Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala.

external-link copy
5 : 41

وَقَالُواْ قُلُوبُنَا فِيٓ أَكِنَّةٖ مِّمَّا تَدۡعُونَآ إِلَيۡهِ وَفِيٓ ءَاذَانِنَا وَقۡرٞ وَمِنۢ بَيۡنِنَا وَبَيۡنِكَ حِجَابٞ فَٱعۡمَلۡ إِنَّنَا عَٰمِلُونَ

Ndipo akunena (kuti): “Mitima yathu (yaphimbidwa) m’zivindikiro, ku zomwe ukutiitanirazo, ndipo m’makutu mwathu muli kulemera kwa ugonthi; choncho pakati pathu ndi pakati pa iwe pali chotsekereza (chotchinga); tero chita (zakozo); nafe tichita (zathu; aliyense wa ife asalowelere za mnzake).” info
التفاسير: