Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala.

Al-Hâqqah

external-link copy
1 : 69

ٱلۡحَآقَّةُ

Chakudza cha choonadi (chomwe ndi Qiyâma). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 69

مَا ٱلۡحَآقَّةُ

Kodi chakudza cha choonadi nchiyani? info
التفاسير:

external-link copy
3 : 69

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡحَآقَّةُ

Nanga nchiyani chikudziwitse za chakudza cha choonadicho? info
التفاسير:

external-link copy
4 : 69

كَذَّبَتۡ ثَمُودُ وَعَادُۢ بِٱلۡقَارِعَةِ

Asamudu ndi Âdi adatsutsa zakudza kwa Qiyâma (yomwe idzadzidzimutsa zolengedwa mwamphamvu ndi zoopsa zake). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 69

فَأَمَّا ثَمُودُ فَأُهۡلِكُواْ بِٱلطَّاغِيَةِ

Tsono Asamudu adaonongedwa ndi phokoso lopyola muyeso, (lamphamvu kwambiri). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 69

وَأَمَّا عَادٞ فَأُهۡلِكُواْ بِرِيحٖ صَرۡصَرٍ عَاتِيَةٖ

Ndipo Âdi adaonongedwa ndi chimphepo cha mkuntho, chozizira, champhamvu kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 69

سَخَّرَهَا عَلَيۡهِمۡ سَبۡعَ لَيَالٖ وَثَمَٰنِيَةَ أَيَّامٍ حُسُومٗاۖ فَتَرَى ٱلۡقَوۡمَ فِيهَا صَرۡعَىٰ كَأَنَّهُمۡ أَعۡجَازُ نَخۡلٍ خَاوِيَةٖ

Allah adachitumiza kwa iwo pa usiku usanu ndi uwiri ndi masana asanu ndi atatu mosadukiza; kotero ukadawaona ali lambalamba mmenemo ngati mathunthu a mitengo ya kanjedza yopanda kanthu m’kati mwake. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 69

فَهَلۡ تَرَىٰ لَهُم مِّنۢ بَاقِيَةٖ

Kodi nanga ukumuona wotsala mwa iwo? info
التفاسير:

external-link copy
9 : 69

وَجَآءَ فِرۡعَوۡنُ وَمَن قَبۡلَهُۥ وَٱلۡمُؤۡتَفِكَٰتُ بِٱلۡخَاطِئَةِ

Ndipo Firiaun ndi amene adalipo iye asadabadwe, ndi khamu la anthu amidzi yotembenuzidwa (anthu a Luti) adadza ndi machimo (akulu). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 69

فَعَصَوۡاْ رَسُولَ رَبِّهِمۡ فَأَخَذَهُمۡ أَخۡذَةٗ رَّابِيَةً

Ndipo (yense wa iwowa) adanyoza Mtumiki wa Mbuye wawo; choncho adawalanga chilango chopitilira muyeso. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 69

إِنَّا لَمَّا طَغَا ٱلۡمَآءُ حَمَلۡنَٰكُمۡ فِي ٱلۡجَارِيَةِ

Ndithu pamene madzi adasefukira mopyola muyeso (mpaka kumeza mapiri nthawi ya chigumula cha Nowa) Ife tidakukwezani mchombo choyandama ndi kuyenda. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 69

لِنَجۡعَلَهَا لَكُمۡ تَذۡكِرَةٗ وَتَعِيَهَآ أُذُنٞ وَٰعِيَةٞ

Kuti tichichite (chochitikacho chomwe okhulupirira adapulumuka nacho; osakhulupirira adaonongeka nacho) kukhala lingaliro ndi phunziro kwa inu, ndikuti lisunge (nkhaniyi) khutu losunga. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 69

فَإِذَا نُفِخَ فِي ٱلصُّورِ نَفۡخَةٞ وَٰحِدَةٞ

Choncho likadzaimbidwa lipenga, kuimba kumodzi kokha (zamoyo zonse zidzafa). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 69

وَحُمِلَتِ ٱلۡأَرۡضُ وَٱلۡجِبَالُ فَدُكَّتَا دَكَّةٗ وَٰحِدَةٗ

Ndipo nthaka ndi mapiri nkuchotsedwa m’malo mwake ndi kuphwanyidwa kamodzi nkamodzi. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 69

فَيَوۡمَئِذٖ وَقَعَتِ ٱلۡوَاقِعَةُ

Chomwecho tsiku limenelo, chochitika chidzachitika (imene ili Qiyâma). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 69

وَٱنشَقَّتِ ٱلسَّمَآءُ فَهِيَ يَوۡمَئِذٖ وَاهِيَةٞ

Ndipo thambo lidzasweka choncho ilo tsiku limenelo lidzakhala lofooka (pamene lidali lolimba). info
التفاسير:

external-link copy
17 : 69

وَٱلۡمَلَكُ عَلَىٰٓ أَرۡجَآئِهَاۚ وَيَحۡمِلُ عَرۡشَ رَبِّكَ فَوۡقَهُمۡ يَوۡمَئِذٖ ثَمَٰنِيَةٞ

Ndipo angelo adzakhala m’mphepete mwake, ndipo pamwamba pawo tsiku limenero (angelo) asanu ndi atatu adzasenza Arsh (Mpando wachifumu) ya Mbuye wako. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 69

يَوۡمَئِذٖ تُعۡرَضُونَ لَا تَخۡفَىٰ مِنكُمۡ خَافِيَةٞ

Tsiku limenelo mudzabweretsedwa ku chiweruzo; sichidzabisika chilichonse chobisika mwa inu. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 69

فَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ فَيَقُولُ هَآؤُمُ ٱقۡرَءُواْ كِتَٰبِيَهۡ

Tsono amene adzapatsidwa kaundula wake chakudzanja lakumanja kwake adzanena (mokondwa kwa amene ali m’phepete mwake): “Tengani! Werengani kaundula wanga!” info
التفاسير:

external-link copy
20 : 69

إِنِّي ظَنَنتُ أَنِّي مُلَٰقٍ حِسَابِيَهۡ

“Ndithudi ine ndidatsimikiza (pa dziko lapansi) kuti ndidzakumana ndi chiwerengero changa.” info
التفاسير:

external-link copy
21 : 69

فَهُوَ فِي عِيشَةٖ رَّاضِيَةٖ

Choncho, iye adzakhala m’moyo wosangalatsa. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 69

فِي جَنَّةٍ عَالِيَةٖ

M’munda wapamwamba. info
التفاسير:

external-link copy
23 : 69

قُطُوفُهَا دَانِيَةٞ

Zipatso zake zoyandikira pansi (zosavuta kuzithyola). info
التفاسير:

external-link copy
24 : 69

كُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ هَنِيٓـَٔۢا بِمَآ أَسۡلَفۡتُمۡ فِي ٱلۡأَيَّامِ ٱلۡخَالِيَةِ

(Adzawauza kuti:) “Idyani, ndipo imwani mosangalala pa zimene mudatsogoza mmasiku aja adapita (a pa dziko lapansi).” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 69

وَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِشِمَالِهِۦ فَيَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي لَمۡ أُوتَ كِتَٰبِيَهۡ

Ndipo amene adzapatsidwe kaundula wake kudzanja lake lamanzere, adzanena (modandaula): “Kalanga ine! Ndiponi ndikadapanda kupatsidwa kaundula wangayu!” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 69

وَلَمۡ أَدۡرِ مَا حِسَابِيَهۡ

“Nkusadziwa chiwerengero changa!” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 69

يَٰلَيۡتَهَا كَانَتِ ٱلۡقَاضِيَةَ

“Ha! imfa ija ikadandimaliziratu (ndi kundilekanitsa ine ndi zimenezi).” info
التفاسير:

external-link copy
28 : 69

مَآ أَغۡنَىٰ عَنِّي مَالِيَهۡۜ

“Chuma changa sichidandithandize!” info
التفاسير:

external-link copy
29 : 69

هَلَكَ عَنِّي سُلۡطَٰنِيَهۡ

“Mphamvu zanga (ndi moyo wanga wathanzi) zandichokera!” info
التفاسير:

external-link copy
30 : 69

خُذُوهُ فَغُلُّوهُ

(Kudzanenedwa kwa angelo oyang’anira Jahena): Mgwireni ndipo mnjateni (pomphatikiza manja ndi khosi)! info
التفاسير:

external-link copy
31 : 69

ثُمَّ ٱلۡجَحِيمَ صَلُّوهُ

Kenako mponyeni ku Moto. info
التفاسير:

external-link copy
32 : 69

ثُمَّ فِي سِلۡسِلَةٖ ذَرۡعُهَا سَبۡعُونَ ذِرَاعٗا فَٱسۡلُكُوهُ

Kenakonso mulowetseni mtcheni lotalika mikwamba makumi asanu ndi awiri! info
التفاسير:

external-link copy
33 : 69

إِنَّهُۥ كَانَ لَا يُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ ٱلۡعَظِيمِ

Ndithudi, iye sadali kukhulupirira mwa Allah wamkulu. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 69

وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ

Sadalinso kulimbikitsa zodyetsa osauka. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 69

فَلَيۡسَ لَهُ ٱلۡيَوۡمَ هَٰهُنَا حَمِيمٞ

Basi, lero kuno alibe bwenzi (lomthandiza). info
التفاسير:

external-link copy
36 : 69

وَلَا طَعَامٌ إِلَّا مِنۡ غِسۡلِينٖ

Ngakhale chakudya kupatula mafinya (a anthu a ku Moto). info
التفاسير:

external-link copy
37 : 69

لَّا يَأۡكُلُهُۥٓ إِلَّا ٱلۡخَٰطِـُٔونَ

Zomwe palibe angazidye kupatula ochimwa (mwadala). info
التفاسير:

external-link copy
38 : 69

فَلَآ أُقۡسِمُ بِمَا تُبۡصِرُونَ

Choncho ndikulumbilira zimene mukuziona. info
التفاسير:

external-link copy
39 : 69

وَمَا لَا تُبۡصِرُونَ

Ndi zimene simukuziona. info
التفاسير:

external-link copy
40 : 69

إِنَّهُۥ لَقَوۡلُ رَسُولٖ كَرِيمٖ

Ndithudi iyi (Qur’an) ndiliwu la mthenga wolemekezeka (Jibril). info
التفاسير:

external-link copy
41 : 69

وَمَا هُوَ بِقَوۡلِ شَاعِرٖۚ قَلِيلٗا مَّا تُؤۡمِنُونَ

Ndipo simawu a mlakatuli, ndi zochepa zimene mukuzikhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
42 : 69

وَلَا بِقَوۡلِ كَاهِنٖۚ قَلِيلٗا مَّا تَذَكَّرُونَ

Ndiponso simawu a mlosi, ndizochepa zimene mmakumbukira! info
التفاسير:

external-link copy
43 : 69

تَنزِيلٞ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

(Ichi ndi) chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa. info
التفاسير:

external-link copy
44 : 69

وَلَوۡ تَقَوَّلَ عَلَيۡنَا بَعۡضَ ٱلۡأَقَاوِيلِ

Ndipo (Mneneri) akadatipekera bodza linalake. info
التفاسير:

external-link copy
45 : 69

لَأَخَذۡنَا مِنۡهُ بِٱلۡيَمِينِ

Tikadamgwira (mwamphamvu) ndimkono wamanja. info
التفاسير:

external-link copy
46 : 69

ثُمَّ لَقَطَعۡنَا مِنۡهُ ٱلۡوَتِينَ

Ndipo tikadadula mwa iye mtsempha wa moyo (kotero kuti ndikuferatu nthawi yomweyo). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 69

فَمَا مِنكُم مِّنۡ أَحَدٍ عَنۡهُ حَٰجِزِينَ

Sipakadapezeka aliyense mwa inu womteteza (kuchilango Chathu). info
التفاسير:

external-link copy
48 : 69

وَإِنَّهُۥ لَتَذۡكِرَةٞ لِّلۡمُتَّقِينَ

Ndithu iyi (Qur’an) ndi phunziro labwino kwa owopa (Allah.) info
التفاسير:

external-link copy
49 : 69

وَإِنَّا لَنَعۡلَمُ أَنَّ مِنكُم مُّكَذِّبِينَ

Ndithu Ife, tikudziwa kuti ena mwa inu ndiotsutsa (Qur’an). info
التفاسير:

external-link copy
50 : 69

وَإِنَّهُۥ لَحَسۡرَةٌ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ

Ndipo ndithu iyi (Qur’an) idzakhala chowadandaulitsa (chachikulu) osakhulupirira (pamene adzaona chilango chawo ndi mtendere wa okhulupirira). info
التفاسير:

external-link copy
51 : 69

وَإِنَّهُۥ لَحَقُّ ٱلۡيَقِينِ

Ndithu iyoyi ndichoonadi Chotsimikizika; (mulibe chikaiko), info
التفاسير:

external-link copy
52 : 69

فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ

Basi, lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu (pitiriza kutamanda dzina Lake). info
التفاسير: