Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

external-link copy
44 : 8

وَإِذۡ يُرِيكُمُوهُمۡ إِذِ ٱلۡتَقَيۡتُمۡ فِيٓ أَعۡيُنِكُمۡ قَلِيلٗا وَيُقَلِّلُكُمۡ فِيٓ أَعۡيُنِهِمۡ لِيَقۡضِيَ ٱللَّهُ أَمۡرٗا كَانَ مَفۡعُولٗاۗ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ

Ndipo (kumbukirani) pamene anakuonetsani iwo m’maso mwanu, pamene munakumana nawo kuti iwo ndi ochepa, (owerengeka, kuti mukhale ndi chidwi chomenyana nawo), ndiponso anakuchepetsani kwambiri m’maso mwawo (kuti iwo aone kuti nkosafunika kukonzekera kwambiri chifukwa chakuchepa kwa omenyana nawowo), kuti Allah akwaniritse chimene adalamula kuchitika. Kwa Allah Yekha ndiko kobwerera zinthu zonse. info
التفاسير: