Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима

Бет рақами:close

external-link copy
94 : 16

وَلَا تَتَّخِذُوٓاْ أَيۡمَٰنَكُمۡ دَخَلَۢا بَيۡنَكُمۡ فَتَزِلَّ قَدَمُۢ بَعۡدَ ثُبُوتِهَا وَتَذُوقُواْ ٱلسُّوٓءَ بِمَا صَدَدتُّمۡ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَلَكُمۡ عَذَابٌ عَظِيمٞ

Ndipo musakuchite kulumbira kwanu kukhala njira yonyengelerana pakati panu, kuopera kuti mwendo ungatelere (pa njira yolungama nkukagwera ku Moto) pambuyo pokhazikika mwendowo (pa njirapo) ndi kukazilawa zoipa chifukwa chakutsekereza kwanu (anthu) ku njira ya Allah, ndipo nkupeza chilango chachikulu (tsiku lachimaliziro). info
التفاسير:

external-link copy
95 : 16

وَلَا تَشۡتَرُواْ بِعَهۡدِ ٱللَّهِ ثَمَنٗا قَلِيلًاۚ إِنَّمَا عِندَ ٱللَّهِ هُوَ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

Ndipo musagulitse mapangano a Allah ndi mtengo wochepa (wa zomwe mukupeza pano pa dziko lapansi). Chimene chili kwa Allah, ndicho chabwino kwa inu ngati mukudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
96 : 16

مَا عِندَكُمۡ يَنفَدُ وَمَا عِندَ ٱللَّهِ بَاقٖۗ وَلَنَجۡزِيَنَّ ٱلَّذِينَ صَبَرُوٓاْ أَجۡرَهُم بِأَحۡسَنِ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Zomwe mulinazo nzakutha ndipo zili kwa Allah ndizo zosatha. Ndithudi Ife tidzawapatsa malipiro (aakulu zedi) amene adapirira oposera zabwino zimene ankachita. info
التفاسير:

external-link copy
97 : 16

مَنۡ عَمِلَ صَٰلِحٗا مِّن ذَكَرٍ أَوۡ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَلَنُحۡيِيَنَّهُۥ حَيَوٰةٗ طَيِّبَةٗۖ وَلَنَجۡزِيَنَّهُمۡ أَجۡرَهُم بِأَحۡسَنِ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Amene akuchita zabwino, wamwamuna kapena wamkazi uku ali wokhulupirira timkhazika ndi moyo wabwino (pano pa dziko, ndi tsiku la Qiyâma) tidzawalipira malipiro awo mochuluka kwambiri chifukwa cha zabwino zomwe ankachita. info
التفاسير:

external-link copy
98 : 16

فَإِذَا قَرَأۡتَ ٱلۡقُرۡءَانَ فَٱسۡتَعِذۡ بِٱللَّهِ مِنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ ٱلرَّجِيمِ

Ndipo ukafuna kuwerenga Qur’an dzitchinjirize ndi Allah kwa satana wopirikitsidwa (ponena kuti Awudhu Billahi mina Shaitwani Rajim). info
التفاسير:

external-link copy
99 : 16

إِنَّهُۥ لَيۡسَ لَهُۥ سُلۡطَٰنٌ عَلَى ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ

Ndithu iye (satana) alibe mphamvu pa amene akhulupirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo. info
التفاسير:

external-link copy
100 : 16

إِنَّمَا سُلۡطَٰنُهُۥ عَلَى ٱلَّذِينَ يَتَوَلَّوۡنَهُۥ وَٱلَّذِينَ هُم بِهِۦ مُشۡرِكُونَ

Ndithudi mphamvu zake zili pa amene akumusankha (amulola) kukhala bwenzi lawo (mlangizi wawo) ndiponso ndi omwe akumphatikiza iye (ndi Allah). info
التفاسير:

external-link copy
101 : 16

وَإِذَا بَدَّلۡنَآ ءَايَةٗ مَّكَانَ ءَايَةٖ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا يُنَزِّلُ قَالُوٓاْ إِنَّمَآ أَنتَ مُفۡتَرِۭۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

Ndipo tikasintha Ayah (ndime) ndikubwera ndi Ina pamalopo, pomwe Allah akudziwa zimene akuvumbulutsa, akunena: “Ndithu iwe ndiwe wopeka.” Koma ambiri a iwo sadziwa (chilichonse). info
التفاسير:

external-link copy
102 : 16

قُلۡ نَزَّلَهُۥ رُوحُ ٱلۡقُدُسِ مِن رَّبِّكَ بِٱلۡحَقِّ لِيُثَبِّتَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَهُدٗى وَبُشۡرَىٰ لِلۡمُسۡلِمِينَ

Nena: “Mzimu woyera (Gabriel) waitsitsa (Qur’an) kuchokera kwa Mbuye wako mwachoonadi kuti awalimbikitse nayo amene akhulupirira ndi kuti ikhale chiongoko ndi nkhani yabwino kwa amene alowa m’Chisilamu (amene agonjera Allah). info
التفاسير: