Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима

Бет рақами:close

external-link copy
160 : 26

كَذَّبَتۡ قَوۡمُ لُوطٍ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Anthu a Luti adatsutsa atumiki. info
التفاسير:

external-link copy
161 : 26

إِذۡ قَالَ لَهُمۡ أَخُوهُمۡ لُوطٌ أَلَا تَتَّقُونَ

Pamene m’bale wawo Luti adanena kwa iwo (kuti): “Kodi simuopa (Allah)?” info
التفاسير:

external-link copy
162 : 26

إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٞ

“Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.” info
التفاسير:

external-link copy
163 : 26

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ

“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.” info
التفاسير:

external-link copy
164 : 26

وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; palibe komwe kuli malipiro anga koma kwa Mbuye wazolengedwa.” info
التفاسير:

external-link copy
165 : 26

أَتَأۡتُونَ ٱلذُّكۡرَانَ مِنَ ٱلۡعَٰلَمِينَ

“Kodi mukugonana ndi amuna (anzanu) muzolengedwa (za Allah), info
التفاسير:

external-link copy
166 : 26

وَتَذَرُونَ مَا خَلَقَ لَكُمۡ رَبُّكُم مِّنۡ أَزۡوَٰجِكُمۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٌ عَادُونَ

“Ndikusiya amene Mbuye wanu adakulengerani kuti akhale akazi anu? Ndithu inu ndinu anthu olumpha malire.” info
التفاسير:

external-link copy
167 : 26

قَالُواْ لَئِن لَّمۡ تَنتَهِ يَٰلُوطُ لَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُخۡرَجِينَ

Iwo adati: “Ngati susiya (izi), E iwe Luti! ndithu ukhala mmodzi wa opirikitsidwa.” info
التفاسير:

external-link copy
168 : 26

قَالَ إِنِّي لِعَمَلِكُم مِّنَ ٱلۡقَالِينَ

Iye adati: “Ndithu ine ndine m’modzi wakuzida izi zochita zanu (choncho Sindisiya kuzidzudzula).” info
التفاسير:

external-link copy
169 : 26

رَبِّ نَجِّنِي وَأَهۡلِي مِمَّا يَعۡمَلُونَ

“E Mbuye wanga! Ndipulumutseni ine ndi banja langa ku (matsoka a) zimene akuchita.” info
التفاسير:

external-link copy
170 : 26

فَنَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ أَجۡمَعِينَ

Ndipo tidampulumutsa iye ndi onse a pa banja lake, info
التفاسير:

external-link copy
171 : 26

إِلَّا عَجُوزٗا فِي ٱلۡغَٰبِرِينَ

Kupatula nkhalamba yaikazi idali mwa otsalira m’mbuyo. info
التفاسير:

external-link copy
172 : 26

ثُمَّ دَمَّرۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ

Titatero tidawaononga enawo. info
التفاسير:

external-link copy
173 : 26

وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِم مَّطَرٗاۖ فَسَآءَ مَطَرُ ٱلۡمُنذَرِينَ

Ndipo tidawavumbwitsira mvula (yamiyala); iyipirenji, mvula ya ochenjezedwa! info
التفاسير:

external-link copy
174 : 26

إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ

Ndithu pazimenezi pali malingaliro. Koma ambiri a iwo sadali okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
175 : 26

وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ

Ndipo, ndithu Mbuye wako, Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
176 : 26

كَذَّبَ أَصۡحَٰبُ لۡـَٔيۡكَةِ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Anthu a m’dziko lamitengo yambiri (Madiana) adatsutsa atumiki. info
التفاسير:

external-link copy
177 : 26

إِذۡ قَالَ لَهُمۡ شُعَيۡبٌ أَلَا تَتَّقُونَ

(Akumbutse) pamene (Mneneri) Shuaib adati kwa iwo: “Kodi simuopa (Allah)?” info
التفاسير:

external-link copy
178 : 26

إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٞ

“Ndithu ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.” info
التفاسير:

external-link copy
179 : 26

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ

“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.” info
التفاسير:

external-link copy
180 : 26

وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; kulibe malipiro anga koma kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.” info
التفاسير:

external-link copy
181 : 26

۞ أَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ وَلَا تَكُونُواْ مِنَ ٱلۡمُخۡسِرِينَ

“Kwaniritsani mulingo (pamalonda pamene mukupima), ndipo musakhale mwaopungula (mulingo).” info
التفاسير:

external-link copy
182 : 26

وَزِنُواْ بِٱلۡقِسۡطَاسِ ٱلۡمُسۡتَقِيمِ

“Ndipo yesani ndi sikelo yolungama (yolondola).” info
التفاسير:

external-link copy
183 : 26

وَلَا تَبۡخَسُواْ ٱلنَّاسَ أَشۡيَآءَهُمۡ وَلَا تَعۡثَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِينَ

“Ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo, ndiponso musayende padziko uku mukuononga.” info
التفاسير: