قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا

صفحہ نمبر:close

external-link copy
10 : 5

وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَآ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَحِيمِ

Ndipo amene sadakhulupirire, natsutsa zizindikiro Zathu, iwo ndi anthu a ku Moto. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ إِذۡ هَمَّ قَوۡمٌ أَن يَبۡسُطُوٓاْ إِلَيۡكُمۡ أَيۡدِيَهُمۡ فَكَفَّ أَيۡدِيَهُمۡ عَنكُمۡۖ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَۚ وَعَلَى ٱللَّهِ فَلۡيَتَوَكَّلِ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ

E inu amene mwakhulupirira! Kumbukirani mtendere wa Allah omwe uli pa inu, pamene anthu ena adatsimikiza kukutambasulirani manja awo (pofuna kuchita nanu nkhondo) koma (Allah) adawatsekereza manja awo kukufikani inu. Choncho opani Allah. Ndipo kwa Allah Yekha, ayadzamire okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 5

۞ وَلَقَدۡ أَخَذَ ٱللَّهُ مِيثَٰقَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَبَعَثۡنَا مِنۡهُمُ ٱثۡنَيۡ عَشَرَ نَقِيبٗاۖ وَقَالَ ٱللَّهُ إِنِّي مَعَكُمۡۖ لَئِنۡ أَقَمۡتُمُ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتَيۡتُمُ ٱلزَّكَوٰةَ وَءَامَنتُم بِرُسُلِي وَعَزَّرۡتُمُوهُمۡ وَأَقۡرَضۡتُمُ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنٗا لَّأُكَفِّرَنَّ عَنكُمۡ سَيِّـَٔاتِكُمۡ وَلَأُدۡخِلَنَّكُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۚ فَمَن كَفَرَ بَعۡدَ ذَٰلِكَ مِنكُمۡ فَقَدۡ ضَلَّ سَوَآءَ ٱلسَّبِيلِ

Ndipo ndithudi, Allah adamanga pangano ndi ana a Israyeli, ndipo tidawaikira Akuluakulu khumi ndi awiri mwa iwo. Ndipo Allah adati: “Ndithudi Ine ndili pamodzi ndi inu, ngati mupemphera Swala ndikupereka chopereka, ndikukhulupirira atumiki Anga, ndi kuwalemekeza ndi kumkongoza Allah Ngongole yabwino, ndithudi ndikufafanizirani zoipa zanu, ndikudzakulowetsani m’Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje. Koma amene akane mwa inu pambuyo pa (chipangano) ichi, ndithu wasochera njira yowongoka.” info
التفاسير:

external-link copy
13 : 5

فَبِمَا نَقۡضِهِم مِّيثَٰقَهُمۡ لَعَنَّٰهُمۡ وَجَعَلۡنَا قُلُوبَهُمۡ قَٰسِيَةٗۖ يُحَرِّفُونَ ٱلۡكَلِمَ عَن مَّوَاضِعِهِۦ وَنَسُواْ حَظّٗا مِّمَّا ذُكِّرُواْ بِهِۦۚ وَلَا تَزَالُ تَطَّلِعُ عَلَىٰ خَآئِنَةٖ مِّنۡهُمۡ إِلَّا قَلِيلٗا مِّنۡهُمۡۖ فَٱعۡفُ عَنۡهُمۡ وَٱصۡفَحۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Choncho chifukwa chakuswa pangano lawo, tidawatembelera; ndipo tidaumitsa mitima yawo. Ankasintha mawu (a Allah omwe adali m’mabuku a Taurat ndi Injili) kuwachotsa m’malo mwake ndipo adasiya kukwaniritsa gawo lalikulu la zomwe adakumbutsidwa. Ndipo ukhala ukuona (iwe Mtumiki {s.a.w}) chinyengo mwa ambiri a iwo, kupatula ochepa a iwo. Choncho akhululukire ndi kuwaleka. Ndithudi, Allah amakonda ochita zabwino.[159] info

[159] Ndime iyi ikupitirizanso kutchula zina mwa zoipa za Ayuda. Ndipo zina mwa izozi ndiko kusintha mawu a m’buku lawo lomwe Allah adawavumbulutsira. Iwo ankachotsamo mawu omwe sadali kuwafuna naikamo amene ankawafuna. Zoterezi Akhrisitu anazichitanso. Ndipo akuchitabe mpaka lero. Mabaibulo awo omwe akusindikiza nkuwagawa m’maiko athu kuno ku Africa ndi kwina kulikonse ngati utaona mofatsa omwe asindikiza posachedwapa upeza kusiyana pang’ono ndi omwe adasindikiza m’mbuyomu. (a) Mwina akuchotsa zimene zidalimo (b) Kapena akuikamo zomwe mudalibe (c) Mwina matanthauzo achiganizo amawasinthiratu kusiyana ndi momwe zidalili m’buku lomwe adasindikiza kale. Zonsezi zikusonyeza kuti amenewa ndiwo machitidwe awo pofuna kukopa anthu ambiri kuchipembedzo chawo. Akaona kuti ichi chikopa anthu ambiri, amachiikamo nanena kuti ndi mawu a Mulungu. Ndipo akaona kuti malamulo awa apirikitsa anthu amawachotsa kapena kuwachepetsa mphamvu yake. Umo ndimomwe alili machitidwe awo.

التفاسير: