قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا

صفحہ نمبر:close

external-link copy
75 : 23

۞ وَلَوۡ رَحِمۡنَٰهُمۡ وَكَشَفۡنَا مَا بِهِم مِّن ضُرّٖ لَّلَجُّواْ فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ

Ndipo tikadawachitira chifundo ndi kuwachotsera masautso omwe ali nawo, ndithu akadapitiriza kuyumbayumba m’kuchita kwawo zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
76 : 23

وَلَقَدۡ أَخَذۡنَٰهُم بِٱلۡعَذَابِ فَمَا ٱسۡتَكَانُواْ لِرَبِّهِمۡ وَمَا يَتَضَرَّعُونَ

Ndipo ndithu tidawalanga ndi chilango (chaukali), koma sadacheukire kwa Mbuye wawo ndikudzichepetsa. info
التفاسير:

external-link copy
77 : 23

حَتَّىٰٓ إِذَا فَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَابٗا ذَا عَذَابٖ شَدِيدٍ إِذَا هُمۡ فِيهِ مُبۡلِسُونَ

Kufikira pamene tidawatsekulira khomo la chilango chaukali; pamenepo ndipo adataya mtima. info
التفاسير:

external-link copy
78 : 23

وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنشَأَ لَكُمُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَٱلۡأَفۡـِٔدَةَۚ قَلِيلٗا مَّا تَشۡكُرُونَ

Ndipo Iye ndi Yemwe adakupangirani makutu, maso ndi mitima; nzochepa zimene mukuthokoza. info
التفاسير:

external-link copy
79 : 23

وَهُوَ ٱلَّذِي ذَرَأَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَإِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ

Iyenso ndi Yemwe wakufalitsani pa dziko; kenako mudzasonkhanitsidwa kwa Iye. info
التفاسير:

external-link copy
80 : 23

وَهُوَ ٱلَّذِي يُحۡيِۦ وَيُمِيتُ وَلَهُ ٱخۡتِلَٰفُ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ

Ndipo Iye ndi Yemwe amapatsa moyo ndi imfa, ndipo kusinthana kwa usiku ndi usana Nkwake. Kodi simuzindikira? info
التفاسير:

external-link copy
81 : 23

بَلۡ قَالُواْ مِثۡلَ مَا قَالَ ٱلۡأَوَّلُونَ

Koma akunena monga (anthu) oyamba adanenera. info
التفاسير:

external-link copy
82 : 23

قَالُوٓاْ أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ

Akunena: “Kodi tikadzafa ndikukhala dothi ndi mafupa, tidzaukitsidwanso?” info
التفاسير:

external-link copy
83 : 23

لَقَدۡ وُعِدۡنَا نَحۡنُ وَءَابَآؤُنَا هَٰذَا مِن قَبۡلُ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ

“Ndithudi ife ndi makolo athu kale tidalonjezedwa zimenezi, izi sikanthu koma nkhambakamwa za anthu akale.” info
التفاسير:

external-link copy
84 : 23

قُل لِّمَنِ ٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهَآ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

Nena: “Kodi nthaka njayani ndi zomwe zili m’menemo, ngati inu mukudziwa (kanthu)!” info
التفاسير:

external-link copy
85 : 23

سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ

Adzanena kuti: “Nza Allah!” Nena: “Nanga bwanji simukumkumbukira (kuti Iye Ngokhoza chilichonse)? info
التفاسير:

external-link copy
86 : 23

قُلۡ مَن رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ ٱلسَّبۡعِ وَرَبُّ ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡعَظِيمِ

Nena: “Kodi ndani Mbuye wa thambo zisanu ndi ziwiri, ndi Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) yaikulu?” info
التفاسير:

external-link copy
87 : 23

سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ أَفَلَا تَتَّقُونَ

Anena (kuti): “Nza Allah.” Nena: “Nanga bwanji simukumuopa?” info
التفاسير:

external-link copy
88 : 23

قُلۡ مَنۢ بِيَدِهِۦ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيۡءٖ وَهُوَ يُجِيرُ وَلَا يُجَارُ عَلَيۡهِ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

Nena: “Kodi ndani yemwe m’manja mwake muli mphamvu yolamulira chinthu chilichonse? Ndipo Iye amateteza zonse. Ndipo palibe chimene chingatetezedwe kuchilango Chake. Ngati inu mukudziwa.” info
التفاسير:

external-link copy
89 : 23

سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ فَأَنَّىٰ تُسۡحَرُونَ

Anena (kuti): “Ndi Allah.” Nena: “Nanga mukulodzedwa bwanji (ndi satana)?” info
التفاسير: