Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима

Al-A’râf

external-link copy
1 : 7

الٓمٓصٓ

Alif-Lâm-Mîm-Sad. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 7

كِتَٰبٌ أُنزِلَ إِلَيۡكَ فَلَا يَكُن فِي صَدۡرِكَ حَرَجٞ مِّنۡهُ لِتُنذِرَ بِهِۦ وَذِكۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِينَ

(Iyi Qur’an ndi) buku (lopatulika) lomwe lavumbulutsidwa kwa iwe. Choncho chifuwa chako chisabanike ndi ilo (poopa kufikitsa mawu ake kwa anthu kuti angakuyese wabodza;) kuti uwachenjeze nalo (otsutsa) ndi kuti likhale chikumbutso kwa okhulupirira (kuti aonjezere chikhulupiliro chawo).[178] info

[178] Apa akumuuza Mtumiki (s.a.w) kuti asaope kulengeza zimene Allah wamuululira. Asatekeseke ndi otsutsa ngakhale atachuluka chotani. Mlaliki aliyense akuuzidwanso chimodzimodzi. Anene choonadi kwa anthu ndipo asaope kudzudzulidwa.

التفاسير:

external-link copy
3 : 7

ٱتَّبِعُواْ مَآ أُنزِلَ إِلَيۡكُم مِّن رَّبِّكُمۡ وَلَا تَتَّبِعُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَۗ قَلِيلٗا مَّا تَذَكَّرُونَ

Tsatirani zomwe zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu, ndipo musawatsatire omwe sali Allah powayesa atetezi (anu). Ndizochepa zimene mumazikumbukira. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 7

وَكَم مِّن قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَا فَجَآءَهَا بَأۡسُنَا بَيَٰتًا أَوۡ هُمۡ قَآئِلُونَ

Ndimidzi yambiri imene tidaiononga ndipo chilango Chathu chidaidzera nthawi ya usiku, kapena usana iwo atagona tulo tamasana (akupumula monga momwe zinawachitikira anthu a Loti ndi anthu a Shuaib). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 7

فَمَا كَانَ دَعۡوَىٰهُمۡ إِذۡ جَآءَهُم بَأۡسُنَآ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ

Ndipo sikunali kulira kwawo pamene chinawafika chilango chathu koma kunena (ndi kuvomereza): “Ndithudi, ife tinali ochita zoipa.” (Koma kuvomereza kwawoko sikunawapindulire kanthu). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 7

فَلَنَسۡـَٔلَنَّ ٱلَّذِينَ أُرۡسِلَ إِلَيۡهِمۡ وَلَنَسۡـَٔلَنَّ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Mtheradi tidzawafunsa (anthu) amene anatumiziridwa (atumiki), naonso atumikiwo tidzawafunsa. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 7

فَلَنَقُصَّنَّ عَلَيۡهِم بِعِلۡمٖۖ وَمَا كُنَّا غَآئِبِينَ

Tsono tidzawauza mozindikira bwino-bwino (chilichonse chimene ankachita). Ndipo sitidali kutali (nawo pamene ankachita zochita zawo). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 7

وَٱلۡوَزۡنُ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡحَقُّۚ فَمَن ثَقُلَتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ

Ndipo sikero (yoyezera zochita za anthu) tsiku limenelo idzakhala yoona (yopanda chinyengo). Choncho, amene idzalemere miyeso yake (ya zabwino), iwowo ndiwo opambana. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 7

وَمَنۡ خَفَّتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُم بِمَا كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَظۡلِمُونَ

Ndipo amene idzapepuke miyeso yawo (ya zinthu zawo zabwino), iwo ndi amene ataya pachabe moyo wawo chifukwa cha kuzichitira zosalungama zizindikiro Zathu. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 7

وَلَقَدۡ مَكَّنَّٰكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَجَعَلۡنَا لَكُمۡ فِيهَا مَعَٰيِشَۗ قَلِيلٗا مَّا تَشۡكُرُونَ

Ndithudi tinakupatsani mphamvu yokhalira pa dziko, ndipo takupangirani m’menemo zinthu zofunika pa moyo wanu. Koma kuyamika kwanu mpang’ono. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 7

وَلَقَدۡ خَلَقۡنَٰكُمۡ ثُمَّ صَوَّرۡنَٰكُمۡ ثُمَّ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ لَمۡ يَكُن مِّنَ ٱلسَّٰجِدِينَ

Ndithudi, tinakulengani, kenako tidakukonzani (pokupatsani ziwalo) ndi kunena kwa angelo kuti: “Mgwadireni Adam.” Ndipo adamgwadira kupatula Iblis, sadali mwa ogwada. info
التفاسير: