Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - Çevaca Tercüme - Halid İbrahim Pitala

Sayfa numarası:close

external-link copy
71 : 36

أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا خَلَقۡنَا لَهُم مِّمَّا عَمِلَتۡ أَيۡدِينَآ أَنۡعَٰمٗا فَهُمۡ لَهَا مَٰلِكُونَ

Kodi saona kuti Ife tawalengera nyama, m’zimene manja Athu akonza, zomwe iwo akuti nzawo. info
التفاسير:

external-link copy
72 : 36

وَذَلَّلۡنَٰهَا لَهُمۡ فَمِنۡهَا رَكُوبُهُمۡ وَمِنۡهَا يَأۡكُلُونَ

Ndi kuti tazichita kukhala zowatumikira? Zina mwa izo amazikwerapo; ndipo zina mwa izo amazidya. info
التفاسير:

external-link copy
73 : 36

وَلَهُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ وَمَشَارِبُۚ أَفَلَا يَشۡكُرُونَ

Ndipo m’menemo (m’nyama) muli zowathandiza (zambiri) ndiponso zakumwa. Nanga bwanji sathokoza? info
التفاسير:

external-link copy
74 : 36

وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ ءَالِهَةٗ لَّعَلَّهُمۡ يُنصَرُونَ

Ndipo adzipangira milungu (yabodza) kusiya Allah kuti athandizidwe nayo. info
التفاسير:

external-link copy
75 : 36

لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَهُمۡ وَهُمۡ لَهُمۡ جُندٞ مُّحۡضَرُونَ

(Koma) siingathe kuwathandiza; ndipo iwo (kwa milunguyo) ndi asilikali amene akonzedwa kulondera (mafanowo ndi kuwatumikira). info
التفاسير:

external-link copy
76 : 36

فَلَا يَحۡزُنكَ قَوۡلُهُمۡۘ إِنَّا نَعۡلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعۡلِنُونَ

Mawu awo (onyoza Allah ndi okutsutsa iwe) asakudandaulitse. Ndithu Ife tikudziwa zimene akubisa ndi zimene akuzionetsera poyera. info
التفاسير:

external-link copy
77 : 36

أَوَلَمۡ يَرَ ٱلۡإِنسَٰنُ أَنَّا خَلَقۡنَٰهُ مِن نُّطۡفَةٖ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٞ مُّبِينٞ

Kodi munthu sazindikira kuti Ife tidamulenga ndi dontho la umuna? Koma iye wakhala wotsutsa woonekera. info
التفاسير:

external-link copy
78 : 36

وَضَرَبَ لَنَا مَثَلٗا وَنَسِيَ خَلۡقَهُۥۖ قَالَ مَن يُحۡيِ ٱلۡعِظَٰمَ وَهِيَ رَمِيمٞ

Ndipo akutiponyera fanizo (lotsutsa kukhoza Kwathu kuukitsa akufa) ndi kuiwala chilengedwe chake (chochokera kumadzi opanda pake). Akunena: “Ndani angaukitse mafupa pomwe ali ofumbwa?” info
التفاسير:

external-link copy
79 : 36

قُلۡ يُحۡيِيهَا ٱلَّذِيٓ أَنشَأَهَآ أَوَّلَ مَرَّةٖۖ وَهُوَ بِكُلِّ خَلۡقٍ عَلِيمٌ

Nena: “Adzawaukitsa Yemwe adawalenga panthawi yoyamba. Ndipo Iye Ngodziwa kalengedwe ka mtundu uliwonse. info
التفاسير:

external-link copy
80 : 36

ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلشَّجَرِ ٱلۡأَخۡضَرِ نَارٗا فَإِذَآ أَنتُم مِّنۡهُ تُوقِدُونَ

Yemwe adakupangirani moto kuchokera mu mtengo wauwisi; kenako inu mumakoleza moto m’menemo. info
التفاسير:

external-link copy
81 : 36

أَوَلَيۡسَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يَخۡلُقَ مِثۡلَهُمۚ بَلَىٰ وَهُوَ ٱلۡخَلَّٰقُ ٱلۡعَلِيمُ

Kodi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka (mukuganiza kuti) siwokhoza kuwalenga (iwo kachiwiri) monga momwe alili? Inde! Iye ndi Mlengi Wamkulu, Wodziwa kwambiri! info
التفاسير:

external-link copy
82 : 36

إِنَّمَآ أَمۡرُهُۥٓ إِذَآ أَرَادَ شَيۡـًٔا أَن يَقُولَ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ

Ndithu machitidwe Ake akafuna kuti chinthu chichitike, amangonena kwa icho: “Chitika!” Ndipo chimachitika (nthawi yomweyo). info
التفاسير:

external-link copy
83 : 36

فَسُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي بِيَدِهِۦ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيۡءٖ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ

Kotero alemekezeke Yemwe m’manja Mwake muli ulamuliro pa chinthu chilichonse; ndipo kwa Iye (ndiko) mudzabweerera nonse. info
التفاسير: