قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا

external-link copy
131 : 7

فَإِذَا جَآءَتۡهُمُ ٱلۡحَسَنَةُ قَالُواْ لَنَا هَٰذِهِۦۖ وَإِن تُصِبۡهُمۡ سَيِّئَةٞ يَطَّيَّرُواْ بِمُوسَىٰ وَمَن مَّعَهُۥٓۗ أَلَآ إِنَّمَا طَٰٓئِرُهُمۡ عِندَ ٱللَّهِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

(Adali chonchi): Ubwino ukawadzera, amati: “Ubwinowu nchifukwa cha zochita zathu zabwino.” Ndipo choipa chikawadzera, amakankhira kwa Mûsa ndi amene adali naye. (Amati iye ndiye wadzetsa tsokalo chifukwa choisambula milungu yawo). Dziwani kuti tsoka lawo limachokera kwa Allah (chifukwa cha zochita zawo zoipa). Koma ambiri a iwo sazindikira. info
التفاسير: