ශුද්ධවූ අල් කුර්ආන් අර්ථ කථනය - චිචේවා පරිවර්තනය - කාලිද් ඉබ්රාහීම් බීතාලා

පිටු අංක:close

external-link copy
164 : 7

وَإِذۡ قَالَتۡ أُمَّةٞ مِّنۡهُمۡ لِمَ تَعِظُونَ قَوۡمًا ٱللَّهُ مُهۡلِكُهُمۡ أَوۡ مُعَذِّبُهُمۡ عَذَابٗا شَدِيدٗاۖ قَالُواْ مَعۡذِرَةً إِلَىٰ رَبِّكُمۡ وَلَعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ

Ndipo (akumbutse ) pamene gulu lina mwa iwo linkanena (kwa omwe amachenjeza amene adaswa kupatulika kwa tsiku la Sabata pamene adati): “Pali phindu lanji kuwachenjeza anthu omwe Allah awawononga kapena kuwalanga ndi chilango chaukali pompano pa dziko lapansi)? (Iwo) adati: “Kuti tidzakhale ndi chidandaulo kwa Mbuye wathu (ponena kuti tidawachenjeza koma sadatimvere) ndi kutinso mwina angaope (Allah nasiya kuswa lamulo Lake).” info
التفاسير:

external-link copy
165 : 7

فَلَمَّا نَسُواْ مَا ذُكِّرُواْ بِهِۦٓ أَنجَيۡنَا ٱلَّذِينَ يَنۡهَوۡنَ عَنِ ٱلسُّوٓءِ وَأَخَذۡنَا ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ بِعَذَابِۭ بَـِٔيسِۭ بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ

Choncho, pamene sanalabadire zimene anauzidwa ndi kuchenjezedwa, tinawapulumutsa (anthu) omwe amaletsa zoipa, ndipo tidawakhaulitsa amene ankadzichitira okha zoipa ndi chilango choipa kwambiri chifukwa chakupandukila (kwawo) malamulo. info
التفاسير:

external-link copy
166 : 7

فَلَمَّا عَتَوۡاْ عَن مَّا نُهُواْ عَنۡهُ قُلۡنَا لَهُمۡ كُونُواْ قِرَدَةً خَٰسِـِٔينَ

Pamene anadzikweza pakusasiya zimene analetsedwazo tidawauza: “Khalani anyani, oyaluka (paliponse).” info
التفاسير:

external-link copy
167 : 7

وَإِذۡ تَأَذَّنَ رَبُّكَ لَيَبۡعَثَنَّ عَلَيۡهِمۡ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ مَن يَسُومُهُمۡ سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِۗ إِنَّ رَبَّكَ لَسَرِيعُ ٱلۡعِقَابِ وَإِنَّهُۥ لَغَفُورٞ رَّحِيمٞ

Ndipo (akumbutse) pamene Mbuye wako analengeza (kuti) ndithu adzawatumizira iwo (Ayuda) anthu mpaka tsiku la Qiyâma, omwe adzawazunza ndi mazunzo oipa. Ndithu Mbuye wako ngofulumira kulanga, ndipo ndithu palibe chikaiko, Iye Ngokhululuka kwambiri, Ngwachifundo chambiri. info
التفاسير:

external-link copy
168 : 7

وَقَطَّعۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ أُمَمٗاۖ مِّنۡهُمُ ٱلصَّٰلِحُونَ وَمِنۡهُمۡ دُونَ ذَٰلِكَۖ وَبَلَوۡنَٰهُم بِٱلۡحَسَنَٰتِ وَٱلسَّيِّـَٔاتِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ

Ndipo tidawalekanitsa pakati pawo (Ayuda), ndi kuwabalalitsa pa dziko lonse kukhala mafuko osiyanasiyana. Ena mwa iwo abwino (olungama) ndipo ena sali choncho (oipa). Tinawayesa mayeso a zabwino ndi zoipa kuti abwelere (koma ayi, sanabwelere). info
التفاسير:

external-link copy
169 : 7

فَخَلَفَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ خَلۡفٞ وَرِثُواْ ٱلۡكِتَٰبَ يَأۡخُذُونَ عَرَضَ هَٰذَا ٱلۡأَدۡنَىٰ وَيَقُولُونَ سَيُغۡفَرُ لَنَا وَإِن يَأۡتِهِمۡ عَرَضٞ مِّثۡلُهُۥ يَأۡخُذُوهُۚ أَلَمۡ يُؤۡخَذۡ عَلَيۡهِم مِّيثَٰقُ ٱلۡكِتَٰبِ أَن لَّا يَقُولُواْ عَلَى ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡحَقَّ وَدَرَسُواْ مَا فِيهِۗ وَٱلدَّارُ ٱلۡأٓخِرَةُ خَيۡرٞ لِّلَّذِينَ يَتَّقُونَۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ

Choncho, anawatsatira pambuyo (anthu abwinowo), otsatira atsopano omwe analandira buku (la Allah nalowa mmalo mwa iwo koma popanda kulitsata ndi kulilingalira). Ankatenga zinthu zoletsedwa za pa dziko lapansi uku akunena: “Tidzakhululukidwa, (Allah adzatikhululukira).” Ngati zina zonga izo zitawapeza, amazitenganso. Kodi silidatengedwe pangano kwa iwo la m’buku kuti sadzamunenera Allah bodza koma zoona zokhazokha? (Nanga akuneneranji kuti Allah adzawakhululukira pomwe akupitiriza machimo)? Pomwe iwo aphunzira zomwe zili mmenemo. Komatu nyumba ya chimaliziro idzawakhalira bwino amene akuopa (Allah). Nanga bwanji simukuzindikira? info
التفاسير:

external-link copy
170 : 7

وَٱلَّذِينَ يُمَسِّكُونَ بِٱلۡكِتَٰبِ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ إِنَّا لَا نُضِيعُ أَجۡرَ ٱلۡمُصۡلِحِينَ

Ndipo amene akugwirisitsa buku (la Allah potsata zophunzitsa zake) ndi kumapemphera Swala, (tidzawalipira zabwino). Ndithu Ife sitipititsa pachabe malipiro a ochita zabwino. info
التفاسير: