قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

بەت نومۇرى:close

external-link copy
17 : 40

ٱلۡيَوۡمَ تُجۡزَىٰ كُلُّ نَفۡسِۭ بِمَا كَسَبَتۡۚ لَا ظُلۡمَ ٱلۡيَوۡمَۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَرِيعُ ٱلۡحِسَابِ

Mzimu uliwonse lero, ulipidwa zimene udachita; palibe kupondereza lero (pochepetsa mphoto kapena kuonjeza chilango). Ndithu Allah Ngwachangu (pa) chiwerengero Chake. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 40

وَأَنذِرۡهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡأٓزِفَةِ إِذِ ٱلۡقُلُوبُ لَدَى ٱلۡحَنَاجِرِ كَٰظِمِينَۚ مَا لِلظَّٰلِمِينَ مِنۡ حَمِيمٖ وَلَا شَفِيعٖ يُطَاعُ

Achenjeze (iwe Mtumiki {s.a.w}) za tsiku lomwe lili pafupi (Qiyâma), pamene mitima idzakhala ku mmero (chifukwa cha mantha oopsa) atadzadzidwa ndi nkhawa. Wodzichitira chinyengo sazakhala ndi bwenzi ngakhale mpulumutsi womveredwa (powateteza iwo). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 40

يَعۡلَمُ خَآئِنَةَ ٱلۡأَعۡيُنِ وَمَا تُخۡفِي ٱلصُّدُورُ

Iye (Allah ) akudziwa kuyang’ana kwa maso a chinyengo ndi zimene zifuwa zikubisa (mzobisika zonse). info
التفاسير:

external-link copy
20 : 40

وَٱللَّهُ يَقۡضِي بِٱلۡحَقِّۖ وَٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ لَا يَقۡضُونَ بِشَيۡءٍۗ إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ

Ndipo Allah amaweruza mwa chilungamo. Koma omwe akuwapembedza kusiya Allah, saweruza chilichonse (chifukwa cha kufooka ndi kulephera kwawo). Ndithu Allah Yekha ndiye Wakumva, Woona (chilichonse). info
التفاسير:

external-link copy
21 : 40

۞ أَوَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ كَانُواْ مِن قَبۡلِهِمۡۚ كَانُواْ هُمۡ أَشَدَّ مِنۡهُمۡ قُوَّةٗ وَءَاثَارٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ فَأَخَذَهُمُ ٱللَّهُ بِذُنُوبِهِمۡ وَمَا كَانَ لَهُم مِّنَ ٱللَّهِ مِن وَاقٖ

Kodi sadayende padziko ndikuona momwe mathero a anthu akale adalili? Adali opambana panyonga ndi mzochitachita zawo za mdziko kuposa iwo, (monga kumanga nyumba zikuluzikulu). Koma Allah adawaononga, psiti! chifukwa cha machimo awo, ndipo adalibe mtetezi ku chilango cha Allah. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 40

ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ كَانَت تَّأۡتِيهِمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَكَفَرُواْ فَأَخَذَهُمُ ٱللَّهُۚ إِنَّهُۥ قَوِيّٞ شَدِيدُ ٱلۡعِقَابِ

Zimenezo nchifukwa chakuti ankawadzera aneneri awo ndi zizizwa zoonekera poyera, koma adazikanira. Choncho Allah adawaononga motheratu. Iye Ngwanyonga zambiri, Wolanga mokhwima. info
التفاسير:

external-link copy
23 : 40

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَا وَسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٍ

Ndipo ndithu tidamtuma Mûsa ndi zizizwa zathu ndi zisonyezo zamphamvu zoonekera poyera, info
التفاسير:

external-link copy
24 : 40

إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَهَٰمَٰنَ وَقَٰرُونَ فَقَالُواْ سَٰحِرٞ كَذَّابٞ

Kwa Farawo ndi Haamana ndi Kaaruna. Ndipo adati: “(Uyu) ndi wamatsenga, wabodza.” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 40

فَلَمَّا جَآءَهُم بِٱلۡحَقِّ مِنۡ عِندِنَا قَالُواْ ٱقۡتُلُوٓاْ أَبۡنَآءَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ وَٱسۡتَحۡيُواْ نِسَآءَهُمۡۚ وَمَا كَيۡدُ ٱلۡكَٰفِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَٰلٖ

Ndipo pamene (Mûsa) adawadzera ndi choona chochokera kwa Ife, (Farawo pamodzi ndi omtsatira) adati: “Iphani ana achimuna a amene akhulupirira naye limodzi; ndipo siyani ana awo achikazi.” Koma ndale za okanira sizakanthu, nzotaika. info
التفاسير: