Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala.

external-link copy
96 : 6

فَالِقُ ٱلۡإِصۡبَاحِ وَجَعَلَ ٱلَّيۡلَ سَكَنٗا وَٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ حُسۡبَانٗاۚ ذَٰلِكَ تَقۡدِيرُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ

Iye ndi Yemwe ali Wotsekula m’bandakucha, ndipo amaupanga usiku kukhala wabata (nthawi yopumula) ndi dzuwa ndi mwezi kukhala zowerengera masiku ndi zaka (kalendala). Ichi nchikonzero cha Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri. info
التفاسير: