قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

بەت نومۇرى:close

external-link copy
45 : 21

قُلۡ إِنَّمَآ أُنذِرُكُم بِٱلۡوَحۡيِۚ وَلَا يَسۡمَعُ ٱلصُّمُّ ٱلدُّعَآءَ إِذَا مَا يُنذَرُونَ

Nena: “Ndithu ndikukuchenjezani ndi chivumbulutso (cha Allah). Koma agonthi samva kuitana pamene akuchenjezedwa.” info
التفاسير:

external-link copy
46 : 21

وَلَئِن مَّسَّتۡهُمۡ نَفۡحَةٞ مِّنۡ عَذَابِ رَبِّكَ لَيَقُولُنَّ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ

Ndipo kukadawakhudza kumenya kumodzi kwa chilango cha Mbuye wako, ndithudi, (akadadzichepetsa nthawi yomweyo). Akadanena: “Tsoka kwa ife ndithu tidali osalungama.” info
التفاسير:

external-link copy
47 : 21

وَنَضَعُ ٱلۡمَوَٰزِينَ ٱلۡقِسۡطَ لِيَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَلَا تُظۡلَمُ نَفۡسٞ شَيۡـٔٗاۖ وَإِن كَانَ مِثۡقَالَ حَبَّةٖ مِّنۡ خَرۡدَلٍ أَتَيۡنَا بِهَاۗ وَكَفَىٰ بِنَا حَٰسِبِينَ

Ndipo tsiku la Qiyâma tidzaika masikero achilungamo, choncho mzimu uliwonse sudzachitidwa chinyengo pa chilichonse. Ngakhale (chinthucho) chili cholemera ngati njere ya mpiru, tidzachibweretsa; ndipo tikukwana (kukhala akatswiri) pa chiwerengero. info
التفاسير:

external-link copy
48 : 21

وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ ٱلۡفُرۡقَانَ وَضِيَآءٗ وَذِكۡرٗا لِّلۡمُتَّقِينَ

Ndipo ndithu Mûsa ndi Harun tidawapatsa (buku) losiyanitsa pakati pa choonadi ndi chonama, ndiponso muuni ndi ulaliki kwa anthu oopa (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
49 : 21

ٱلَّذِينَ يَخۡشَوۡنَ رَبَّهُم بِٱلۡغَيۡبِ وَهُم مِّنَ ٱلسَّاعَةِ مُشۡفِقُونَ

Omwe akumuopa Mbuye wawo ngakhale ali paokha, omwenso amaopa Qiyâma. info
التفاسير:

external-link copy
50 : 21

وَهَٰذَا ذِكۡرٞ مُّبَارَكٌ أَنزَلۡنَٰهُۚ أَفَأَنتُمۡ لَهُۥ مُنكِرُونَ

Ndipo iyi (Qur’an) ndi ulaliki wodalitsika umene tauvumbulutsa (kwa inu); kodi inu mukuikana? info
التفاسير:

external-link copy
51 : 21

۞ وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَآ إِبۡرَٰهِيمَ رُشۡدَهُۥ مِن قَبۡلُ وَكُنَّا بِهِۦ عَٰلِمِينَ

Ndipo ndithu Ibrahim tidampatsa kulungama kwake kuyambira kale (kuubwana), ndipo tinkamudziwa (bwinobwino). info
التفاسير:

external-link copy
52 : 21

إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦ مَا هَٰذِهِ ٱلتَّمَاثِيلُ ٱلَّتِيٓ أَنتُمۡ لَهَا عَٰكِفُونَ

(Akumbutse anthu) pamene adauza bambo wake ndi anthu ake, “Nchiyani mafano awa omwe inu nthawi zonse mukupitiriza kuwapembedza.” info
التفاسير:

external-link copy
53 : 21

قَالُواْ وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا لَهَا عَٰبِدِينَ

Adati: “Tidapeza makolo athu akuwapembedza. (Choncho nafenso Tikuwapembedza).” info
التفاسير:

external-link copy
54 : 21

قَالَ لَقَدۡ كُنتُمۡ أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُمۡ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ

(Iye) adati: “Ndithu inu ndi makolo anu mudali mkusokera koonekera.” info
التفاسير:

external-link copy
55 : 21

قَالُوٓاْ أَجِئۡتَنَا بِٱلۡحَقِّ أَمۡ أَنتَ مِنَ ٱللَّٰعِبِينَ

(Iwo) adati: “Kodi watibweretsera choonadi, kapena iwe ndi m’modzi mwa osereula?” info
التفاسير:

external-link copy
56 : 21

قَالَ بَل رَّبُّكُمۡ رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ ٱلَّذِي فَطَرَهُنَّ وَأَنَا۠ عَلَىٰ ذَٰلِكُم مِّنَ ٱلشَّٰهِدِينَ

(Iye) adati: (“Iyayi, ine siwosereula), koma Mbuye wanu, ndi Mbuye wa thambo ndi nthaka amene adalenga zimenezi; ine pa zimenezi, ndine m’modzi wochitira umboni.” info
التفاسير:

external-link copy
57 : 21

وَتَٱللَّهِ لَأَكِيدَنَّ أَصۡنَٰمَكُم بَعۡدَ أَن تُوَلُّواْ مُدۡبِرِينَ

“Ndipo ndikulumbilira Allah, ndiwachitira chiwembu mafano anuwo pambuyo ponditembenukira misana kupita komwe mukupita.” info
التفاسير: