የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ

የገፅ ቁጥር:close

external-link copy
14 : 72

وَأَنَّا مِنَّا ٱلۡمُسۡلِمُونَ وَمِنَّا ٱلۡقَٰسِطُونَۖ فَمَنۡ أَسۡلَمَ فَأُوْلَٰٓئِكَ تَحَرَّوۡاْ رَشَدٗا

Ndithu mwa ife alipo Asilamu ndiponso mwa ife alipo opatuka (mu njira ya chilungamo); amene walowa m’Chisilamu, iwowo ndi amene alunjika njira ya choonadi. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 72

وَأَمَّا ٱلۡقَٰسِطُونَ فَكَانُواْ لِجَهَنَّمَ حَطَبٗا

Koma opatuka (kunjira ya chilungamo) adzakhala nkhuni za Jahannam.” info
التفاسير:

external-link copy
16 : 72

وَأَلَّوِ ٱسۡتَقَٰمُواْ عَلَى ٱلطَّرِيقَةِ لَأَسۡقَيۡنَٰهُم مَّآءً غَدَقٗا

Ndithu (anthu ndi ziwanda) akadalungama panjira ya chilungamo tikadawamwetsa madzi ambiri (okwanira nyengo zonse). info
التفاسير:

external-link copy
17 : 72

لِّنَفۡتِنَهُمۡ فِيهِۚ وَمَن يُعۡرِضۡ عَن ذِكۡرِ رَبِّهِۦ يَسۡلُكۡهُ عَذَابٗا صَعَدٗا

Kuti tiwayese ndi zimenezo (mmene angamyamikire Allah pa mtendere Wake pa iwo). Koma amene anyozera kupembedza Mbuye wake, amlowetsa ku chilango chovuta (chimene sangathe kupirira nacho). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 72

وَأَنَّ ٱلۡمَسَٰجِدَ لِلَّهِ فَلَا تَدۡعُواْ مَعَ ٱللَّهِ أَحَدٗا

Ndithu misikiti ndi ya Allah yekha! Choncho, musapembedze aliyense pamodzi ndi Allah. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 72

وَأَنَّهُۥ لَمَّا قَامَ عَبۡدُ ٱللَّهِ يَدۡعُوهُ كَادُواْ يَكُونُونَ عَلَيۡهِ لِبَدٗا

Ndipo ndithu pamene adaima kapolo wa Allah (Muhammad{s.a.w}, pa Swala yake) uku akumpembedza (Allah), ziwanda zidatsala pang’ono kumgwera (chifukwa cha kuchuluka kwawo ndi kumzinga podabwa ndi zimene adaziona ndi kuzimva). info
التفاسير:

external-link copy
20 : 72

قُلۡ إِنَّمَآ أَدۡعُواْ رَبِّي وَلَآ أُشۡرِكُ بِهِۦٓ أَحَدٗا

Nena: “Ndikumpembedza Mbuye wanga M’modzi (Yekha) ndipo sindingamphatikize ndi aliyense (m’mapemphero Ake).” info
التفاسير:

external-link copy
21 : 72

قُلۡ إِنِّي لَآ أَمۡلِكُ لَكُمۡ ضَرّٗا وَلَا رَشَدٗا

Nena: “Ine ndilibe udindo wokupatsani mavuto kapena chilungamo (ndi zabwino).” info
التفاسير:

external-link copy
22 : 72

قُلۡ إِنِّي لَن يُجِيرَنِي مِنَ ٱللَّهِ أَحَدٞ وَلَنۡ أَجِدَ مِن دُونِهِۦ مُلۡتَحَدًا

Nena: “Ine palibe anganditeteze ku chilango cha Allah (ngati nditamnyoza) sindingapeze malo (othawira kuchilango Chake) kupatula kwa Iye.” info
التفاسير:

external-link copy
23 : 72

إِلَّا بَلَٰغٗا مِّنَ ٱللَّهِ وَرِسَٰلَٰتِهِۦۚ وَمَن يَعۡصِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ فَإِنَّ لَهُۥ نَارَ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًا

“Koma (mphamvu imene ndili nayo) ndikufikitsa uthenga wa Allah umene adanditumizira; ndithu amene anyoza Allah ndi Mtumiki Wake (ndi kupatuka pa chipembedzo cha (Allah) ndithu moto wa Jahannam ndi wake, akakhala m’menemo muyaya.” info
التفاسير:

external-link copy
24 : 72

حَتَّىٰٓ إِذَا رَأَوۡاْ مَا يُوعَدُونَ فَسَيَعۡلَمُونَ مَنۡ أَضۡعَفُ نَاصِرٗا وَأَقَلُّ عَدَدٗا

Mpaka pomwe adzaziona zimene alonjezedwa ndipamene adzadziwa (kuti) kodi ndani mwini mthandizi wofooka ndiponso wochepekedwa mchiwerengero (cha omtsatira, iwo kapena Asilamu).” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 72

قُلۡ إِنۡ أَدۡرِيٓ أَقَرِيبٞ مَّا تُوعَدُونَ أَمۡ يَجۡعَلُ لَهُۥ رَبِّيٓ أَمَدًا

Nena (kuti): “Sindikudziwa ngati zomwe mukulonjezedwa (za chilango) zili pafupi, kapena Mbuye wanga azitalikitsa.” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 72

عَٰلِمُ ٱلۡغَيۡبِ فَلَا يُظۡهِرُ عَلَىٰ غَيۡبِهِۦٓ أَحَدًا

“(Iye) ndi wodziwa zobisika; sazionetsa zobisika Zake kwa aliyense (mzolengedwa Zake),” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 72

إِلَّا مَنِ ٱرۡتَضَىٰ مِن رَّسُولٖ فَإِنَّهُۥ يَسۡلُكُ مِنۢ بَيۡنِ يَدَيۡهِ وَمِنۡ خَلۡفِهِۦ رَصَدٗا

“Kupatula Mtumiki (Wake) amene wamuyanja; (iyeyo amamdziwitsa zobisikazo) ndipo ndithu amamuikira alonda kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake (omulonda).” info
التفاسير:

external-link copy
28 : 72

لِّيَعۡلَمَ أَن قَدۡ أَبۡلَغُواْ رِسَٰلَٰتِ رَبِّهِمۡ وَأَحَاطَ بِمَا لَدَيۡهِمۡ وَأَحۡصَىٰ كُلَّ شَيۡءٍ عَدَدَۢا

“Kuti adziwe ngati afikitsa uthenga wa Mbuye wawo, ndipo wawazungulira (podziwa zonse zili kwa iwo) ndipo wadziwa kuchuluka kwa zinthu zonse zimene zilipo; (palibe chobisika kwa Iye).” info
التفاسير: