قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا

صفحہ نمبر:close

external-link copy
4 : 57

هُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ يَعۡلَمُ مَا يَلِجُ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا يَخۡرُجُ مِنۡهَا وَمَا يَنزِلُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ وَمَا يَعۡرُجُ فِيهَاۖ وَهُوَ مَعَكُمۡ أَيۡنَ مَا كُنتُمۡۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ

Iye ndi Amene adalenga kumwamba ndi pansi (ndi zonse zammenemo) m’masiku asanu ndi limodzi kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu monga momwe Iye adziwira polongosola ufumu Wake). Akudziwa chilichonse cholowa m’nthaka ndi chimene chikutuluka m’menemo; ndi chilichonse chimene chikutsika kuchokera kumwamba ndi chimene chikukwera kumeneko. Ndipo Iye ali nanu paliponse pamene muli. Ndithu Allah amaona chilichonse chimene mukuchita, (sichibisika chilichonse kwa Iye). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 57

لَّهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ

Ufumu wakumwamba ndi pansi Ngwake ndipo kwa Allah nkobwerera zinthu (zonse). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 57

يُولِجُ ٱلَّيۡلَ فِي ٱلنَّهَارِ وَيُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِي ٱلَّيۡلِۚ وَهُوَ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ

Usiku amawulowetsa mu usana, ndipo usana amawulowetsa mu usiku. (Choncho kumasiyana kutalika kwake); ndipo Iye Ngodziwa zobisika za m’zifuwa (ndi zoganiza za m’mitima). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 57

ءَامِنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَأَنفِقُواْ مِمَّا جَعَلَكُم مُّسۡتَخۡلَفِينَ فِيهِۖ فَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنكُمۡ وَأَنفَقُواْ لَهُمۡ أَجۡرٞ كَبِيرٞ

Khulupirirani Allah ndi Mthenga Wake, ndipo perekani (pa njira ya Allah m’chuma chimene Allah wakupatsani uchiyang’anira. Choncho mwa inu amene akhulupirira (mwa Allah ndi mthenga Wake) ndikupereka (zimene awapatsa) iwo ali ndi malipiro aakulu (kwa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 57

وَمَا لَكُمۡ لَا تُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلرَّسُولُ يَدۡعُوكُمۡ لِتُؤۡمِنُواْ بِرَبِّكُمۡ وَقَدۡ أَخَذَ مِيثَٰقَكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ

Kodi nchifukwa ninji simukhulupirira Allah pomwe Mtumiki akukuitanani kuti mukhulupirire Mbuye wanu (ndi kukulimbitsani pa zimenezo) chikhalirecho (Iye) adalandira lonjezo lanu, (muli mumsana wa tate wanu Adam kuti mdzakhulupirira,) ngati mulidi okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 57

هُوَ ٱلَّذِي يُنَزِّلُ عَلَىٰ عَبۡدِهِۦٓ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٖ لِّيُخۡرِجَكُم مِّنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ بِكُمۡ لَرَءُوفٞ رَّحِيمٞ

Iye ndi Amene akuvumbulutsa kwa kapolo Wake Ayah (ndime) zofotokoza mwatsatanetsatane kuti akutulutseni mum’dima (wa kusokera) ndi kukuikani ku chiongoko cha kuunika. Ndipo ndithu Allah Ngoleza kwa inu, Ngwachisoni. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 57

وَمَا لَكُمۡ أَلَّا تُنفِقُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ وَلِلَّهِ مِيرَٰثُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ لَا يَسۡتَوِي مِنكُم مَّنۡ أَنفَقَ مِن قَبۡلِ ٱلۡفَتۡحِ وَقَٰتَلَۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَعۡظَمُ دَرَجَةٗ مِّنَ ٱلَّذِينَ أَنفَقُواْ مِنۢ بَعۡدُ وَقَٰتَلُواْۚ وَكُلّٗا وَعَدَ ٱللَّهُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٞ

Kodi ndichifukwa chiani simukupereka pa njira ya Allah (chuma chanu) pamene Allah Ndimwini wa zosiyidwa zonse za kumwamba ndi za m’dziko lapansi. Sali ofanana mwa inu amene adapereka chuma (panjira ya Allah) pamodzi ndi kumenya nkhondo usadagonjetsedwe (mzinda wa Makka), iwowo ndiomwe ali ndi ulemelero waukulu kuposa amene apereka chuma chawo ndi kumenya nkhondo pambuyo. Koma onsewo Allah wawalonjeza zabwino (ngakhale ali osiyana ulemelero wawo); ndipo Allah akudziwa zonse zimene muchita. (Choncho aliyense adzalipidwa molingana ndi zimene amachita). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 57

مَّن ذَا ٱلَّذِي يُقۡرِضُ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنٗا فَيُضَٰعِفَهُۥ لَهُۥ وَلَهُۥٓ أَجۡرٞ كَرِيمٞ

Kodi ndani (okhulupirira) amene angamkongoze Allah ngongole yabwino kuti amuchulukitsire malipiro ake? Ndipo iye adzalandira malipiro aulemu (pa tsiku la chiweruziro). info
التفاسير: