Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala.

numero y'urupapuro:close

external-link copy
52 : 37

يَقُولُ أَءِنَّكَ لَمِنَ ٱلۡمُصَدِّقِينَ

Yemwe amandiuza: “Kodi iwe ndiwe mmodzi wa ovomereza?” info
التفاسير:

external-link copy
53 : 37

أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَدِينُونَ

“Zakuti tikadzafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, (tidzaukanso) ndi kulandira malipiro (pa zochita zathu)?” info
التفاسير:

external-link copy
54 : 37

قَالَ هَلۡ أَنتُم مُّطَّلِعُونَ

(Wokhulupirira) adzanena (kwa anzake: “Inu anthu a kumtendere) kodi simungasuzumire (nane ku moto kuti timuone)?” info
التفاسير:

external-link copy
55 : 37

فَٱطَّلَعَ فَرَءَاهُ فِي سَوَآءِ ٱلۡجَحِيمِ

Choncho adzayang’ana ndipo adzamuona ali mkatikati mwa moto. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 37

قَالَ تَٱللَّهِ إِن كِدتَّ لَتُرۡدِينِ

Adzanena: “Ndikulumbilira Allah! Udatsala pang’ono kuti undiononge (ndikadakuvomera paja pa dziko lapansi).” info
التفاسير:

external-link copy
57 : 37

وَلَوۡلَا نِعۡمَةُ رَبِّي لَكُنتُ مِنَ ٱلۡمُحۡضَرِينَ

“Ndipo pakadapanda chisomo cha Mbuye wanga, ndikadakhala mmodzi mwa opezeka ku Moto.” info
التفاسير:

external-link copy
58 : 37

أَفَمَا نَحۡنُ بِمَيِّتِينَ

“Kodi zili choncho kuti sitidzafanso (tizingosangalala m’Munda wamtendere).” info
التفاسير:

external-link copy
59 : 37

إِلَّا مَوۡتَتَنَا ٱلۡأُولَىٰ وَمَا نَحۡنُ بِمُعَذَّبِينَ

“Kupatula imfa yathu yoyamba ija, ndi kutinso ife sitilangidwa?” info
التفاسير:

external-link copy
60 : 37

إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ

Ndithu izi (zimene Allah waika m’Munda wamtendere) ndiko kupambana kwakukulu. info
التفاسير:

external-link copy
61 : 37

لِمِثۡلِ هَٰذَا فَلۡيَعۡمَلِ ٱلۡعَٰمِلُونَ

(Pofuna kupeza) zonga zimenezi ogwira ntchito agwire. info
التفاسير:

external-link copy
62 : 37

أَذَٰلِكَ خَيۡرٞ نُّزُلًا أَمۡ شَجَرَةُ ٱلزَّقُّومِ

Kodi zimenezo ndilo phwando labwino kapena mtengo wa Zaqqum (wowawa kwambiri womwe anthu a ku Moto azikadya)? info
التفاسير:

external-link copy
63 : 37

إِنَّا جَعَلۡنَٰهَا فِتۡنَةٗ لِّلظَّٰلِمِينَ

Ndithu Ife taupanga (mtengo umenewu) kukhala mayeso ndi chilango cha anthu ochimwa (podzichitira okha chinyengo ndi kupembedza mafano.) info
التفاسير:

external-link copy
64 : 37

إِنَّهَا شَجَرَةٞ تَخۡرُجُ فِيٓ أَصۡلِ ٱلۡجَحِيمِ

Umenewu ndimtengo omwe umatuluka pakatikati pa Jahannam (adaulenga kuchokera ku Moto). info
التفاسير:

external-link copy
65 : 37

طَلۡعُهَا كَأَنَّهُۥ رُءُوسُ ٱلشَّيَٰطِينِ

Zipatso zake (nzoipa) ngati mitu ya asatana. info
التفاسير:

external-link copy
66 : 37

فَإِنَّهُمۡ لَأٓكِلُونَ مِنۡهَا فَمَالِـُٔونَ مِنۡهَا ٱلۡبُطُونَ

Ndithu iwo akadya mtengowo ndi kudzaza mimba zawo ndi zipatso zake (pakuti sakapeza chakudya china kupatula zipatso za mtengowo). info
التفاسير:

external-link copy
67 : 37

ثُمَّ إِنَّ لَهُمۡ عَلَيۡهَا لَشَوۡبٗا مِّنۡ حَمِيمٖ

Kenako, ndithu kuwawa kwa mtengowo kosakanikirana ndi madzi owira kuzakhala pa iwo. info
التفاسير:

external-link copy
68 : 37

ثُمَّ إِنَّ مَرۡجِعَهُمۡ لَإِلَى ٱلۡجَحِيمِ

Kenako ndithu kobwerera kwawo ndi ku Jahannam. info
التفاسير:

external-link copy
69 : 37

إِنَّهُمۡ أَلۡفَوۡاْ ءَابَآءَهُمۡ ضَآلِّينَ

Ndithu iwo adapeza makolo awo ali osokera. info
التفاسير:

external-link copy
70 : 37

فَهُمۡ عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِمۡ يُهۡرَعُونَ

Ndipo iwonso adatsata mapazi awo mothamanga. info
التفاسير:

external-link copy
71 : 37

وَلَقَدۡ ضَلَّ قَبۡلَهُمۡ أَكۡثَرُ ٱلۡأَوَّلِينَ

Ndipo, ndithu akale ambiri adasokera patsogolo pawo. info
التفاسير:

external-link copy
72 : 37

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا فِيهِم مُّنذِرِينَ

Ndipo, ndithu tidatuma achenjezi kwa iwo. info
التفاسير:

external-link copy
73 : 37

فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُنذَرِينَ

Tapenya momwe adalili mapeto a omwe adachenjezedwa. info
التفاسير:

external-link copy
74 : 37

إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ

Kupatula akapolo a Allah, oyeretsedwa (iwo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere). info
التفاسير:

external-link copy
75 : 37

وَلَقَدۡ نَادَىٰنَا نُوحٞ فَلَنِعۡمَ ٱلۡمُجِيبُونَ

Ndithu Nuh adatiitana, (ndipo tidamuyankha mayankho abwino), taonani kukhala bwino Ife Oyankha. info
التفاسير:

external-link copy
76 : 37

وَنَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥ مِنَ ٱلۡكَرۡبِ ٱلۡعَظِيمِ

Ndipo tidampulumutsa iye ndi anthu ake ku vuto lalikulu. info
التفاسير: