[443] Kuyeretsa mzimu ndiko kuukongoletsa ndi maphunziro ndi ntchito zabwino. Zimenezi ndizo zimamkwanitsa munthu kuti atchulidwe munthu. Ndipo zimenezi ndizo zingapereke ulemelero kwa munthu pa dziko mpaka pa tsiku lachimaliziro.
[445] (Ndime 11-15) Asamudu atchulidwa m’surat AL-FAJR. Anthu awa adamukana Mtumiki wawo, Mtumiki Swalih (a.s); adamuuza kuti ngati afuna amukhulupirire, atulutse ngamira kuchokera mthanthwe, apo ndipo adzamukhulupilira kuti ndi Mneneri. Swalih adampempha Allah, ndipo lidasweka thanthwe lija ndikutulukamo ngamira monga momwe adafunira anthu aja. Koma sadamukhulupirirebe. Mneneri Swalih (a.s) adawauza kuti: “Chenjerani ndi ngamira ya Allah iyi, musaikhudze ndi choipa chilichonse.” Ndipo adawakakamiza kuti pa tsiku limene ngamira ija ikumwa madzi, iwo asatunge madzi. Ndiponso pa tsiku limene iwo akutunga madzi ngamira siidzamwa madzi. Koma adamkanira. Ndipo m’modzi wa iwo amene adali wamphulupulu adaipha ngamira ija. Allah nthawi yomweyo adawatsitsira chilango chifukwa cha machimo awo, chomwe chidawakwanira onse kuyambira uja wopha ngamira ndi ena onse.