هُوَ بِٱلۡهَزۡلِ

Imeneyi sinkhambakamwa. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 86

إِنَّهُمۡ يَكِيدُونَ كَيۡدٗا

Ndithudi iwo akukonza chiwembu.[416] info

[416] (Ndime15-16) Tanthauzo lake ndikuti akafiri (osakhulupilira) akuchita ndale kuti azimitse dangalira la Qur’an ndikuyesetsa kuti awabweze amene adakhulupilira ndiponso ndikufuna kumupha Mneneri (s.a.w). Naye Allah akuwachitira ndale powaonongera ziwembu zawo zomwe amazikonza.

التفاسير:

external-link copy
16 : 86

وَأَكِيدُ كَيۡدٗا

Nanenso ndikuwakonzera chiwembu (champhamvu kwambiri chimene sangathe kuchipewa). info
التفاسير:

external-link copy
17 : 86

فَمَهِّلِ ٱلۡكَٰفِرِينَ أَمۡهِلۡهُمۡ رُوَيۡدَۢا

Basi, apatse nthawi osakhulupirira apatse nthawi pang’ono, (aona posachedwa). info
التفاسير: