የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ

An-Nâzi’ât

external-link copy
1 : 79

وَٱلنَّٰزِعَٰتِ غَرۡقٗا

Ndikulumbilira (angelo) amene amazula mwamphamvu (mizimu ya osakhulupirira).[379] info

[379] (Ndime 1-5) M’Qur’an nthawi zambiri Allah amalumbilira zolengedwa Zake; zamoyo ndi zopanda moyo, zooneka ndi zosaoneka. Cholinga ndikutilimbikitsa kuti tikhale olingalira luso Lake pa chinthu chilichonse chimene wachilumbilira kuti tizindikire ulemelero Wake ndi mphamvu Zake zoposa.

التفاسير:

external-link copy
2 : 79

وَٱلنَّٰشِطَٰتِ نَشۡطٗا

Ndikulumbiliranso (angelo) amene amachotsa moleza (mizimu ya okhulupirira). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 79

وَٱلسَّٰبِحَٰتِ سَبۡحٗا

Ndi omwe amasambira (nayo mizimuyo) mu mlengalenga (ponka nayo ku malo ake oyembekezera). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 79

فَٱلسَّٰبِقَٰتِ سَبۡقٗا

Ndi iwo amene akupikisana pokwaniritsa malamulo a Allah. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 79

فَٱلۡمُدَبِّرَٰتِ أَمۡرٗا

Ndi iwo (angelo) amene akulongosola malamulo (Ake). (Ndithudi inu anthu mudzauka kwa akufa). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 79

يَوۡمَ تَرۡجُفُ ٱلرَّاجِفَةُ

Patsiku lomwe (lipenga loyamba lidzaimbidwa), dziko lapansi ndi mapiri ake zidzagwedezeka (ndipo aliyense adzafa). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 79

تَتۡبَعُهَا ٱلرَّادِفَةُ

Ndipo kudzatsatira kuyimba kwa lipenga lachiwiri (kumene kudzaukitsa akufa onse). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 79

قُلُوبٞ يَوۡمَئِذٖ وَاجِفَةٌ

Tsiku limenelo mitima idzanjenjemera ndi kuopa. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 79

أَبۡصَٰرُهَا خَٰشِعَةٞ

Maso a eni mitimayo adzakhala ozyolika (chifukwa chamadandaulo); info
التفاسير:

external-link copy
10 : 79

يَقُولُونَ أَءِنَّا لَمَرۡدُودُونَ فِي ٱلۡحَافِرَةِ

(Osakhulupirira) akunena: “Kodi nzoona tidzabwezedwa pambuyo pa imfa monga tidalili kale?” info
التفاسير:

external-link copy
11 : 79

أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمٗا نَّخِرَةٗ

“Pomwe ife titakhala mafupa ofumbwa (tingabwezedwe ndi kuukitsidwa mwa tsopano)?” info
التفاسير:

external-link copy
12 : 79

قَالُواْ تِلۡكَ إِذٗا كَرَّةٌ خَاسِرَةٞ

Adanena (mokanira ndi mwachipongwe): “Choncho kubwerera kumeneko ngati kudzakhalepodi kudzakhala kotaika (ndi kopanda phindu kwa ife. Pomwe ife sindife oyenera kutaika).” info
التفاسير:

external-link copy
13 : 79

فَإِنَّمَا هِيَ زَجۡرَةٞ وَٰحِدَةٞ

(Musaganize kubwererako nchinthu chovuta). Ndithundithu Kiyamayo ndi nkuwo umodzi. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 79

فَإِذَا هُم بِٱلسَّاهِرَةِ

Mwadzidzidzi (zolengedwa zonse) zidzangoona zili pa dziko latsopano (zili zamoyo). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 79

هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ مُوسَىٰٓ

Kodi yakufika (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Mûsa?[380] info

[380] Kuyambira Ayah iyi mpaka Ayah 26 Allah akumtonthoza mneneri Wake pomuuza nkhani ya Mneneri Musa momwe Farawo adamkanira, ndikuti asaganize kuti vutoli lampeza iye yekha koma kuti aneneri enanso akale lidawaonekeranso. Ndiponso m’ma Ayah amenewa muli chenjezo kwa akafiri kuti aope Allah kuti asawalange monga adamulangira Farawo ndi anthu ake amene adali kutsutsana ndi Allah.

التفاسير:

external-link copy
16 : 79

إِذۡ نَادَىٰهُ رَبُّهُۥ بِٱلۡوَادِ ٱلۡمُقَدَّسِ طُوًى

Pamene Mbuye wake adamuitana pa chigwa choyera (chotchedwa) Tuwaa. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 79

ٱذۡهَبۡ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ

(Adamuuza kuti) pita kwa Farawo ndithu iye wapyola malire, (mkudzitukumula kwake ndikupondereza anthu). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 79

فَقُلۡ هَل لَّكَ إِلَىٰٓ أَن تَزَكَّىٰ

Choncho ukamuuze kuti: “Kodi ukufuna kudziyeretsa?” info
التفاسير:

external-link copy
19 : 79

وَأَهۡدِيَكَ إِلَىٰ رَبِّكَ فَتَخۡشَىٰ

“Ndikuti ndikuongolere kwa Mbuye wako kuti uzimuopa?” info
التفاسير:

external-link copy
20 : 79

فَأَرَىٰهُ ٱلۡأٓيَةَ ٱلۡكُبۡرَىٰ

(Basi Mûsa) adamuonetsa (Farawo) chozizwitsa chachikulu. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 79

فَكَذَّبَ وَعَصَىٰ

Koma (Farawo) adatsutsa (Mûsa pazimene adadza nazo zija) ndi kunyoza. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 79

ثُمَّ أَدۡبَرَ يَسۡعَىٰ

Kenaka adabwerera uku akulimbika kutsutsana naye (Allah), info
التفاسير:

external-link copy
23 : 79

فَحَشَرَ فَنَادَىٰ

Adawasonkhanitsa (afiti) uku akuitana anthu; info
التفاسير:

external-link copy
24 : 79

فَقَالَ أَنَا۠ رَبُّكُمُ ٱلۡأَعۡلَىٰ

Nanena: “Ine ndine mbuye wanu wapamwambamwamba!” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 79

فَأَخَذَهُ ٱللَّهُ نَكَالَ ٱلۡأٓخِرَةِ وَٱلۡأُولَىٰٓ

Pamenepo Allah adamulanga chifukwa cha mawu ake omaliza ndi oyamba. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 79

إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبۡرَةٗ لِّمَن يَخۡشَىٰٓ

Ndithu pa zimenezi pali phunziro (lalikulu) kwa yemwe akuopa Allah. info
التفاسير:

external-link copy
27 : 79

ءَأَنتُمۡ أَشَدُّ خَلۡقًا أَمِ ٱلسَّمَآءُۚ بَنَىٰهَا

Kodi kulengedwa kwanu, (inu osakhulupirira kuti muuke) nkovuta kapena thambo limene adalimanga (posonkhanitsa mbali zake zosiyanasiyana ndikukhala chinthu chimodzi)?[381] info

[381] Tanthauzo lake ndikuti: “Kodi chilengedwe chanu nchovuta kwambiri kuposa chilengedwe cha thambo pamene inu mukuganiza kuti Allah sangathe kukudzutsani pambuyo pa imfa?”

التفاسير:

external-link copy
28 : 79

رَفَعَ سَمۡكَهَا فَسَوَّىٰهَا

Adatukula nsinkhu wake ndikulikonza bwino (popanda pena pong’ambika kapena posiyana ndi pena). info
التفاسير:

external-link copy
29 : 79

وَأَغۡطَشَ لَيۡلَهَا وَأَخۡرَجَ ضُحَىٰهَا

Ndipo amauvindikira usiku wake ndi mdima ndipo amatulutsa kuwala wake. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 79

وَٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ ذَٰلِكَ دَحَىٰهَآ

Ndipo pambuyo pazimenezo, nthaka adaiyala (kuti ikhale yoyenera kuikhala). info
التفاسير:

external-link copy
31 : 79

أَخۡرَجَ مِنۡهَا مَآءَهَا وَمَرۡعَىٰهَا

Adatulutsa m’menemo madzi ake (potulutsa akasupe) ndikumeretsa msipu wake; info
التفاسير:

external-link copy
32 : 79

وَٱلۡجِبَالَ أَرۡسَىٰهَا

Ndipo mapiri adawakhazikitsa (ndikuwalimbika); info
التفاسير:

external-link copy
33 : 79

مَتَٰعٗا لَّكُمۡ وَلِأَنۡعَٰمِكُمۡ

(Adachita zonsezi) chifukwa chokusangalatsani inu ndi ziweto zanu.[382] info

[382] Mu Ayah iyi Allah akusonyeza kuti Iye ndi Mwini mphamvu zonse zochitira chinthu chilichonse chachikulu kuposa kuwaukitsa akufa; ndiponso akukumbutsa ufulu Wake waukulu womwe adatichitira potipatsa zinthu zonsezo kuti tithandizike nazo.

التفاسير:

external-link copy
34 : 79

فَإِذَا جَآءَتِ ٱلطَّآمَّةُ ٱلۡكُبۡرَىٰ

Choncho likadzafika tsoka lalikulu (tsiku la Qiyâma). info
التفاسير:

external-link copy
35 : 79

يَوۡمَ يَتَذَكَّرُ ٱلۡإِنسَٰنُ مَا سَعَىٰ

Tsiku limenelo munthu adzakumbukira zimene adachita, (zabwino ndi zoipa). info
التفاسير:

external-link copy
36 : 79

وَبُرِّزَتِ ٱلۡجَحِيمُ لِمَن يَرَىٰ

Ndipo Moto waukali udzawonetsedwa kwa yense openya. info
التفاسير:

external-link copy
37 : 79

فَأَمَّا مَن طَغَىٰ

Tsono amene adapyola malire (pochita machimo), info
التفاسير:

external-link copy
38 : 79

وَءَاثَرَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا

Ndikudzisankhira (yekha) moyo wa pa dziko lapansi, info
التفاسير:

external-link copy
39 : 79

فَإِنَّ ٱلۡجَحِيمَ هِيَ ٱلۡمَأۡوَىٰ

Ndithu Jahannam ndiwo malo ake. info
التفاسير:

external-link copy
40 : 79

وَأَمَّا مَنۡ خَافَ مَقَامَ رَبِّهِۦ وَنَهَى ٱلنَّفۡسَ عَنِ ٱلۡهَوَىٰ

Tsono amene akuopa kuti adzaimilira pamaso pa Mbuye wake, nauletsa mtima wake ku zilakolako zoipa, info
التفاسير:

external-link copy
41 : 79

فَإِنَّ ٱلۡجَنَّةَ هِيَ ٱلۡمَأۡوَىٰ

Ndithu Munda wamtendere ndiwo adzakhale malo ake. info
التفاسير:

external-link copy
42 : 79

يَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلسَّاعَةِ أَيَّانَ مُرۡسَىٰهَا

Akukufunsa (iwe Mtumiki) (s.a.w) za nthawi (ya tsiku lachimaliziro kuti): “Idzakhala liti?” info
التفاسير:

external-link copy
43 : 79

فِيمَ أَنتَ مِن ذِكۡرَىٰهَآ

Uli ndi mphamvu yanji iwe yofotokozera za tsikulo? (Iwe ulibe kuzindikira za nthawiyo kotero kuti ungaitchule kwa iwo). info
التفاسير:

external-link copy
44 : 79

إِلَىٰ رَبِّكَ مُنتَهَىٰهَآ

Kwa Mbuye wako ndiko kuli mathero ake. info
التفاسير:

external-link copy
45 : 79

إِنَّمَآ أَنتَ مُنذِرُ مَن يَخۡشَىٰهَا

Iwe (ntchito yako) ndikuwachenjeza amene akuiopa; (osati kulengeza zanthawi yake). info
التفاسير:

external-link copy
46 : 79

كَأَنَّهُمۡ يَوۡمَ يَرَوۡنَهَا لَمۡ يَلۡبَثُوٓاْ إِلَّا عَشِيَّةً أَوۡ ضُحَىٰهَا

Tsiku limene adzaiona adzakhala ngati sadakhale (pa dziko nthawi yayitali), koma ngati madzulo amodzi kapena masana ake (nthawi ya m’mawa).[383] info

[383] Apa tanthauzo lake ndikuti adzaona masiku onse amene adakhala m’dziko ngati lidali ola limodzi.

التفاسير: