قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

بەت نومۇرى:close

external-link copy
11 : 71

يُرۡسِلِ ٱلسَّمَآءَ عَلَيۡكُم مِّدۡرَارٗا

Akutumizirani mvula yotsika mochuluka, info
التفاسير:

external-link copy
12 : 71

وَيُمۡدِدۡكُم بِأَمۡوَٰلٖ وَبَنِينَ وَيَجۡعَل لَّكُمۡ جَنَّٰتٖ وَيَجۡعَل لَّكُمۡ أَنۡهَٰرٗا

Ndikukupatsani chuma ndi ana, (zomwe ndi zokongoletsa za dziko lapansi), ndi kukupangirani minda (yokongola) ndi kukupangirani mitsinje (yothilira mbewu zanu ndi kumwetsa ziweto zanu). info
التفاسير:

external-link copy
13 : 71

مَّا لَكُمۡ لَا تَرۡجُونَ لِلَّهِ وَقَارٗا

Kodi chifukwa ninji simupereka ulemu kwa Allah (woyenera Umulungu Wake kuti akakuchitireni chifundo ndi kukupulumutsani ku chilango)? info
التفاسير:

external-link copy
14 : 71

وَقَدۡ خَلَقَكُمۡ أَطۡوَارًا

Pomwe Iye adakulengani mnjira zosiyanasiyana; (madzi a umunthu, kenako magazi, kenako magazi ochindikala, kenako mafupa ndipo kenako mnofu), info
التفاسير:

external-link copy
15 : 71

أَلَمۡ تَرَوۡاْ كَيۡفَ خَلَقَ ٱللَّهُ سَبۡعَ سَمَٰوَٰتٖ طِبَاقٗا

Kodi simudaone momwe Allah adalengera thambo zisanu ndi ziwiri mosanjikizana? info
التفاسير:

external-link copy
16 : 71

وَجَعَلَ ٱلۡقَمَرَ فِيهِنَّ نُورٗا وَجَعَلَ ٱلشَّمۡسَ سِرَاجٗا

Ndi kuyika mwezi mthambomo kukhala kuunika, ndiponso kuyika dzuwa kukhala nyali. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 71

وَٱللَّهُ أَنۢبَتَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ نَبَاتٗا

Ndipo Allah adakulengani kuchokera m’nthaka monga mmera. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 71

ثُمَّ يُعِيدُكُمۡ فِيهَا وَيُخۡرِجُكُمۡ إِخۡرَاجٗا

Kenako adzakubwezerani momwemo ndikudzakutulutsaninso (popanda cholepheretsa). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 71

وَٱللَّهُ جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ بِسَاطٗا

Ndipo Allah wakupangirani nthaka kukhala ngati choyala, info
التفاسير:

external-link copy
20 : 71

لِّتَسۡلُكُواْ مِنۡهَا سُبُلٗا فِجَاجٗا

Kuti muziyendayenda m’menemo m’njira zazikulu.” info
التفاسير:

external-link copy
21 : 71

قَالَ نُوحٞ رَّبِّ إِنَّهُمۡ عَصَوۡنِي وَٱتَّبَعُواْ مَن لَّمۡ يَزِدۡهُ مَالُهُۥ وَوَلَدُهُۥٓ إِلَّا خَسَارٗا

Adanena Nuh: “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga andinyoza (pa zimene ndawalamula kuti akhulupirire Inu ndi kupempha chikhululuko chanu), ndipo (ofooka mwa iwo) amtsatira yemwe chuma chake ndi ana ake sizidzamuonjezera (chilichonse chabwino) koma kutaika (ndi kuonongeka pa tsiku lachimaliziro). info
التفاسير:

external-link copy
22 : 71

وَمَكَرُواْ مَكۡرٗا كُبَّارٗا

Ndipo (eni chuma ndi ana) awatchera (otsatira awo) ndale zazikulu (ndi zopyola muyeso kuti asakhulupirire).” info
التفاسير:

external-link copy
23 : 71

وَقَالُواْ لَا تَذَرُنَّ ءَالِهَتَكُمۡ وَلَا تَذَرُنَّ وَدّٗا وَلَا سُوَاعٗا وَلَا يَغُوثَ وَيَعُوقَ وَنَسۡرٗا

Ndipo adanena (kwa owatsatira awo): “Musasiye kupembedza milungu yanu; musamusiye Wadda, Suwaa’, Yaghutha, Ya’uqa ndi Nasra” (maina a mafano awo). info
التفاسير:

external-link copy
24 : 71

وَقَدۡ أَضَلُّواْ كَثِيرٗاۖ وَلَا تَزِدِ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا ضَلَٰلٗا

Ndipo ndithu iwo asokeretsa (anthu) ambiri; ndipo musawaonjezere ochita zoipa (china chake) koma kusokera basi.” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 71

مِّمَّا خَطِيٓـَٰٔتِهِمۡ أُغۡرِقُواْ فَأُدۡخِلُواْ نَارٗا فَلَمۡ يَجِدُواْ لَهُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ أَنصَارٗا

Chifukwa cha zochimwa zawo adamizidwa ndi kulowetsedwa ku Moto (waukulu woyaka); sadapeze owapulumutsa ndi kuwateteza m’malo mwa Allah. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 71

وَقَالَ نُوحٞ رَّبِّ لَا تَذَرۡ عَلَى ٱلۡأَرۡضِ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ دَيَّارًا

Ndipo adanena Nuh (atataya mtima za anthu ake): “Mbuye wanga! Musasiye aliyense mwa osakhulupirira kukhala pa dziko.” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 71

إِنَّكَ إِن تَذَرۡهُمۡ يُضِلُّواْ عِبَادَكَ وَلَا يَلِدُوٓاْ إِلَّا فَاجِرٗا كَفَّارٗا

“Ndithu Inu Mbuye wanga ngati muwasiya (popanda kuwaononga ndi kuwathetsa) asokeretsa akapolo anu (kunjira yolungama). Ndipo sangabereke (ana abwino) koma oipa; osakhulupirira (okhala kutali ndi choonadi, ndiponso onyoza Inu).” info
التفاسير:

external-link copy
28 : 71

رَّبِّ ٱغۡفِرۡ لِي وَلِوَٰلِدَيَّ وَلِمَن دَخَلَ بَيۡتِيَ مُؤۡمِنٗا وَلِلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِۖ وَلَا تَزِدِ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا تَبَارَۢا

“Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndi makolo anga, ndi aliyense walowa m’nyumba yanga ali okhulupirira ndi okhulupirira amuna ndi okhulupirira akazi. Ndipo musawaonjezere anthu achinyengo chinachake koma kuwaononga basi.” info
التفاسير: