قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

external-link copy
49 : 33

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا نَكَحۡتُمُ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ ثُمَّ طَلَّقۡتُمُوهُنَّ مِن قَبۡلِ أَن تَمَسُّوهُنَّ فَمَا لَكُمۡ عَلَيۡهِنَّ مِنۡ عِدَّةٖ تَعۡتَدُّونَهَاۖ فَمَتِّعُوهُنَّ وَسَرِّحُوهُنَّ سَرَاحٗا جَمِيلٗا

E inu amene mwakhulupirira! Mukakwatira akazi okhulupirira, kenako ndikulekana nawo musadawakhudze, inu mulibe chiwerengero cha ‘Edda’ pa iwo choti nkuchiwerengera. Asangalatseni powapatsa cholekanira. siyananawoni; kusiyana kwabwino.[329] info

[329] ‘Edda’ ndi nthawi imene mkazi amakhala pa chiyembekezero asanakwatiwe ndi mwamuna wina pambuyo posiyana. Edda zilipo za mitundu iwiri: yosiyana ukwati yomwe mkazi amayembekezera miyezi itatu ndi yomwalira mwamuna yomwe mkazi amayembekezera miyezi inayi ndi masiku khumi. Koma mkazi wapakati Edda yake imatha ndikubereka. Yang’anani ndemanga ya Qur’an ( 2 : 228 ).

التفاسير: