Ibisobanuro bya qoran ntagatifu - Ibisobanuro bya Qur'an Ntagatifu mu rurimi rw'igi Chewa - Khaled Ibrahim Betala.

external-link copy
58 : 11

وَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا نَجَّيۡنَا هُودٗا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةٖ مِّنَّا وَنَجَّيۡنَٰهُم مِّنۡ عَذَابٍ غَلِيظٖ

Ndipo pamene lamulo lathu lidafika (lakuwaononga), tidampulumutsa Hûd ndi amene adakhulupirira pamodzi naye, mwachifundo Chathu, ndipo tidawapulumutsa kuchilango chokhwima.[223] info

[223] Chilangocho chidali chimphepo choononga chomwe chinagumula nyumba ndi kulowa m’mphuno za adani a Allah ndi kutulukira kokhalira kwawo. Chinkangowagwetsa chafufumimba kotero kuti anthu adali lambilambi ngati mathunthu a mitengo ya kanjedza.

التفاسير: