قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا

external-link copy
90 : 4

إِلَّا ٱلَّذِينَ يَصِلُونَ إِلَىٰ قَوۡمِۭ بَيۡنَكُمۡ وَبَيۡنَهُم مِّيثَٰقٌ أَوۡ جَآءُوكُمۡ حَصِرَتۡ صُدُورُهُمۡ أَن يُقَٰتِلُوكُمۡ أَوۡ يُقَٰتِلُواْ قَوۡمَهُمۡۚ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَسَلَّطَهُمۡ عَلَيۡكُمۡ فَلَقَٰتَلُوكُمۡۚ فَإِنِ ٱعۡتَزَلُوكُمۡ فَلَمۡ يُقَٰتِلُوكُمۡ وَأَلۡقَوۡاْ إِلَيۡكُمُ ٱلسَّلَمَ فَمَا جَعَلَ ٱللَّهُ لَكُمۡ عَلَيۡهِمۡ سَبِيلٗا

Kupatula omwe akugwirizana ndi anthu amene pali pangano pakati panu ndi iwo, kapena omwe akudza kwa inu uku zifuwa zawo zili zobanika kumenyana nanu, kapena kumenyana ndi anthu awo. (Oterewo musamenyane nawo). Ngati Allah akadafuna, akadawapatsa mphamvu yokugonjetserani, choncho akadakumenyani. Ngati atakupewani, osamenyana nanu ndipo nkukupatsani mtendere, ndiye kuti Allah sadakupangireni njira pa iwo (yakuti mumenyane nawo). info
التفاسير: