Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима

Бет рақами:close

external-link copy
38 : 3

هُنَالِكَ دَعَا زَكَرِيَّا رَبَّهُۥۖ قَالَ رَبِّ هَبۡ لِي مِن لَّدُنكَ ذُرِّيَّةٗ طَيِّبَةًۖ إِنَّكَ سَمِيعُ ٱلدُّعَآءِ

Pompo Zakariya adapempha Mbuye wake nati: “Mbuye wanga! Ndipatseni kuchokera kwa Inu mwana wabwino. Ndithudi, Inu ndinu Akumva pempho!”[69] info

[69] Mneneri Zakariya ataona zododometsazo, adaganiza kuti nayenso apemphe kuti amninkhe chozizwitsa chobala mwana pomwe adali wokalamba zedi. Nayenso mkazi wake adali chumba. Ndipo adamubaladi mneneri Yahya (Yohane).

التفاسير:

external-link copy
39 : 3

فَنَادَتۡهُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ وَهُوَ قَآئِمٞ يُصَلِّي فِي ٱلۡمِحۡرَابِ أَنَّ ٱللَّهَ يُبَشِّرُكَ بِيَحۡيَىٰ مُصَدِّقَۢا بِكَلِمَةٖ مِّنَ ٱللَّهِ وَسَيِّدٗا وَحَصُورٗا وَنَبِيّٗا مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ

Mwadzidzidzi, mngelo adamuitana uku iye ataimilira akupemphera mchipinda cha m’kachisi: “Allah akukuuza nkhani yabwino (yakuti ubereka mwana; dzina lake) Yahya yemwe adzakhala wotsimikizira (mneneri yemwe adzabadwa) ndi liwu lochokera kwa Allah, (yemwe ndi mneneri Isa (Yesu) amene adzakhalanso wolemekezeka ndi wolungama ndi mneneri wa mwa anthu abwino.” info
التفاسير:

external-link copy
40 : 3

قَالَ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٞ وَقَدۡ بَلَغَنِيَ ٱلۡكِبَرُ وَٱمۡرَأَتِي عَاقِرٞۖ قَالَ كَذَٰلِكَ ٱللَّهُ يَفۡعَلُ مَا يَشَآءُ

(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndidzakhala bwanji ndi mwana pomwe ukalamba wandifikira, nayenso mkazi wanga ndichumba.” (Mngelo adati): “Ndimomwemo; Allah amachita chimene wafuna.” info
التفاسير:

external-link copy
41 : 3

قَالَ رَبِّ ٱجۡعَل لِّيٓ ءَايَةٗۖ قَالَ ءَايَتُكَ أَلَّا تُكَلِّمَ ٱلنَّاسَ ثَلَٰثَةَ أَيَّامٍ إِلَّا رَمۡزٗاۗ وَٱذۡكُر رَّبَّكَ كَثِيرٗا وَسَبِّحۡ بِٱلۡعَشِيِّ وَٱلۡإِبۡكَٰرِ

(Iye) adati: “Mbuye wanga! Ndipatseni chizindikiro!” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu koma momangolozera (ndi chala) basi. Ndipo tamanda Mbuye wako, kutamanda kwambiri ndiponso umlemekeze (popemphera) madzulo ndi m’mawa.” info
التفاسير:

external-link copy
42 : 3

وَإِذۡ قَالَتِ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ يَٰمَرۡيَمُ إِنَّ ٱللَّهَ ٱصۡطَفَىٰكِ وَطَهَّرَكِ وَٱصۡطَفَىٰكِ عَلَىٰ نِسَآءِ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndipo (kumbukira) pamene angelo adati: “E Iwe Mariya! Ndithudi, Allah wakusankha, wakuyeretsa ndipo wakulemekeza, mwa akazi onse amitundu ya anthu.”[70] info

[70] Apa patchulidwa nkhani ya mayi Mariya pomwe mngelo adamuuza nkhani yabwinoyi.

التفاسير:

external-link copy
43 : 3

يَٰمَرۡيَمُ ٱقۡنُتِي لِرَبِّكِ وَٱسۡجُدِي وَٱرۡكَعِي مَعَ ٱلرَّٰكِعِينَ

“E iwe Mariya, dzichepetse kwa Mbuye wako ndi kumlambira powerama pamodzi ndi owerama.” info
التفاسير:

external-link copy
44 : 3

ذَٰلِكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلۡغَيۡبِ نُوحِيهِ إِلَيۡكَۚ وَمَا كُنتَ لَدَيۡهِمۡ إِذۡ يُلۡقُونَ أَقۡلَٰمَهُمۡ أَيُّهُمۡ يَكۡفُلُ مَرۡيَمَ وَمَا كُنتَ لَدَيۡهِمۡ إِذۡ يَخۡتَصِمُونَ

Izi ndizina mwa nkhani zobisika zomwe tikukuvumbulutsira. Sudali nawo pamene amaponya zolembera zawo (m’madzi m’njira ya mayere) kuti aone ndani mwa iwo alere Mariya. Komanso sudali nawo pamene adali kutsutsana. info
التفاسير:

external-link copy
45 : 3

إِذۡ قَالَتِ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ يَٰمَرۡيَمُ إِنَّ ٱللَّهَ يُبَشِّرُكِ بِكَلِمَةٖ مِّنۡهُ ٱسۡمُهُ ٱلۡمَسِيحُ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ وَجِيهٗا فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِ وَمِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ

(Kumbukira) pamene angelo adati: “E iwe Mariya! Ndithu Allah akukuuza nkhani yabwino (kuti ubereka mwana popanda mwamuna koma kupyolera mu) liwu lochokera kwa Iye (Allah, lakuti: “Bereka,” ndipo nkubereka popanda kupezana ndi mwamuna). Dzina lake ndi Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, adzakhala wolemekezeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro; ndiponso ndi mmodzi wa oyandikitsidwa kwa Allah. info
التفاسير: