የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ

የገፅ ቁጥር:close

external-link copy
55 : 16

لِيَكۡفُرُواْ بِمَآ ءَاتَيۡنَٰهُمۡۚ فَتَمَتَّعُواْ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ

Ncholinga choti akane mtendere umene tawapatsa, choncho sangalalani pang’ono, posachedwapa mudziwa (mapeto a zochita zanu). info
التفاسير:

external-link copy
56 : 16

وَيَجۡعَلُونَ لِمَا لَا يَعۡلَمُونَ نَصِيبٗا مِّمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡۗ تَٱللَّهِ لَتُسۡـَٔلُنَّ عَمَّا كُنتُمۡ تَفۡتَرُونَ

Ndipo gawo la zomwe tawapatsa akuliikira (milungu yawo yabodza) yomwe siizindikira chilichonse. Tallahi, (ndikulumbira Allah,) ndithudi, mudzafunsidwa pa zimene munkapeka. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 16

وَيَجۡعَلُونَ لِلَّهِ ٱلۡبَنَٰتِ سُبۡحَٰنَهُۥ وَلَهُم مَّا يَشۡتَهُونَ

Ndipo (mwaumbuli) akumuikira Allah ana aakazi (ponena kuti adabereka ana aakazi) Subuhana! (Wayera Allah kuzimenezi!) Ndipo iwo (eni) amadzifunira amene amawakonda (omwe ndi ana achimuna)! info
التفاسير:

external-link copy
58 : 16

وَإِذَا بُشِّرَ أَحَدُهُم بِٱلۡأُنثَىٰ ظَلَّ وَجۡهُهُۥ مُسۡوَدّٗا وَهُوَ كَظِيمٞ

Ndipo mmodzi wawo akauzidwa nkhani ya (kuti wabereka) mwana wamkazi nkhope yake imada, ndipo amadzala ndi madandaulo. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 16

يَتَوَٰرَىٰ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ مِن سُوٓءِ مَا بُشِّرَ بِهِۦٓۚ أَيُمۡسِكُهُۥ عَلَىٰ هُونٍ أَمۡ يَدُسُّهُۥ فِي ٱلتُّرَابِۗ أَلَا سَآءَ مَا يَحۡكُمُونَ

Amadzibisa kwa anthu chifukwa chankhani yoipa imene wauzidwa (nayamba kulingalira): Kodi akhale naye pamodzi ndikuyaluka (pamaso pa anthu), kapena angomkwilira m’dothi (ali moyo)? Mverani! Ndi choipa kwabasi chiweruzo chawo.[251] info

[251] Ophatikiza Allah ndi mafano adali kuda ana aakazi. Kubala mwana wamkazi amachiona monga chochititsa manyazi pamaso pa anthu kotero kuti ena mwa iwo akawauza kuti mkazi wawo wabala mwana wamkazi, amakamkwilira mwanayo ali wamoyo chifukwa choopa kunyozedwa pamaso pa anthu, pomwe iwo amawayesa angelo ngati ana aakazi a Allah. Chimene amachida, amampachika nacho Allah, ndipo chomwe amachikonda amati ndicho chawochawo. Izi nzamwano, zomwe osakhulupilira adali kumuyankhulira Allah.

التفاسير:

external-link copy
60 : 16

لِلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ مَثَلُ ٱلسَّوۡءِۖ وَلِلَّهِ ٱلۡمَثَلُ ٱلۡأَعۡلَىٰۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

Kwa awo amene sakhulupirira za tsiku la chimaliziro, ali ndi mbiri yoipa; koma Allah ali ndi mbiri zapamwamba; ndipo Iye Ngwanyonga, Ngwanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
61 : 16

وَلَوۡ يُؤَاخِذُ ٱللَّهُ ٱلنَّاسَ بِظُلۡمِهِم مَّا تَرَكَ عَلَيۡهَا مِن دَآبَّةٖ وَلَٰكِن يُؤَخِّرُهُمۡ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗىۖ فَإِذَا جَآءَ أَجَلُهُمۡ لَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ سَاعَةٗ وَلَا يَسۡتَقۡدِمُونَ

Ndipo Allah akadakhala akulanga anthu (mwachangu) pa zolakwa zawo, sakadasiya ngakhale nyama imodzi pamwamba pa nthaka; koma akuwachedwetsera (chilangocho) mpaka panthawi yoikidwa; ndipo ikadzadza nthawi yawoyo, sangathe kuichedwetsa ngakhale ola limodzi; ndiponso sangathe kuifulumizitsa (ngakhale ola limodzi.) info
التفاسير:

external-link copy
62 : 16

وَيَجۡعَلُونَ لِلَّهِ مَا يَكۡرَهُونَۚ وَتَصِفُ أَلۡسِنَتُهُمُ ٱلۡكَذِبَ أَنَّ لَهُمُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ لَا جَرَمَ أَنَّ لَهُمُ ٱلنَّارَ وَأَنَّهُم مُّفۡرَطُونَ

Ndipo akumuikira Allah zimene (iwo) akuzida (omwe ndi ana aakazi pomati Allah adabala ana aakazi), ndipo malirime awo akunena bodza kuti iwo adzapeza zabwino (kwa Allah); palibe chikaiko, ndithu Moto ndi wawo, ndipo iwo adzasiidwa (mmenemo). info
التفاسير:

external-link copy
63 : 16

تَٱللَّهِ لَقَدۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰٓ أُمَمٖ مِّن قَبۡلِكَ فَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَهُوَ وَلِيُّهُمُ ٱلۡيَوۡمَ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ

Pali Mulungu! Ndithudi tidatumiza (atumiki) kumitundu yomwe idalipo patsogolo pako, koma satana adawakometsera zochita zawo (zoipa ankaziona kuti nzabwino napitiriza kuzichita). Choncho iye (satana) ndi bwenzi wawo lero, (koma pa tsiku la chimaliziro, adzadana naye kwambiri), ndipo iwo adzapata chilango chowawa. info
التفاسير:

external-link copy
64 : 16

وَمَآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ إِلَّا لِتُبَيِّنَ لَهُمُ ٱلَّذِي ٱخۡتَلَفُواْ فِيهِ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٗ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ

Ndipo sitidakutumizire buku (ili) koma kuti uwafotokozere zomwe akusiyana pa izo ndi kuti (likhale) chiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira. info
التفاسير: