የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ

የገፅ ቁጥር:close

external-link copy
24 : 22

وَهُدُوٓاْ إِلَى ٱلطَّيِّبِ مِنَ ٱلۡقَوۡلِ وَهُدُوٓاْ إِلَىٰ صِرَٰطِ ٱلۡحَمِيدِ

Ndipo adzatsogozedwa (kupita kumalo) kokamba mawu abwino okhaokha; ndiponso adzatsogozedwa ku njira ya Mwini kutamandidwa (kunjira yonkera ku Jannah). info
التفاسير:

external-link copy
25 : 22

إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَيَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ ٱلَّذِي جَعَلۡنَٰهُ لِلنَّاسِ سَوَآءً ٱلۡعَٰكِفُ فِيهِ وَٱلۡبَادِۚ وَمَن يُرِدۡ فِيهِ بِإِلۡحَادِۭ بِظُلۡمٖ نُّذِقۡهُ مِنۡ عَذَابٍ أَلِيمٖ

Ndithu. amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndipo nkumatsekereza ena ku njira ya Allah, (ndiponso nkumatsekereza kulowa) mu Msikiti Wopatulika umene tidauchita kuti ukhale wa anthu onse mofanana kwa amene akukhala m’menemo ndi kwa alendo, (anthu otere tidzawalanga ndi chilango chaukali), ndipo aliyense wofuna kuchita zopotoka m’menemo mosalungama, timulawitsa chilango chowawa zedi. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 22

وَإِذۡ بَوَّأۡنَا لِإِبۡرَٰهِيمَ مَكَانَ ٱلۡبَيۡتِ أَن لَّا تُشۡرِكۡ بِي شَيۡـٔٗا وَطَهِّرۡ بَيۡتِيَ لِلطَّآئِفِينَ وَٱلۡقَآئِمِينَ وَٱلرُّكَّعِ ٱلسُّجُودِ

Ndipo (kumbukira) pamene tidamkhazika Ibrahim (ndi kumlondolera) pamalo pa Nyumba (yopatulikayo; tidamuuza kuti): “Usandiphatikize ndi chilichonse; ndipo iyeretse nyumba yanga chifukwa cha amene akuizungulira ndi kumakhala pompo (pochita mapemphero awo); ndi omwe amawerama ndi kugwetsa nkhope zawo pansi.[290] info

[290] Allah akuuza Mtumiki Muhammad (s.a.w) kuti akambire opembedza mafano zankhani ya Ibrahim yemwe iwo amati akumutsata pakupembedza kwawo mafano ndi kuichita nyumba yopatulikayo kukhala nyumba yopembedzera mafano kuti Ibrahim adamulondolera pamalo anyumbayo ndi kumlamula kuti aimange ndikuti asandiphatikize pamapemphero ndi china chilichonse, ndikuti aiyeretse nyumba ya Allah kuuve wamafano ndi uve wina uliwonse kuti pakhale pamalo pozungulira chifukwa choopa Allah. Nanga bwanji iwo apasankha kukhala popembedzera mafano.

التفاسير:

external-link copy
27 : 22

وَأَذِّن فِي ٱلنَّاسِ بِٱلۡحَجِّ يَأۡتُوكَ رِجَالٗا وَعَلَىٰ كُلِّ ضَامِرٖ يَأۡتِينَ مِن كُلِّ فَجٍّ عَمِيقٖ

Ndipo (tidamuuza): “Lengeza kwa anthu za Hajj; akudzera (ena) oyenda ndi mapazi, ndipo (ena ali) pamwamba pa chiweto choonda (chifukwa chamasautso a paulendo); adza kuchokera kunjira zamtalimtali. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 22

لِّيَشۡهَدُواْ مَنَٰفِعَ لَهُمۡ وَيَذۡكُرُواْ ٱسۡمَ ٱللَّهِ فِيٓ أَيَّامٖ مَّعۡلُومَٰتٍ عَلَىٰ مَا رَزَقَهُم مِّنۢ بَهِيمَةِ ٱلۡأَنۡعَٰمِۖ فَكُلُواْ مِنۡهَا وَأَطۡعِمُواْ ٱلۡبَآئِسَ ٱلۡفَقِيرَ

Kuti adzaone zabwino zawo, ndikuti (achulukitse) kutchula dzina la Allah m’masiku odziwika (ubwino wake), kupyolera m’zimene wawapatsa monga ziweto za miyendo inayi. Ndipo idyani ina mwa nyamayo ndi kum’dyetsa wovutika, wosauka. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 22

ثُمَّ لۡيَقۡضُواْ تَفَثَهُمۡ وَلۡيُوفُواْ نُذُورَهُمۡ وَلۡيَطَّوَّفُواْ بِٱلۡبَيۡتِ ٱلۡعَتِيقِ

Kenako adziyeretse kuzitakataka zawo, ndipo akwaniritse naziri (malonjezo) zawo ndikuzungulira nyumba yakale. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 22

ذَٰلِكَۖ وَمَن يُعَظِّمۡ حُرُمَٰتِ ٱللَّهِ فَهُوَ خَيۡرٞ لَّهُۥ عِندَ رَبِّهِۦۗ وَأُحِلَّتۡ لَكُمُ ٱلۡأَنۡعَٰمُ إِلَّا مَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡۖ فَٱجۡتَنِبُواْ ٱلرِّجۡسَ مِنَ ٱلۡأَوۡثَٰنِ وَٱجۡتَنِبُواْ قَوۡلَ ٱلزُّورِ

Umo ndi momwe zikhalire; ndipo amene alemekeze zinthu zopatulika za Allah kutero ndi bwino kwa iyeyo pamaso pa Mbuye wake. Ndipo ziweto za miyendo inayi nzovomerezeka kwa inu kuzidya, kupatula zomwe zatchulidwa kwa inu (m’Qur’an kuti nzoletsedwa); choncho upeweni uve wa mafano, ndiponso pewani mawu abodza. info
التفاسير: