قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا

Maryam

external-link copy
1 : 19

كٓهيعٓصٓ

Kâf-Hâ-Yâ- ‘Aîn-Sâd. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 19

ذِكۡرُ رَحۡمَتِ رَبِّكَ عَبۡدَهُۥ زَكَرِيَّآ

Ichi (ndi) chikumbutso cha chifundo cha Mbuye wako pa kapolo Wake Zakariya. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 19

إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥ نِدَآءً خَفِيّٗا

Pamene adaitana Mbuye wake, kuitana kwa chinsinsi. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 19

قَالَ رَبِّ إِنِّي وَهَنَ ٱلۡعَظۡمُ مِنِّي وَٱشۡتَعَلَ ٱلرَّأۡسُ شَيۡبٗا وَلَمۡ أَكُنۢ بِدُعَآئِكَ رَبِّ شَقِيّٗا

Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu mafupa anga afooka, ndipo mutu wanga wayaka (ukung’anima) ndi imvi; sindidali watsoka pokupemphani Mbuye wanga (koma nthawi iliyonse ndikakupemphani mumandivomereza)[264] info

[264] Apa tanthauzo lake nkuti: “E Mbuye wanga! Palibe pamene mudalitaya pachabe pempho langa koma mudandizoloweza kuti ndikakupemphani mumandipatsa zomwe ndapempha. Choncho yankhaninso pempho langali.”

التفاسير:

external-link copy
5 : 19

وَإِنِّي خِفۡتُ ٱلۡمَوَٰلِيَ مِن وَرَآءِي وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرٗا فَهَبۡ لِي مِن لَّدُنكَ وَلِيّٗا

“Ndipo ndithu ine ndikuopera abale anga (kuononga chipembedzo) pambuyo panga; ndipo mkazi wanga ndi chumba; choncho ndipatseni (mwana) mlowammalo wanga wochokera kwa Inu.” info
التفاسير:

external-link copy
6 : 19

يَرِثُنِي وَيَرِثُ مِنۡ ءَالِ يَعۡقُوبَۖ وَٱجۡعَلۡهُ رَبِّ رَضِيّٗا

“Adzandilowe chokolo (pa nzeru za utsogoleri ndi uneneri) ndikulowanso ufumu wa banja la Ya’qub; ndipo Mbuye wanga nchiteni kukhala woyanjidwa (ndi Inu)” info
التفاسير:

external-link copy
7 : 19

يَٰزَكَرِيَّآ إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَٰمٍ ٱسۡمُهُۥ يَحۡيَىٰ لَمۡ نَجۡعَل لَّهُۥ مِن قَبۡلُ سَمِيّٗا

(Adauzidwa): “E iwe Zakariya! Ife tikukuuza nkhani yabwino yakuti ubereka mwana dzina lake Yahya palibe patsogolo pake amene tidamutcha dzina longa lake.” info
التفاسير:

external-link copy
8 : 19

قَالَ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٞ وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرٗا وَقَدۡ بَلَغۡتُ مِنَ ٱلۡكِبَرِ عِتِيّٗا

(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndingapeze bwanji mwana pomwe mkazi wanga ndi nkhalamba yosabereka ndipo ine ndafikanso pa ukulu wopyola muyeso?” info
التفاسير:

external-link copy
9 : 19

قَالَ كَذَٰلِكَ قَالَ رَبُّكَ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٞ وَقَدۡ خَلَقۡتُكَ مِن قَبۡلُ وَلَمۡ تَكُ شَيۡـٔٗا

Adati: “Ndimomwemo. Mbuye wako wanena (kuti): ‘Izi nzofewa kwa Ine; ndithu ndidakulenga kale pomwe iwe sudali kanthu.” info
التفاسير:

external-link copy
10 : 19

قَالَ رَبِّ ٱجۡعَل لِّيٓ ءَايَةٗۖ قَالَ ءَايَتُكَ أَلَّا تُكَلِّمَ ٱلنَّاسَ ثَلَٰثَ لَيَالٖ سَوِيّٗا

Adati: “Mbuye wanga ndipatseni chizindikiro (chodziwitsa kuti mkazi wanga ali ndi pakati).” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu pomwe iwe uli bwinobwino.” info
التفاسير:

external-link copy
11 : 19

فَخَرَجَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ مِنَ ٱلۡمِحۡرَابِ فَأَوۡحَىٰٓ إِلَيۡهِمۡ أَن سَبِّحُواْ بُكۡرَةٗ وَعَشِيّٗا

Ndipo adatuluka kuchipinda chopemphelera ndikuonekera kwa anthu ake, ndipo adawalozera (pomwe sadathe kuyankhula) kuti: “Lemekezani Allah m’mawa ndi madzulo.” info
التفاسير: