ශුද්ධවූ අල් කුර්ආන් අර්ථ කථනය - චිචේවා පරිවර්තනය - කාලිද් ඉබ්රාහීම් බීතාලා

පිටු අංක:close

external-link copy
50 : 40

قَالُوٓاْ أَوَلَمۡ تَكُ تَأۡتِيكُمۡ رُسُلُكُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِۖ قَالُواْ بَلَىٰۚ قَالُواْ فَٱدۡعُواْۗ وَمَا دُعَٰٓؤُاْ ٱلۡكَٰفِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَٰلٍ

(Alonda aja) adzati: “Kodi sadakudzereni aneneri anu ndi umboni oonekera poyera?” Iwo adzati: “Inde, (adatidzera. Koma ife tidanyoza).” (Ndipo) adzawauza: “Choncho pemphani nokha. Koma pempho la okanira silili la kanthu, ndi lotaika basi.” info
التفاسير:

external-link copy
51 : 40

إِنَّا لَنَنصُرُ رُسُلَنَا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَيَوۡمَ يَقُومُ ٱلۡأَشۡهَٰدُ

Ndithu Ife timapulumutsa aneneri Athu ndi amene akhulupirira pa moyo wa dziko lapansi ndi tsiku limene zidzaimilira mboni (kupereka umboni). info
التفاسير:

external-link copy
52 : 40

يَوۡمَ لَا يَنفَعُ ٱلظَّٰلِمِينَ مَعۡذِرَتُهُمۡۖ وَلَهُمُ ٱللَّعۡنَةُ وَلَهُمۡ سُوٓءُ ٱلدَّارِ

Tsiku limene achinyengo sadzawathandiza madandaulo awo, ndipo matembelero adzakhala pa iwo, ndipo pokhala pawo padzakhala poipa kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
53 : 40

وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡهُدَىٰ وَأَوۡرَثۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱلۡكِتَٰبَ

Ndithu Mûsa tidampatsa chiongoko, ndipo tidawasiira buku ana a Israyeli. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 40

هُدٗى وَذِكۡرَىٰ لِأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ

(Lomwe lidali) chiongoko ndi chikumbutso kwa eni nzeru. info
التفاسير:

external-link copy
55 : 40

فَٱصۡبِرۡ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لِذَنۢبِكَ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ بِٱلۡعَشِيِّ وَٱلۡإِبۡكَٰرِ

Choncho pirira, ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Ndipo pempha chikhululuko cha machimo ako (ukachimwa), ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda madzulo ndi m’mawa. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 40

إِنَّ ٱلَّذِينَ يُجَٰدِلُونَ فِيٓ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ بِغَيۡرِ سُلۡطَٰنٍ أَتَىٰهُمۡ إِن فِي صُدُورِهِمۡ إِلَّا كِبۡرٞ مَّا هُم بِبَٰلِغِيهِۚ فَٱسۡتَعِذۡ بِٱللَّهِۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ

Ndithu amene akutsutsana pa zisonyezo za Allah popanda umboni umene udawadzera, mmitima mwawo mulibe chilichonse koma kudzitukumula (ndikufuna ukulu), koma saufikira. Dzitchinjirize mwa Allah, ndithu Iye Ngwakumva, Ngopenya. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 40

لَخَلۡقُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ أَكۡبَرُ مِنۡ خَلۡقِ ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ

Ndithu kulenga kwa thambo ndi nthaka nkwakukulu kuposa kulenga kwa anthu. Koma anthu ambiri sakudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
58 : 40

وَمَا يَسۡتَوِي ٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡبَصِيرُ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَلَا ٱلۡمُسِيٓءُۚ قَلِيلٗا مَّا تَتَذَكَّرُونَ

Ndipo sali wolingana wakhungu ndi wopenya ndiponso amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndi wochita zoipa. Zimene inu mukumbukira nzochepa, ndithu! info
التفاسير: