قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

Adh-Dhâriyât

external-link copy
1 : 51

وَٱلذَّٰرِيَٰتِ ذَرۡوٗا

. Ndikulumbilira mphepo imene ikubalalitsa mitambo ya mvula. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 51

فَٱلۡحَٰمِلَٰتِ وِقۡرٗا

Ndi imene imasenza mitolo yolemera (ya madzi). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 51

فَٱلۡجَٰرِيَٰتِ يُسۡرٗا

Ndi kuyenda (nawo madziwo) mwaubwino. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 51

فَٱلۡمُقَسِّمَٰتِ أَمۡرًا

Ndi awo amene amagawa rizq (limene Allah amalipereka kwa amene wamfuna). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 51

إِنَّمَا تُوعَدُونَ لَصَادِقٞ

Ndithu zimene mukulonjezedwa nzoonadi, (zidzachitika). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 51

وَإِنَّ ٱلدِّينَ لَوَٰقِعٞ

Ndipo, ndithu malipiro (pa zochita zanu) adzapezekadi. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 51

وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلۡحُبُكِ

Ndikulumbilira thambo lomwe njira zake zambiri nzoikidwa mwaluso. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 51

إِنَّكُمۡ لَفِي قَوۡلٖ مُّخۡتَلِفٖ

Ndithu inu muli m’mau otsutsana, (pa zimene mukunena). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 51

يُؤۡفَكُ عَنۡهُ مَنۡ أُفِكَ

(Kupyolera m’mawu amenewa) akuchotsedwa ku icho (chikhulupiliro chalonjezo loona) amene adachotsedwa (ku chikhulupilirocho). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 51

قُتِلَ ٱلۡخَرَّٰصُونَ

Aonongeka abodza (amene akunena za tsiku lachiweruziro mongoganizira.) info
التفاسير:

external-link copy
11 : 51

ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي غَمۡرَةٖ سَاهُونَ

Iwo amene akubira mu umbuli, osalabadira (za tsiku lachimaliziro). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 51

يَسۡـَٔلُونَ أَيَّانَ يَوۡمُ ٱلدِّينِ

Akufunsa (mwachipongwe ponena kuti) “Lidzakhala liti tsiku lamalipiro?” info
التفاسير:

external-link copy
13 : 51

يَوۡمَ هُمۡ عَلَى ٱلنَّارِ يُفۡتَنُونَ

(Limenelo ndi) tsiku lomwe iwo adzalangidwa ku Moto. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 51

ذُوقُواْ فِتۡنَتَكُمۡ هَٰذَا ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تَسۡتَعۡجِلُونَ

(Adzawauza kuti): “Lawani chilango chanu ichi chimene munkachifulumizitsa (kuti chikufikeni).” info
التفاسير:

external-link copy
15 : 51

إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٖ وَعُيُونٍ

Ndithu oopa (Allah) adzakhala (akusangalala) m’minda ndi mu akasupe okongola, info
التفاسير:

external-link copy
16 : 51

ءَاخِذِينَ مَآ ءَاتَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَبۡلَ ذَٰلِكَ مُحۡسِنِينَ

Uku akulandira zimene wawapatsa Mbuye wawo (malipiro aulemu); ndithu iwo ankachita zabwino asanapeze izi. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 51

كَانُواْ قَلِيلٗا مِّنَ ٱلَّيۡلِ مَا يَهۡجَعُونَ

Nthawi yausiku amagona pang’ono. (Amadzuka nachita mapemphero mochulukitsa). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 51

وَبِٱلۡأَسۡحَارِ هُمۡ يَسۡتَغۡفِرُونَ

Ndipo kum’bandakucha, iwo amapempha chikhululuko, info
التفاسير:

external-link copy
19 : 51

وَفِيٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ حَقّٞ لِّلسَّآئِلِ وَٱلۡمَحۡرُومِ

Ndipo m’chuma chawo mudali gawo (lodziwika) la opempha ndi osapempha (mwa osauka). info
التفاسير:

external-link copy
20 : 51

وَفِي ٱلۡأَرۡضِ ءَايَٰتٞ لِّلۡمُوقِنِينَ

M’nthaka muli zizindikiro kwa otsimikiza, (zosonyeza kuti Allah alipo). info
التفاسير:

external-link copy
21 : 51

وَفِيٓ أَنفُسِكُمۡۚ أَفَلَا تُبۡصِرُونَ

Ndi mwa inu nomwe; kodi simuona? info
التفاسير:

external-link copy
22 : 51

وَفِي ٱلسَّمَآءِ رِزۡقُكُمۡ وَمَا تُوعَدُونَ

Ndipo kumwamba kuli zokuthandizani (pa moyo wanu), ndi zimene mukulonjezedwa. info
التفاسير:

external-link copy
23 : 51

فَوَرَبِّ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ إِنَّهُۥ لَحَقّٞ مِّثۡلَ مَآ أَنَّكُمۡ تَنطِقُونَ

Ndikulumbilira Mbuye wa kumwamba ndi pansi, ndithu zimenezo ndi zoona monga kulili kuyankhula kwanu. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 51

هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ضَيۡفِ إِبۡرَٰهِيمَ ٱلۡمُكۡرَمِينَ

Kodi yakufika nkhani ya alendo a Ibrahim; (angelo) olemekezeka? info
التفاسير:

external-link copy
25 : 51

إِذۡ دَخَلُواْ عَلَيۡهِ فَقَالُواْ سَلَٰمٗاۖ قَالَ سَلَٰمٞ قَوۡمٞ مُّنكَرُونَ

Pamene adalowa kwa iye ndi kunena kuti: “Salaam,” (“Mtendere”)! Iye adayankha: “Salaam,” (“Mtendere) inu ndinu anthu osadziwika (achilendo).” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 51

فَرَاغَ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ فَجَآءَ بِعِجۡلٖ سَمِينٖ

Adatembenukira kwa akunyumba ake (mwakachetechete), ndipo adadza ndi nyama ya mwana wa ng’ombe yonona (yowotcha). info
التفاسير:

external-link copy
27 : 51

فَقَرَّبَهُۥٓ إِلَيۡهِمۡ قَالَ أَلَا تَأۡكُلُونَ

Naipereka kwa iwo (koma sadadye); iye adanena (modabwa): “Kodi bwanji simukudya?” info
التفاسير:

external-link copy
28 : 51

فَأَوۡجَسَ مِنۡهُمۡ خِيفَةٗۖ قَالُواْ لَا تَخَفۡۖ وَبَشَّرُوهُ بِغُلَٰمٍ عَلِيمٖ

Mumtima mwake adadzazidwa mantha ndi iwo. Iwo adati: “Usaope,” ndipo adamuuza nkhani yabwino ya kubala mwana wodziwa. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 51

فَأَقۡبَلَتِ ٱمۡرَأَتُهُۥ فِي صَرَّةٖ فَصَكَّتۡ وَجۡهَهَا وَقَالَتۡ عَجُوزٌ عَقِيمٞ

Adadza mkazi wake ndi mkuwe (pamene adamva nkhani yabwino ija). Adadzimenya kunkhope (ndi dzanja lake kusonyeza kudabwa ndi kusatheka). Ndipo adati: (“Ine ndine) nkhalamba (ndiponso) chumba; (ndingabereke bwanji)?” info
التفاسير:

external-link copy
30 : 51

قَالُواْ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡعَلِيمُ

Iwo adati: “Momwemo, Mbuye wako wanena. Iye Ngwanzeru zakuya (pa chilichonse chimene akulamula); Ngodziwa; (palibe chimene chingabisike kwa Iye). info
التفاسير:

external-link copy
31 : 51

۞ قَالَ فَمَا خَطۡبُكُمۡ أَيُّهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ

۞ (Ibrahim) adati: “Kodi nkhani yanu ndiyotani E inu otumidwa?” info
التفاسير:

external-link copy
32 : 51

قَالُوٓاْ إِنَّآ أُرۡسِلۡنَآ إِلَىٰ قَوۡمٖ مُّجۡرِمِينَ

Iwo adati: “Tatumizidwa kwa anthu oipa.” info
التفاسير:

external-link copy
33 : 51

لِنُرۡسِلَ عَلَيۡهِمۡ حِجَارَةٗ مِّن طِينٖ

“Kuti tiwagende ndi miyala yotenthedwa kuchokera kudongo.” info
التفاسير:

external-link copy
34 : 51

مُّسَوَّمَةً عِندَ رَبِّكَ لِلۡمُسۡرِفِينَ

“Yoikidwa chizindikiro cha aliyense wochimwa kuchokera kwa Mbuye wako.” info
التفاسير:

external-link copy
35 : 51

فَأَخۡرَجۡنَا مَن كَانَ فِيهَا مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Tidawatulutsa okhulupirira omwe adali m’mudzimo. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 51

فَمَا وَجَدۡنَا فِيهَا غَيۡرَ بَيۡتٖ مِّنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ

Sitidapeze mmenemo (okhulupirira ambiri) kupatula mnyumba imodzi ya Asilamu. info
التفاسير:

external-link copy
37 : 51

وَتَرَكۡنَا فِيهَآ ءَايَةٗ لِّلَّذِينَ يَخَافُونَ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ

Ndipo tidasiya pamenepo chizindikiro (chosonyeza kuonongeka kwa eni mudziwo kuti chikhale lingaliro) kwa amene akuopa chilango chopweteka. info
التفاسير:

external-link copy
38 : 51

وَفِي مُوسَىٰٓ إِذۡ أَرۡسَلۡنَٰهُ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ بِسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٖ

M’nkhani ya Mûsa (muli phunziro) pamene tidamtuma kwa Farawo uku atalimbikitsidwa ndi chisonyezo choonekera. info
التفاسير:

external-link copy
39 : 51

فَتَوَلَّىٰ بِرُكۡنِهِۦ وَقَالَ سَٰحِرٌ أَوۡ مَجۡنُونٞ

Koma Farawo adanyoza (kukhulupirira Mûsa) chifukwa chotama nyonga zake, ndipo adati: “Uyu ndi wamatsenga kapena wamisala.” info
التفاسير:

external-link copy
40 : 51

فَأَخَذۡنَٰهُ وَجُنُودَهُۥ فَنَبَذۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡيَمِّ وَهُوَ مُلِيمٞ

Tidamlanga pamodzi ndi khamu lake la nkhondo ndi kuwaponya mnyanja; iye ali wodzudzulidwa. info
التفاسير:

external-link copy
41 : 51

وَفِي عَادٍ إِذۡ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلرِّيحَ ٱلۡعَقِيمَ

Ndipo m’nkhani ya Âdi (muli phunziro) pamene tidawatumizira chimphepo (chamkuntho) chopanda chabwino mkati mwake. info
التفاسير:

external-link copy
42 : 51

مَا تَذَرُ مِن شَيۡءٍ أَتَتۡ عَلَيۡهِ إِلَّا جَعَلَتۡهُ كَٱلرَّمِيمِ

Chomwe sichisiya chinthu chimene chachidutsa koma kuchichita monga chofumbwa. info
التفاسير:

external-link copy
43 : 51

وَفِي ثَمُودَ إِذۡ قِيلَ لَهُمۡ تَمَتَّعُواْ حَتَّىٰ حِينٖ

Ndipo m’nkhani ya Samudu (muli chisonyezo) pamene kudanenedwa kwa iwo kuti: “Sangalalani (mnyumba zanu) mpaka nthawi yaikika.” info
التفاسير:

external-link copy
44 : 51

فَعَتَوۡاْ عَنۡ أَمۡرِ رَبِّهِمۡ فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّٰعِقَةُ وَهُمۡ يَنظُرُونَ

Koma adadzikweza (ponyozera) lamulo la Mbuye wawo. Choncho chiphokoso chidawaononga uku akupenya. info
التفاسير:

external-link copy
45 : 51

فَمَا ٱسۡتَطَٰعُواْ مِن قِيَامٖ وَمَا كَانُواْ مُنتَصِرِينَ

Sadathe kuimilira ndi (kuthawa) ndiponso sadali wodzipulumutsa. info
التفاسير:

external-link copy
46 : 51

وَقَوۡمَ نُوحٖ مِّن قَبۡلُۖ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمٗا فَٰسِقِينَ

Naonso anthu a Nuh (tidawaononga) kale chifukwa iwo adali anthu otuluka mchilamulo (cha Allah). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 51

وَٱلسَّمَآءَ بَنَيۡنَٰهَا بِأَيۡيْدٖ وَإِنَّا لَمُوسِعُونَ

Thambo tidalimanga mwamphamvu (ndi luntha); ndipo tingathe kuchita zochuluka (kuposa zimenezi.) info
التفاسير:

external-link copy
48 : 51

وَٱلۡأَرۡضَ فَرَشۡنَٰهَا فَنِعۡمَ ٱلۡمَٰهِدُونَ

Ndipo nthaka tidaiyala; taonani kukonza bwino Ife amene tidakonza nthaka! info
التفاسير:

external-link copy
49 : 51

وَمِن كُلِّ شَيۡءٍ خَلَقۡنَا زَوۡجَيۡنِ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ

Ndipo m’chinthu chilichonse talenga ziwiriziwiri kuti inu mulingalire (ndi kukhulupirira mphamvu Zathu). info
التفاسير:

external-link copy
50 : 51

فَفِرُّوٓاْ إِلَى ٱللَّهِۖ إِنِّي لَكُم مِّنۡهُ نَذِيرٞ مُّبِينٞ

Thawirani kwa Allah. Ine ndine mchenjezi woonekera kwa inu wochokera kwa Iye. info
التفاسير:

external-link copy
51 : 51

وَلَا تَجۡعَلُواْ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَۖ إِنِّي لَكُم مِّنۡهُ نَذِيرٞ مُّبِينٞ

Ndipo musadzipangire mulungu wina wompembedza ndi kumuphatikiza ndi Allah. Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera poyera kwa inu wochokera kwa Iye. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 51

كَذَٰلِكَ مَآ أَتَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا قَالُواْ سَاحِرٌ أَوۡ مَجۡنُونٌ

Momwemo (ndimo idalili mibadwo yakale pamodzi ndi aneneri awo); palibe Mthenga amene adawadzera anthu akale, anthu akowa kulibe, popanda kumnena kuti: “Ndiwamatsenga kapena wamisala.” info
التفاسير:

external-link copy
53 : 51

أَتَوَاصَوۡاْ بِهِۦۚ بَلۡ هُمۡ قَوۡمٞ طَاغُونَ

Kodi adalangizana za mawuwa pakati pawo? Iyayi, koma iwo ndianthu opyola malire. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 51

فَتَوَلَّ عَنۡهُمۡ فَمَآ أَنتَ بِمَلُومٖ

Choncho apatukire iwo (amakani), iwe suli wodzudzulidwa (pakuleka kwawo kuyankha kuitana). info
التفاسير:

external-link copy
55 : 51

وَذَكِّرۡ فَإِنَّ ٱلذِّكۡرَىٰ تَنفَعُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Kumbutsa. Ndithu kukumbutsa kumawathandiza okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 51

وَمَا خَلَقۡتُ ٱلۡجِنَّ وَٱلۡإِنسَ إِلَّا لِيَعۡبُدُونِ

Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti azindipembedza. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 51

مَآ أُرِيدُ مِنۡهُم مِّن رِّزۡقٖ وَمَآ أُرِيدُ أَن يُطۡعِمُونِ

Sindifuna kwa iwo chithandizo ndiponso sindifuna kuti azindidyetsa. info
التفاسير:

external-link copy
58 : 51

إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلرَّزَّاقُ ذُو ٱلۡقُوَّةِ ٱلۡمَتِينُ

Ndithu Allah ndi Amene amapereka rizq; Iye ndi Mwini mphamvu zoposa; Wolimba, (salaphera kanthu). info
التفاسير:

external-link copy
59 : 51

فَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ ذَنُوبٗا مِّثۡلَ ذَنُوبِ أَصۡحَٰبِهِمۡ فَلَا يَسۡتَعۡجِلُونِ

Ndithu amene adzichitira okha chinyengo (pokana ndi kutsutsa) ali nalo gawo la chilango monga gawo la anzawo (a mibadwo yakale); choncho asandifulumizitse (kutsitsa chilango nthawi yake isanafike)! info
التفاسير:

external-link copy
60 : 51

فَوَيۡلٞ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن يَوۡمِهِمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ

Kuonongeka kuli pa amene atsutsa za tsiku lawo limene alonjezedwa. info
التفاسير: