Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala.

external-link copy
64 : 7

فَكَذَّبُوهُ فَأَنجَيۡنَٰهُ وَٱلَّذِينَ مَعَهُۥ فِي ٱلۡفُلۡكِ وَأَغۡرَقۡنَا ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَآۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمًا عَمِينَ

Koma adamtsutsa. Choncho, tidampulumutsa iye ndi amene adali naye pamodzi m’chombo. Ndipo tidawamiza aja adatsutsa zizindikiro Zathu. Ndithudi, iwo adali anthu akhungu.[187] info

[187] Nkhani ya Mneneri Nuh paliponse akuifotokoza motalikitsa. Koma m’sura iyi aifotokoza mwachidule. Ndipo Nuh ndimneneri wakale kwabasi. Iye adali kuwalalikira anthu a ku Iraq. Ndipo m’nthawi imeneyo pafupifupi dziko lonse lapansi chitukuko chidali ku Iraq monga momwe tikuwerengera m’mabuku ambiri yakale.

التفاسير: