Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Ash-Shams

external-link copy
1 : 91

وَٱلشَّمۡسِ وَضُحَىٰهَا

Ndikulumbilira dzuwa ndi dangalira lake. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 91

وَٱلۡقَمَرِ إِذَا تَلَىٰهَا

Ndi mwezi pamene ukulitsatira (dzuwalo ndikulowa mmalo mwake powalitsa dziko dzuwalo litalowa). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 91

وَٱلنَّهَارِ إِذَا جَلَّىٰهَا

Ndi usana pamene ukulisonyeza poyera (kuti lisaphimbidwe). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 91

وَٱلَّيۡلِ إِذَا يَغۡشَىٰهَا

Ndi usiku pamene ukuliphimba. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 91

وَٱلسَّمَآءِ وَمَا بَنَىٰهَا

Ndi thambo ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu) Yemwe adalimanga ndi kulitukula (mwaluso). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 91

وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا طَحَىٰهَا

Ndi nthaka ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu), Yemwe adaiyala (mbali zonse ndi kuichita kukhala ngati choyala). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 91

وَنَفۡسٖ وَمَا سَوَّىٰهَا

Ndi mzimu ndi Yemwe adawulinganiza (powupatsa mphamvu). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 91

فَأَلۡهَمَهَا فُجُورَهَا وَتَقۡوَىٰهَا

Ndipo adaudziwitsa zoipa zake ndi zabwino zake; (ndi kuwupatsa ufulu ndi mphamvu zochitira zimene ukufuna). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 91

قَدۡ أَفۡلَحَ مَن زَكَّىٰهَا

Ndithu wapambana amene wauyeretsa.[443] info

[443] Kuyeretsa mzimu ndiko kuukongoletsa ndi maphunziro ndi ntchito zabwino. Zimenezi ndizo zimamkwanitsa munthu kuti atchulidwe munthu. Ndipo zimenezi ndizo zingapereke ulemelero kwa munthu pa dziko mpaka pa tsiku lachimaliziro.

التفاسير:

external-link copy
10 : 91

وَقَدۡ خَابَ مَن دَسَّىٰهَا

Ndipo ndithu wataika amene wauononga.[444] info

[444] Kuwuononga mzimu ndiko kuuchitira mphwayi; kungoulekelera ndikumautsatira pa zimene ufuna mpaka kulowa mu uve ndi m’machimo a umbuli ndipo ndi kuonongeka pa dziko lino mpaka pa tsiku lachimaliziro.

التفاسير:

external-link copy
11 : 91

كَذَّبَتۡ ثَمُودُ بِطَغۡوَىٰهَآ

Thamud (Samudu) adakanira (Mneneri wawo) chifukwa cha kulumpha malire kwawo.[445] info

[445] (Ndime 11-15) Asamudu atchulidwa m’surat AL-FAJR. Anthu awa adamukana Mtumiki wawo, Mtumiki Swalih (a.s); adamuuza kuti ngati afuna amukhulupirire, atulutse ngamira kuchokera mthanthwe, apo ndipo adzamukhulupilira kuti ndi Mneneri. Swalih adampempha Allah, ndipo lidasweka thanthwe lija ndikutulukamo ngamira monga momwe adafunira anthu aja. Koma sadamukhulupirirebe. Mneneri Swalih (a.s) adawauza kuti: “Chenjerani ndi ngamira ya Allah iyi, musaikhudze ndi choipa chilichonse.” Ndipo adawakakamiza kuti pa tsiku limene ngamira ija ikumwa madzi, iwo asatunge madzi. Ndiponso pa tsiku limene iwo akutunga madzi ngamira siidzamwa madzi. Koma adamkanira. Ndipo m’modzi wa iwo amene adali wamphulupulu adaipha ngamira ija. Allah nthawi yomweyo adawatsitsira chilango chifukwa cha machimo awo, chomwe chidawakwanira onse kuyambira uja wopha ngamira ndi ena onse.

التفاسير:

external-link copy
12 : 91

إِذِ ٱنۢبَعَثَ أَشۡقَىٰهَا

Pamene woipitsitsa wawo adadzipereka (kupha ngamira yozizwitsa). info
التفاسير:

external-link copy
13 : 91

فَقَالَ لَهُمۡ رَسُولُ ٱللَّهِ نَاقَةَ ٱللَّهِ وَسُقۡيَٰهَا

Pamenepo Mneneri wa Allah (Swaleh) adawauza: “Isiyeni ngamira ya Allah (idye mdziko la Allah). Musailetse kumwa madzi (pa tsiku lake).” info
التفاسير:

external-link copy
14 : 91

فَكَذَّبُوهُ فَعَقَرُوهَا فَدَمۡدَمَ عَلَيۡهِمۡ رَبُّهُم بِذَنۢبِهِمۡ فَسَوَّىٰهَا

Koma adamutsutsa ndikuipha; kwa chifukwa chimenecho Mbuye wawo (Allah) adawaononga chifukwa cha tchimo lawo; adangowafafaniza (onse mnthaka). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 91

وَلَا يَخَافُ عُقۡبَٰهَا

Iye saopa zotsatira za chilangochi (chifukwa amenewa ndi malipiro a chilungamo pa zomwe adachita). info
التفاسير: