ශුද්ධවූ අල් කුර්ආන් අර්ථ කථනය - චිචේවා පරිවර්තනය - කාලිද් ඉබ්රාහීම් බීතාලා

Al-Mu’minûn

external-link copy
1 : 23

قَدۡ أَفۡلَحَ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ

۞ Ndithu apambana okhulupirira (mwa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 23

ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي صَلَاتِهِمۡ خَٰشِعُونَ

Amene amakhudzumuka pa mapemphero awo (poipereka mitima yawo kwa Allah modzichepetsa). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 23

وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَنِ ٱللَّغۡوِ مُعۡرِضُونَ

Ndi omwe amapewa zinthu zopanda pake (zachabe). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 23

وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِلزَّكَوٰةِ فَٰعِلُونَ

Ndi omwe amakwaniritsa (nsanamira ya) chopereka (Zakaat). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 23

وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِفُرُوجِهِمۡ حَٰفِظُونَ

Ndi omwe amasunga umaliseche wawo. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 23

إِلَّا عَلَىٰٓ أَزۡوَٰجِهِمۡ أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُمۡ فَإِنَّهُمۡ غَيۡرُ مَلُومِينَ

Kupatula kwa akazi awo ndi adzakazi omwe manja awo akumanja apeza. Choncho iwo (pakukumana ndi amenewo) saali odzudzulidwa. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 23

فَمَنِ ٱبۡتَغَىٰ وَرَآءَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡعَادُونَ

Koma omwe angafune zosemphana ndi izi (kulumikizana ndi mkazi posiya njira ziwirizi) iwowo ndiwo opyola malire (a Allah). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 23

وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِأَمَٰنَٰتِهِمۡ وَعَهۡدِهِمۡ رَٰعُونَ

Ndi amene amasunga malonjezo awo ndi zomwe akhulupirika nazo. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 23

وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَوَٰتِهِمۡ يُحَافِظُونَ

Ndi omwe akusunga mapemphero awo (popemphera mu nthawi zake ndi kutsata malamulo ake uku ali odzichepetsa). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 23

أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡوَٰرِثُونَ

Iwo ndi olandira (zabwino tsiku la Qiyâma). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 23

ٱلَّذِينَ يَرِثُونَ ٱلۡفِرۡدَوۡسَ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Amene adzalandira Munda wamtendere (wotchedwa) Fir’dausi (Munda wapamwamba kwambiri). M’menemo iwo adzakhala nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 23

وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن سُلَٰلَةٖ مِّن طِينٖ

Ndipo ndithu tidamlenga munthu kuchokera ku dongo labwino. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 23

ثُمَّ جَعَلۡنَٰهُ نُطۡفَةٗ فِي قَرَارٖ مَّكِينٖ

Kenako tidalenga ana ake ndi dontho lamadzi (ambewu ya munthu) lomwe lidaikidwa pamalo osungidwa. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 23

ثُمَّ خَلَقۡنَا ٱلنُّطۡفَةَ عَلَقَةٗ فَخَلَقۡنَا ٱلۡعَلَقَةَ مُضۡغَةٗ فَخَلَقۡنَا ٱلۡمُضۡغَةَ عِظَٰمٗا فَكَسَوۡنَا ٱلۡعِظَٰمَ لَحۡمٗا ثُمَّ أَنشَأۡنَٰهُ خَلۡقًا ءَاخَرَۚ فَتَبَارَكَ ٱللَّهُ أَحۡسَنُ ٱلۡخَٰلِقِينَ

Kenako tidalisintha dontholo kukhala magazi oundana; ndipo kenako magaziwo tidawasintha kukhala m’nofu; ndipo kenako m’nofu tidausintha kukhala mafupa; ndipo mafupawo tidawaveka minofu, kenako tidamsintha kukhala cholengedwa china. Choncho watukuka Allah, Wabwino polenga. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 23

ثُمَّ إِنَّكُم بَعۡدَ ذَٰلِكَ لَمَيِّتُونَ

Kenako ndithu inu pambuyo pa zimenezo mudzamwalira. info
التفاسير:

external-link copy
16 : 23

ثُمَّ إِنَّكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ تُبۡعَثُونَ

Ndithu inu, kenako mudzaukitsidwa pa tsiku la Qiyâma. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 23

وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا فَوۡقَكُمۡ سَبۡعَ طَرَآئِقَ وَمَا كُنَّا عَنِ ٱلۡخَلۡقِ غَٰفِلِينَ

Ndipo ndithu tapanga njira zisanu ndi ziwiri (mitambo) pamwamba panu, ndipo ndithu (Ife) sitisiya kulabadira zolengedwa. info
التفاسير: