Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
85 : 28

إِنَّ ٱلَّذِي فَرَضَ عَلَيۡكَ ٱلۡقُرۡءَانَ لَرَآدُّكَ إِلَىٰ مَعَادٖۚ قُل رَّبِّيٓ أَعۡلَمُ مَن جَآءَ بِٱلۡهُدَىٰ وَمَنۡ هُوَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ

Ndithudi yemwe wakulamula kuitsata Qur’an, mwachoonadi adzakubwezera pa malo pobwerera. Nena! “Mbuye wanga ndi yemwe akudziwa amene wadza ndi chiongoko ndi yemwe ali m’kusokera koonekera poyera.’’ info
التفاسير:

external-link copy
86 : 28

وَمَا كُنتَ تَرۡجُوٓاْ أَن يُلۡقَىٰٓ إِلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبُ إِلَّا رَحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَۖ فَلَا تَكُونَنَّ ظَهِيرٗا لِّلۡكَٰفِرِينَ

Ndipo iwe sudali kulakalaka kuti ungapatsidwe buku (pamodzi ndi uneneri) koma izi zidachitika pa chifundo chochokera kwa Mbuye wako; choncho usakhale m’thandizi wa anthu osakhulupirira (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
87 : 28

وَلَا يَصُدُّنَّكَ عَنۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ بَعۡدَ إِذۡ أُنزِلَتۡ إِلَيۡكَۖ وَٱدۡعُ إِلَىٰ رَبِّكَۖ وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ

Ndipo asakutsekereze kutsatira ndime za (mawu a) Allah pa mbuyo povumbulutsidwa pa iwe, ndipo aitanire anthu kwa Mbuye wako, komatu usakhale m’gulu la anthu omphatikiza Allah ndi mafano. info
التفاسير:

external-link copy
88 : 28

وَلَا تَدۡعُ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَۘ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۚ كُلُّ شَيۡءٍ هَالِكٌ إِلَّا وَجۡهَهُۥۚ لَهُ ٱلۡحُكۡمُ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ

Ndipo usapemphe mulungu wina pa modzi ndi Allah. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye Yekha. Chinthu chilichonse chidzaonongeka kupatula Nkhope Yake. Ulamuliro (wazinthu zonse) uli kwa Iye ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera nonsenu. info
التفاسير: