ශුද්ධවූ අල් කුර්ආන් අර්ථ කථනය - චිචේවා පරිවර්තනය - කාලිද් ඉබ්රාහීම් බීතාලා

පිටු අංක:close

external-link copy
30 : 2

وَإِذۡ قَالَ رَبُّكَ لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنِّي جَاعِلٞ فِي ٱلۡأَرۡضِ خَلِيفَةٗۖ قَالُوٓاْ أَتَجۡعَلُ فِيهَا مَن يُفۡسِدُ فِيهَا وَيَسۡفِكُ ٱلدِّمَآءَ وَنَحۡنُ نُسَبِّحُ بِحَمۡدِكَ وَنُقَدِّسُ لَكَۖ قَالَ إِنِّيٓ أَعۡلَمُ مَا لَا تَعۡلَمُونَ

Akumbutse (anthu ako nkhani iyi) panthawi yomwe Mbuye wako anati kwa Angelo: “Ine ndikufuna kuika m’dziko lapansi wondiimilira.” (Angelo) adati: “Kodi muika m’menemo amene azidzaonongamo ndi kukhetsa mwazi, pomwe ife tikukulemekezani ndi kukutamandani mokuyeretsani?” (Allah) adati: “Ndithudi, Ine ndikudziwa zimene simukuzidziwa.” info
التفاسير:

external-link copy
31 : 2

وَعَلَّمَ ءَادَمَ ٱلۡأَسۡمَآءَ كُلَّهَا ثُمَّ عَرَضَهُمۡ عَلَى ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ فَقَالَ أَنۢبِـُٔونِي بِأَسۡمَآءِ هَٰٓؤُلَآءِ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Ndipo (Allah) adaphunzitsa Adam mayina a (zinthu) zonse; nazibweretsa (zinthuzo) pamaso pa Angelo, naati (kwa Angelo): “Ndiuzeni mayina a zinthu izi ngati mukunena zoona (kuti inu ndinu ozindikira zinthu).” info
التفاسير:

external-link copy
32 : 2

قَالُواْ سُبۡحَٰنَكَ لَا عِلۡمَ لَنَآ إِلَّا مَا عَلَّمۡتَنَآۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَلِيمُ ٱلۡحَكِيمُ

(Angelo) adati: “Kuyeretsedwa Nkwanu! Ife tilibe kuzindikira kupatula chimene mwatiphunzitsa. Ndithudi, Inu Ngodziwa kwambiri, Anzeru zakuya.” info
التفاسير:

external-link copy
33 : 2

قَالَ يَٰٓـَٔادَمُ أَنۢبِئۡهُم بِأَسۡمَآئِهِمۡۖ فَلَمَّآ أَنۢبَأَهُم بِأَسۡمَآئِهِمۡ قَالَ أَلَمۡ أَقُل لَّكُمۡ إِنِّيٓ أَعۡلَمُ غَيۡبَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَأَعۡلَمُ مَا تُبۡدُونَ وَمَا كُنتُمۡ تَكۡتُمُونَ

(Allah) adanena: “E iwe Adam!: Auze mayina ake (azinthuzo).” Ndipo pamene adawauza mayina ake, (Iye) adati: “Kodi Sindinakuuzeni kuti Ine ndikudziwa zobisika zakumwamba ndi pansi, ndiponso ndikudziwa zimene mukuonetsera poyera ndi zimene mukubisa?” info
التفاسير:

external-link copy
34 : 2

وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ أَبَىٰ وَٱسۡتَكۡبَرَ وَكَانَ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ

Ndipo (akumbutse anthu ako nkhani iyi) parnene tidawauza Angelo: “Mgwadireni Adam.” Onse adamugwadira kupatula Iblisi (Satana); anakana nadzitukumula. Tero adali m’modzi mwa osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 2

وَقُلۡنَا يَٰٓـَٔادَمُ ٱسۡكُنۡ أَنتَ وَزَوۡجُكَ ٱلۡجَنَّةَ وَكُلَا مِنۡهَا رَغَدًا حَيۡثُ شِئۡتُمَا وَلَا تَقۡرَبَا هَٰذِهِ ٱلشَّجَرَةَ فَتَكُونَا مِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo tidati: “E iwe Adam! Khala iwe ndi mkazi wako m’mundamo (mu Edeni); idyani m’menemo motakasuka paliponse pamene mwafuna; koma musauyandikire Mtengo uwu kuopera kuti mungakhale mwa odzichitira okha zoipa.” info
التفاسير:

external-link copy
36 : 2

فَأَزَلَّهُمَا ٱلشَّيۡطَٰنُ عَنۡهَا فَأَخۡرَجَهُمَا مِمَّا كَانَا فِيهِۖ وَقُلۡنَا ٱهۡبِطُواْ بَعۡضُكُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوّٞۖ وَلَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُسۡتَقَرّٞ وَمَتَٰعٌ إِلَىٰ حِينٖ

Koma Satana (Iblisi yemwe uja) adawalakwitsa onse awiriwo (nanyoza lamulo la Allah ndikudya mtengo woletsedwawo), nawatulutsa (mu Mtendere) momwe adaalimo. Ndipo tidawauza: “Tsikani (mukakhale pa dziko lapansi) pakati panu pali chidani. Tsopano pokhala panu ndi pa dziko lapansi, ndipo mukapeza chisangalalo pamenepo kwakanthawi.” info
التفاسير:

external-link copy
37 : 2

فَتَلَقَّىٰٓ ءَادَمُ مِن رَّبِّهِۦ كَلِمَٰتٖ فَتَابَ عَلَيۡهِۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلتَّوَّابُ ٱلرَّحِيمُ

Ndipo Adam adalandira mawu kuchokera kwa Mbuye wake, (napempha chikhululuko cha Allah kupyolera m’mawuwo), ndipo (Mbuye wake) adavomera kulapa kwake. Ndithudi, Iyeyo Ngolandira kwambiri kulapa, Wachisoni chosatha. info
التفاسير: