《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。

external-link copy
102 : 3

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّقُواْ ٱللَّهَ حَقَّ تُقَاتِهِۦ وَلَا تَمُوتُنَّ إِلَّا وَأَنتُم مُّسۡلِمُونَ

E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah; kuopa kwenikweni. Ndipo musafe pokhapokha mutakhala Asilamu (ogonjera).[76] info

[76] Pa ndime iyi akulangiza kuti nthawi iliyonse munthu akhale m’chikhalidwe cha Chisilamu chokwanira popewa zoletsedwa ndi kumachita zimene alamulidwa kuchita mmene angathere, chifukwa chakuti munthu sangadziwe nthawi imene imfa ingamufikire.

التفاسير: