Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
78 : 28

قَالَ إِنَّمَآ أُوتِيتُهُۥ عَلَىٰ عِلۡمٍ عِندِيٓۚ أَوَلَمۡ يَعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ قَدۡ أَهۡلَكَ مِن قَبۡلِهِۦ مِنَ ٱلۡقُرُونِ مَنۡ هُوَ أَشَدُّ مِنۡهُ قُوَّةٗ وَأَكۡثَرُ جَمۡعٗاۚ وَلَا يُسۡـَٔلُ عَن ذُنُوبِهِمُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ

Adati: “Ndithu ndapatsidwa izi chifukwa cha kudziwa kwanga komwe ndili nako.” Kodi iye sadadziwe kuti Allah adawaononga anthu patsogolo pake omwe adali anyonga kwambiri kuposa iye, komanso osonkhanitsa chuma chambiri? Ndipo oipa sadzafunsidwa zolakwa zawo. (Allah akudziwa zonse za iwo)! info
التفاسير:

external-link copy
79 : 28

فَخَرَجَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ فِي زِينَتِهِۦۖ قَالَ ٱلَّذِينَ يُرِيدُونَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا يَٰلَيۡتَ لَنَا مِثۡلَ مَآ أُوتِيَ قَٰرُونُ إِنَّهُۥ لَذُو حَظٍّ عَظِيمٖ

Choncho, adatulukira kwa anthu ake (monyada) uku atadzikongoletsa. Amene akufuna moyo wa pa dziko adanena (mokhumbira): “Kalanga ife! Tikadapatsidwa monga wapatsidwa Qaruna! Ndithu iye ngodala kwakukulu.” info
التفاسير:

external-link copy
80 : 28

وَقَالَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ وَيۡلَكُمۡ ثَوَابُ ٱللَّهِ خَيۡرٞ لِّمَنۡ ءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗاۚ وَلَا يُلَقَّىٰهَآ إِلَّا ٱلصَّٰبِرُونَ

Ndipo amene adapatsidwa kuzindikira adanena: “Tsoka lanu! Malipiro a Allah ngabwino kwa yemwe wakhulupirira ndi kuchita zabwino, (kuposa izi ali nazo Qaruni); ndipo sadzapatsidwa zimenezi koma okhawo ali opirira.” info
التفاسير:

external-link copy
81 : 28

فَخَسَفۡنَا بِهِۦ وَبِدَارِهِ ٱلۡأَرۡضَ فَمَا كَانَ لَهُۥ مِن فِئَةٖ يَنصُرُونَهُۥ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَمَا كَانَ مِنَ ٱلۡمُنتَصِرِينَ

Kenako tidamdidimiza m’nthaka iye ndi nyumba yake; ndipo adalibe gulu lililonse lomuthangata popikisana ndi Allah, ndipo sadali mwa odzipulumutsa okha. info
التفاسير:

external-link copy
82 : 28

وَأَصۡبَحَ ٱلَّذِينَ تَمَنَّوۡاْ مَكَانَهُۥ بِٱلۡأَمۡسِ يَقُولُونَ وَيۡكَأَنَّ ٱللَّهَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦ وَيَقۡدِرُۖ لَوۡلَآ أَن مَّنَّ ٱللَّهُ عَلَيۡنَا لَخَسَفَ بِنَاۖ وَيۡكَأَنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلۡكَٰفِرُونَ

Ndipo amene ankalakalaka ulemelero wake dzulo adayamba kunena: “E zoonadi Allah amamuonjezera chuma amene akumfuna mwa akapolo Ake (chingakhale ali oipa wosayanjidwa ndi Iye), ndipo amamuchepetsera chuma (amene wamfuna kotero ngakhale ali woyanjidwa ndi Iye.) Pakadapanda Allah kutimvera chisoni. (Mkukhumbira kwathu pa zimene adampatsa Qaruna akadatikwilira m’nthaka. Ha! Zoonadi osakhulupirira sangapambane.” info
التفاسير:

external-link copy
83 : 28

تِلۡكَ ٱلدَّارُ ٱلۡأٓخِرَةُ نَجۡعَلُهَا لِلَّذِينَ لَا يُرِيدُونَ عُلُوّٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا فَسَادٗاۚ وَٱلۡعَٰقِبَةُ لِلۡمُتَّقِينَ

Nyumba yomalizirayo tikawapangira amene sakufuna kudzikweza pa dziko ndi kuononga. Ndipo malekezero abwino adzakhala a wanthu owopa (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
84 : 28

مَن جَآءَ بِٱلۡحَسَنَةِ فَلَهُۥ خَيۡرٞ مِّنۡهَاۖ وَمَن جَآءَ بِٱلسَّيِّئَةِ فَلَا يُجۡزَى ٱلَّذِينَ عَمِلُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ إِلَّا مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Amene achite chabwino, adzapeza mphoto yoposa chimene adachitacho ndipo amene achite choipa sadzalipidwa (china chake) koma zoipa zomwezo zimene adali kuzichita. info
التفاسير: