قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

بەت نومۇرى:close

external-link copy
51 : 28

۞ وَلَقَدۡ وَصَّلۡنَا لَهُمُ ٱلۡقَوۡلَ لَعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ

Ndipo ndithu tafikitsa mawu kwa iwo mochulukitsa, mwatsatanetsatane kuti iwo akumbukire. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 28

ٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلِهِۦ هُم بِهِۦ يُؤۡمِنُونَ

Amene tidawapatsa buku kale ili lisadadze, akulikhulupirira ili (buku la Qur’an). info
التفاسير:

external-link copy
53 : 28

وَإِذَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِهِۦٓ إِنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّنَآ إِنَّا كُنَّا مِن قَبۡلِهِۦ مُسۡلِمِينَ

Ndipo likawerengedwa kwa iwo, akuti: “Talikhulupirira; ndithu ichi nchoona chochokera kwa Mbuye wathu; ndithu ilo lisanadze ife tidali Asilamu (ogonjera Allah).” info
التفاسير:

external-link copy
54 : 28

أُوْلَٰٓئِكَ يُؤۡتَوۡنَ أَجۡرَهُم مَّرَّتَيۡنِ بِمَا صَبَرُواْ وَيَدۡرَءُونَ بِٱلۡحَسَنَةِ ٱلسَّيِّئَةَ وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ

Iwo adzapatsidwa malipiro awo kawiri (chifukwa chotsatira Mneneri Mûsa Ndi Mneneri Isa (Yesu), kale; ndipo tsopano ndikumtsatira Mneneri Muhammad{s.a.w}) nchifukwa chakuti adapirira; amachotsa choipa (pochita) chabwino, ndipo m’zimene tawapatsa akupereka chopereka (Sadaka). info
التفاسير:

external-link copy
55 : 28

وَإِذَا سَمِعُواْ ٱللَّغۡوَ أَعۡرَضُواْ عَنۡهُ وَقَالُواْ لَنَآ أَعۡمَٰلُنَا وَلَكُمۡ أَعۡمَٰلُكُمۡ سَلَٰمٌ عَلَيۡكُمۡ لَا نَبۡتَغِي ٱلۡجَٰهِلِينَ

Ndipo akamva zopanda pake amazipewa, ndipo amati (kwa achibwanawo): “Ife tili ndi zochita zathu inunso muli ndi zochita zanu, mtendere ukhale pa inu. Ife sitifuna (kutsutsana) ndi mbuli.” info
التفاسير:

external-link copy
56 : 28

إِنَّكَ لَا تَهۡدِي مَنۡ أَحۡبَبۡتَ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ يَهۡدِي مَن يَشَآءُۚ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُهۡتَدِينَ

Ndithu iwe sungathe kumuongola amene ukumfuna, koma Allah amamuongola amene wamfuna. Ndipo Iye akudziwa za amene ali oongoka. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 28

وَقَالُوٓاْ إِن نَّتَّبِعِ ٱلۡهُدَىٰ مَعَكَ نُتَخَطَّفۡ مِنۡ أَرۡضِنَآۚ أَوَلَمۡ نُمَكِّن لَّهُمۡ حَرَمًا ءَامِنٗا يُجۡبَىٰٓ إِلَيۡهِ ثَمَرَٰتُ كُلِّ شَيۡءٖ رِّزۡقٗا مِّن لَّدُنَّا وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

Ndipo akunena (akafiri a m’ Makka, kuuza Mtumiki): “Ngati titsatira chiongoko (ichi chimene wadza nacho) pamodzi ndi iwe, tifwambidwa m’dziko lathu (potimenya nkhondo mafuko ena a Arabu).” Kodi sitidawakhazike pamalo opatulika ndi pa mtendere pomwe zipatso za mitundumitundu zikudza pamenepo mwaulere (monga rizq) zochokera kwa Ife? Koma ambiri a iwo sadziwa. info
التفاسير:

external-link copy
58 : 28

وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَرۡيَةِۭ بَطِرَتۡ مَعِيشَتَهَاۖ فَتِلۡكَ مَسَٰكِنُهُمۡ لَمۡ تُسۡكَن مِّنۢ بَعۡدِهِمۡ إِلَّا قَلِيلٗاۖ وَكُنَّا نَحۡنُ ٱلۡوَٰرِثِينَ

Kodi ndimidzi ingati imene tidaiononga yomwe inkanyadira za moyo wawo (wosavutika ndi wodya bwino)! Umo m’malo mwawo simudakhalidwebe pambuyo pawo koma mochepa basi; ndipo ife tidalowa chokolo m’zimenezi. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 28

وَمَا كَانَ رَبُّكَ مُهۡلِكَ ٱلۡقُرَىٰ حَتَّىٰ يَبۡعَثَ فِيٓ أُمِّهَا رَسُولٗا يَتۡلُواْ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتِنَاۚ وَمَا كُنَّا مُهۡلِكِي ٱلۡقُرَىٰٓ إِلَّا وَأَهۡلُهَا ظَٰلِمُونَ

Ndipo Mbuye wako sali owononga midzi pokhapokha akatuma mtumiki mu mzinda wawo waukulu ndi kuwawerengera mawu a m’ndime Zathu, (akakana ndi pamene timawaononga); ndiponso sitili owononga midzi pokhapokha anthu ake atakhala achinyengo. info
التفاسير: