قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا

صفحہ نمبر:close

external-link copy
150 : 7

وَلَمَّا رَجَعَ مُوسَىٰٓ إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ غَضۡبَٰنَ أَسِفٗا قَالَ بِئۡسَمَا خَلَفۡتُمُونِي مِنۢ بَعۡدِيٓۖ أَعَجِلۡتُمۡ أَمۡرَ رَبِّكُمۡۖ وَأَلۡقَى ٱلۡأَلۡوَاحَ وَأَخَذَ بِرَأۡسِ أَخِيهِ يَجُرُّهُۥٓ إِلَيۡهِۚ قَالَ ٱبۡنَ أُمَّ إِنَّ ٱلۡقَوۡمَ ٱسۡتَضۡعَفُونِي وَكَادُواْ يَقۡتُلُونَنِي فَلَا تُشۡمِتۡ بِيَ ٱلۡأَعۡدَآءَ وَلَا تَجۡعَلۡنِي مَعَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo pamene Mûsa adabwerera kwa anthu ake ali wokwiya, wodandaula (pomva zomwe zidachitikazo), adati: “Umlowam’malo wanu womwe mudandichitira pambuyo panga, ngoipa zedi. Kodi mudalifulumilira lamulo la Mbuye wanu; (mudachita zanuzanu musanadziwe chimene angakulamulireni Mulungu wanu)? Ndipo adawaponya pansi mapalewo (momwe mudalembedwa malamulo a chipembedzo chake). Nagwira mutu wa M’bale wake nkuukokera kwa iye. (kufuna kummenya chifukwa cha mkwiyo umene adali nawo. M’bale wakeyo) adati: “E iwe mwana wa mayi anga! Ndithu anthu (awa) adandiyesa wofooka, potero (sadamvere malangizo anga). Adatsala pang’ono kundipha. Choncho usawakondweretse adani (ndi chilango chako) pa ine, ndipo usandiike pamodzi ndi anthu oipa.” info
التفاسير:

external-link copy
151 : 7

قَالَ رَبِّ ٱغۡفِرۡ لِي وَلِأَخِي وَأَدۡخِلۡنَا فِي رَحۡمَتِكَۖ وَأَنتَ أَرۡحَمُ ٱلرَّٰحِمِينَ

(Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ndikhululukireni ine ndi m’bale wanga ndipo tilowetseni m’chifundo Chanu. Inu Ndinu Achifundo kuposa achifundo onse.” info
التفاسير:

external-link copy
152 : 7

إِنَّ ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ ٱلۡعِجۡلَ سَيَنَالُهُمۡ غَضَبٞ مِّن رَّبِّهِمۡ وَذِلَّةٞ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُفۡتَرِينَ

Ndithu omwe adapanga (fano la ) Thole uwafika mkwiyo wa Mbuye wawo ndi kunyozeka pa moyo wa dziko lapansi. M’menemo ndi momwe timawalipirira anthu opeka (zinthu za chipembedzo). info
التفاسير:

external-link copy
153 : 7

وَٱلَّذِينَ عَمِلُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ ثُمَّ تَابُواْ مِنۢ بَعۡدِهَا وَءَامَنُوٓاْ إِنَّ رَبَّكَ مِنۢ بَعۡدِهَا لَغَفُورٞ رَّحِيمٞ

Ndipo omwe adachita zoipa, kenako nkulapa pambuyo pake nakhulupirira ndithu Mbuye wako pambuyo pakulapako, Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni. info
التفاسير:

external-link copy
154 : 7

وَلَمَّا سَكَتَ عَن مُّوسَى ٱلۡغَضَبُ أَخَذَ ٱلۡأَلۡوَاحَۖ وَفِي نُسۡخَتِهَا هُدٗى وَرَحۡمَةٞ لِّلَّذِينَ هُمۡ لِرَبِّهِمۡ يَرۡهَبُونَ

Pamene mkwiyo wa Mûsa udatotobwa, adatola mapale aja omwe m’malembo mwake mudali chiongoko ndi chifundo kwa omwe amaopa Mbuye wawo. info
التفاسير:

external-link copy
155 : 7

وَٱخۡتَارَ مُوسَىٰ قَوۡمَهُۥ سَبۡعِينَ رَجُلٗا لِّمِيقَٰتِنَاۖ فَلَمَّآ أَخَذَتۡهُمُ ٱلرَّجۡفَةُ قَالَ رَبِّ لَوۡ شِئۡتَ أَهۡلَكۡتَهُم مِّن قَبۡلُ وَإِيَّٰيَۖ أَتُهۡلِكُنَا بِمَا فَعَلَ ٱلسُّفَهَآءُ مِنَّآۖ إِنۡ هِيَ إِلَّا فِتۡنَتُكَ تُضِلُّ بِهَا مَن تَشَآءُ وَتَهۡدِي مَن تَشَآءُۖ أَنتَ وَلِيُّنَا فَٱغۡفِرۡ لَنَا وَٱرۡحَمۡنَاۖ وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلۡغَٰفِرِينَ

Ndipo Mûsa adasankha anthu ake makumi asanu ndi awiri (70 omwe adali amakhalidwe abwino) kuti akafike kumalo a chipangano chathu (chimene tidamuuza kuti akabwere nawo pa phiripo kuti akapemphe chikhululuko pa machimo awo omwe adachitidwa ndi anzawo oipa). Ndipo pamene chivomerezi chachikulu chidawafika (adatsala pang’ono kufa). (Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ngati mukadafuna mukadawaononga iwo ndi ine kale (pamaso pa anzawo onse kuti adzionere okha kuti amwalira ndi mphamvu za Allah, osati pakuwapha ine). Kodi mutiononga chifukwa cha zochita za mbuli zathu? Izi sichina koma ndi mayesero anu. Kupyolera m’mayeserowo mumamlekelera kusokera amene mwamfuna, ndi kumtsogolera amene mwamfuna. Inu ndiye Mtetezi wathu; choncho, tikhululukireni ndi kutimvera chifundo. Inu ndinu Abwino mwa okhululuka onse.” info
التفاسير: