Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
31 : 29

وَلَمَّا جَآءَتۡ رُسُلُنَآ إِبۡرَٰهِيمَ بِٱلۡبُشۡرَىٰ قَالُوٓاْ إِنَّا مُهۡلِكُوٓاْ أَهۡلِ هَٰذِهِ ٱلۡقَرۡيَةِۖ إِنَّ أَهۡلَهَا كَانُواْ ظَٰلِمِينَ

Ndipo pamene atumiki athu adamdzera Ibrahim ndi nkhani yabwino (yoti abereka Mneneri Ishaq), adanenanso: “Ndithu tiwaononga eni mudzi uwu (wa Sodom); ndithu iwowo ngochimwa.” info
التفاسير:

external-link copy
32 : 29

قَالَ إِنَّ فِيهَا لُوطٗاۚ قَالُواْ نَحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَن فِيهَاۖ لَنُنَجِّيَنَّهُۥ وَأَهۡلَهُۥٓ إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ كَانَتۡ مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ

(Mneneri Ibrahim) adati: “Koma mmenemo muli Luti.” Iwo adati: “Ife ndife odziwa kwambiri za omwe ali m’menemo; ndithu timpulumutsa iye ndi banja lake kupatula mkazi wake; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).” info
التفاسير:

external-link copy
33 : 29

وَلَمَّآ أَن جَآءَتۡ رُسُلُنَا لُوطٗا سِيٓءَ بِهِمۡ وَضَاقَ بِهِمۡ ذَرۡعٗاۖ وَقَالُواْ لَا تَخَفۡ وَلَا تَحۡزَنۡ إِنَّا مُنَجُّوكَ وَأَهۡلَكَ إِلَّا ٱمۡرَأَتَكَ كَانَتۡ مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ

Ndipo pamene atumiki athu adamdzera Luti, adawadandaulira ndi kuwadera nkhawa; (ndipo iwo) adati: “Usaope ndipo usadandaule. Ndithu ife tikupulumutsa ndi banja lako kupatula mkazi wako; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).” info
التفاسير:

external-link copy
34 : 29

إِنَّا مُنزِلُونَ عَلَىٰٓ أَهۡلِ هَٰذِهِ ٱلۡقَرۡيَةِ رِجۡزٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ

“Ndithu ife tiwatsitsira chilango choipa kuchokera kumwamba eni mudzi uwu chifukwa cha kuchimwa kwawo (ndi kuukira malamulo a Allah).” info
التفاسير:

external-link copy
35 : 29

وَلَقَد تَّرَكۡنَا مِنۡهَآ ءَايَةَۢ بَيِّنَةٗ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ

Ndipo ndithu tidasiya chizindikiro mmenemo choonekera kwa anthu anzeru. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 29

وَإِلَىٰ مَدۡيَنَ أَخَاهُمۡ شُعَيۡبٗا فَقَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَٱرۡجُواْ ٱلۡيَوۡمَ ٱلۡأٓخِرَ وَلَا تَعۡثَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِينَ

Ndipo ku Madiyan (tidatumako) m’bale wawo Shuaib, ndipo adati: “E inu anthu anga! Mpembedzeni Allah ndipo opani tsiku lachimaliziro musanke mu ononga pa dziko.” info
التفاسير:

external-link copy
37 : 29

فَكَذَّبُوهُ فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلرَّجۡفَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دَارِهِمۡ جَٰثِمِينَ

Koma adamutsutsa. Ndipo kugwedezeka kwa nthaka kudawachotsa moyo wawo, ndipo kudawachera ali gwadegwade m’nyumba zawo (atafa). info
التفاسير:

external-link copy
38 : 29

وَعَادٗا وَثَمُودَاْ وَقَد تَّبَيَّنَ لَكُم مِّن مَّسَٰكِنِهِمۡۖ وَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَصَدَّهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ وَكَانُواْ مُسۡتَبۡصِرِينَ

Nawonso Âdi ndi Asamudu (tidawaononga). Ndipo mokhala mwawo mukudziwika kwa inu. Ndipo satana adawakometsera zochita zawo (zoipa), ndipo adawatsekereza ku njira (zabwino) chikhalirecho adali openya (anzeru zawo). info
التفاسير: