Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala.

Al-Masad

external-link copy
1 : 111

تَبَّتۡ يَدَآ أَبِي لَهَبٖ وَتَبَّ

Aonongeka manja a Abi Lahab (omwe adali kuwagwiritsa ntchito pozunza Asilamu). Nayenso wawonongeka.[497] info

[497] (Ndime 1-4) Pa chiyambi cha uneneri wa Muhammad (s.a.w) adalamulidwa kuti aulalikire uthenga wabwinowo kwa abale ake apafupi; adawasonkhanitsa ndipo adawalalikira ndi kuwachenjeza za chilango cha tsiku lachimaliziro. Koma Abu Lahab adali m’bale watate wa Mtumiki Muhammad (s.a.w) adakwiya ndipo adanena kuti: “Waonongeka iwe! Waonongeka iwe! Chimenechi ndi chimene watisonkhanitsira?’’ Pa chifukwa ichi idavumbulutsidwa Sura imeneyi. Allah adamubwezera Abu Lahab pamodzi ndi mkazi wake, Ummu Jamil, mawu otembelera. Ummu Jamil ankalimbikira kwambiri kumuzunza Mtumiki (s.a.w) ndi kuwakaikitsa amuna kuti asamutsatire. Ndipo adayesetsa kutsekereza kuti asamutsatire. Ndipo adayesetsa kutsekereza kuti Chisilamu chisafalikire madera ena. “Aonongeka manja a Abu Lahab’’ kumeneku ndi kutembelera komutembelera Abu Lahab kuti aonongeke m’malo moonongeka Mneneri (s.a.w). Pakuti amene amatembelera apayu ndi Mwini Allah, ndiye kuti matembelero adamufikiradi iye.

التفاسير:

external-link copy
2 : 111

مَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُ مَالُهُۥ وَمَا كَسَبَ

Chuma chake ndi ulemelero wake (umene adaupeza) sizidamthandize ku chilango cha Allah. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 111

سَيَصۡلَىٰ نَارٗا ذَاتَ لَهَبٖ

Adzalowa ku Moto wa malawi. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 111

وَٱمۡرَأَتُهُۥ حَمَّالَةَ ٱلۡحَطَبِ

Nayenso mkazi wake (adzalowa ku Moto) yemwe adali kusenza nkhuni (za minga pomutchera Mtumiki (s.a.w) komanso amanka nadanitsa pakati pa anthu). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 111

فِي جِيدِهَا حَبۡلٞ مِّن مَّسَدِۭ

Mkhosi mwake mdzamangidwa chingwe chopiringidwa bwino cha mlaza (chomlanga nacho).[498] info

[498] Uyu mkazi wa Abu Lahab adali wodanitsa. Ntchito yake idali kutapa mawu uku, kuwapititsa uku, ncholinga chofuna kusokoneza.

التفاسير: