[67] (Ndime 35-36) Mkazi wa Imran pamene adali ndi pakati, ankaganiza kuti adzabereka mwana wa mwamuna. Ndipo adalonjeza kwa Allah kuti mwanayo adzampereka kuti akhale wotumikira ku msikiti wa Baiti Limakadasi (Yelusalemu), ndi kutinso adzatumikire pa zinthu zina za chipembedzo. Ntchito yake idzangokhala yokhayo. Koma mmalomwake adabereka mwana wamkazi. Ndipo kuti adzakhale mwana wabwino nkutinso adzabereke ana abwino, adamutcha dzina loti Mariya (wotumikira Allah). Tero mayi Mariya adali mayi wabwino. Ndipo nayenso adabala mwana wabwino yemwe ndi mneneri Isa (Yesu). Mariya ndi mayi wolemekezeka kwabasi.