قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا

Al-Mâ’un

external-link copy
1 : 107

أَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي يُكَذِّبُ بِٱلدِّينِ

Kodi wamuona yemwe akutsutsa za mphoto (ndi chiwerengero cha tsiku lachimaliziro)?[487] info

[487] Sura imeneyi ikufotokoza m’mene alili makhalidwe a anthu ambiri, ngakhale amene amadzitcha kuti ndi Asilamu. Aliyense amene ali ndi makhalidwe otere ndiye kuti sakhulupilira za tsiku la chiweruziro. Akadakhala kuti akukhulupilira za tsikuli, sibwenzi akusiya kuwachitira za chifundo osauka ndi amasiye. Sapereka chithandizo ngakhale kulimbikitsa ena ngati iye alibe.

التفاسير:

external-link copy
2 : 107

فَذَٰلِكَ ٱلَّذِي يَدُعُّ ٱلۡيَتِيمَ

Iye ndi yemwe akukankha wamasiye (mwankhanza). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 107

وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ

Ndipo salimbikitsa (ena pamodzi ndi iye mwini) kudyetsa osauka. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 107

فَوَيۡلٞ لِّلۡمُصَلِّينَ

Choncho kuonongeka kuli pa ena mwa opemphera swala (amene ali ndi mbiri izi); info
التفاسير:

external-link copy
5 : 107

ٱلَّذِينَ هُمۡ عَن صَلَاتِهِمۡ سَاهُونَ

Omwe amachitira mphwayi mapemphero awo.[488] info

[488] Kuchitira mphwayi mapemphero (Swala), kumeneku ndiko kupemphera modukizadukiza. Tsiku lina nkupempherapo, tsiku lina ayi. Kapenanso kupemphera modzionetsera kwa anthu (riyaa).

التفاسير:

external-link copy
6 : 107

ٱلَّذِينَ هُمۡ يُرَآءُونَ

Amenenso (akamachita mapemphero awo) amadzionetsera (kwa anthu mwachipha maso kuti apeze ulemelero ndi kutamandidwa mmitima mwa anthu).[489] info

[489] Riyaa ndiko kuchita ntchito yabwino ndicholinga choonetsa anthu, kuti akuone kuti ndiwe wabwino, mwina kuti ukhale wokondedwa ndi anthu. Kapenanso kuti upeze za m’matumba mwawo. Amenewa ndi machitidwe a “Shiriki” (kum’phatikiza Allah ndi zolengedwa Zake pa mapemphero) ndiponso ndi njira yobera anthu.

التفاسير:

external-link copy
7 : 107

وَيَمۡنَعُونَ ٱلۡمَاعُونَ

Ndipo amamana ziwiya (zawo posabwereka anzawo zinthu zofunika pa moyo wa aliyense monga nkhwangwa, mpeni, mtondo ndi zina zotere). info
التفاسير: