Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina: 402:396 close

external-link copy
53 : 29

وَيَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلۡعَذَابِ وَلَوۡلَآ أَجَلٞ مُّسَمّٗى لَّجَآءَهُمُ ٱلۡعَذَابُۚ وَلَيَأۡتِيَنَّهُم بَغۡتَةٗ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Ndipo akukupempha kuti chilango chidze mwachangu; kukadapanda kuti kudaikidwa nthawi yodziwika, chilango chikadawadzera. Ndipo ndithu chidzawadzera mwadzidzidzi asakudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 29

يَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلۡعَذَابِ وَإِنَّ جَهَنَّمَ لَمُحِيطَةُۢ بِٱلۡكَٰفِرِينَ

Akukupempha kuti chilango chidze mwachangu; ndithu Jahannam idzawazinga osakhuiupirira. info
التفاسير:

external-link copy
55 : 29

يَوۡمَ يَغۡشَىٰهُمُ ٱلۡعَذَابُ مِن فَوۡقِهِمۡ وَمِن تَحۡتِ أَرۡجُلِهِمۡ وَيَقُولُ ذُوقُواْ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Tsiku limene chidzawavindikira chilango kuchokera pamwamba pawo ndi pansi pa miyendo yawo; ndipo adzanena: “Lawani (chilango cha) zomwe munkachita.” info
التفاسير:

external-link copy
56 : 29

يَٰعِبَادِيَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِنَّ أَرۡضِي وَٰسِعَةٞ فَإِيَّٰيَ فَٱعۡبُدُونِ

E inu akapolo Anga amene mwakhulupirira! Ndithu nthaka Yanga njophanuka; (mukhoza kupita dziko lina ngati m’dziko lanulo simukupeza mwayi wopembedza Allah mokwanira); ndipo Ine ndekha ndipembedzeni. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 29

كُلُّ نَفۡسٖ ذَآئِقَةُ ٱلۡمَوۡتِۖ ثُمَّ إِلَيۡنَا تُرۡجَعُونَ

Chamoyo chilichonse chidzalawa imfa. Kenako mudzabwezedwa kwa Ife. info
التفاسير:

external-link copy
58 : 29

وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَنُبَوِّئَنَّهُم مِّنَ ٱلۡجَنَّةِ غُرَفٗا تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ نِعۡمَ أَجۡرُ ٱلۡعَٰمِلِينَ

Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndithudi tidzawakhazika m’zipinda za ku Munda wamtendere, momwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Taonani kukhala bwino malipiro a ochita zabwino! info
التفاسير:

external-link copy
59 : 29

ٱلَّذِينَ صَبَرُواْ وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ

Amene adapirira ndipo kwa Mbuye wawo amatsamira. info
التفاسير:

external-link copy
60 : 29

وَكَأَيِّن مِّن دَآبَّةٖ لَّا تَحۡمِلُ رِزۡقَهَا ٱللَّهُ يَرۡزُقُهَا وَإِيَّاكُمۡۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ

Ndinyama zingati zomwe sizidzipezera rizq lake. Allah akuzipatsa izo pamodzi ndi inunso. Ndipo Iye Ngwakumva; Ngodziwa. info
التفاسير:

external-link copy
61 : 29

وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۖ فَأَنَّىٰ يُؤۡفَكُونَ

Ndipo ngati utawafunsa (kuti): “Kodi ndani adalenga thambo ndi nthaka, ndi kugonjetsa dzuwa ndi mwezi?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nanga akutembenuzidwira kuti? info
التفاسير:

external-link copy
62 : 29

ٱللَّهُ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦ وَيَقۡدِرُ لَهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ

Allah amamtambasulira rizq amene wamfuna mwa akapolo Ake, ndi kumchepetsera (amene wamfunanso). Ndithu Allah Ngodziwa kwambiri za chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
63 : 29

وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّن نَّزَّلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَحۡيَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ مِنۢ بَعۡدِ مَوۡتِهَا لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۚ قُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡقِلُونَ

Ndipo ngati utawafunsa (kuti): “Kodi ndani amene akutsitsa madzi kuchokera ku mitambo ndi kuiukitsa nthaka ndi madziwo pambuyo pakufa kwake?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nena: “Kuyamikidwa konse nkwa Allah.” Koma ambiri a iwo sazindikira. info
التفاسير: