Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

Nûh

external-link copy
1 : 71

إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦٓ أَنۡ أَنذِرۡ قَوۡمَكَ مِن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ

Ndithu Ife tidamtuma Nuh kwa anthu ake, (ndikumuuza kuti): “Chenjeza anthu ako chisadawafike chilango chowawa.” info
التفاسير:

external-link copy
2 : 71

قَالَ يَٰقَوۡمِ إِنِّي لَكُمۡ نَذِيرٞ مُّبِينٌ

Adanena (Nuh): “E inu anthu anga! Ndithu ine ndimchenjezi kwa inu woonekera poyera (wolongosola za uthenga wa Mbuye wanu m’chiyankhulo chimene mukuchidziwa).” info
التفاسير:

external-link copy
3 : 71

أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَٱتَّقُوهُ وَأَطِيعُونِ

“Mpembedzeni Allah ndipo rnuopeni ndikutinso mundimvere (pazimene ndikukulangizani).” info
التفاسير:

external-link copy
4 : 71

يَغۡفِرۡ لَكُم مِّن ذُنُوبِكُمۡ وَيُؤَخِّرۡكُمۡ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمًّىۚ إِنَّ أَجَلَ ٱللَّهِ إِذَا جَآءَ لَا يُؤَخَّرُۚ لَوۡ كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

“(Ngati mutero) adzakukhululukirani machimo anu ndi kukutalikitsirani moyo wanu kufikira m’nthawi imene yaikidwa (kuti ndiwo malire a kutalika kwa moyo). Ndithu nthawi ya Allah ikabwera siyichedwetsedwa (ngakhale pang’ono) mukadakhala mukudziwa.” info
التفاسير:

external-link copy
5 : 71

قَالَ رَبِّ إِنِّي دَعَوۡتُ قَوۡمِي لَيۡلٗا وَنَهَارٗا

Adanena (Nuh): “E Mbuye wanga! Ndithu ine ndaitanira anthu anga (ku chikhulupiliro) usiku ndi usana (popanda kufooka).” info
التفاسير:

external-link copy
6 : 71

فَلَمۡ يَزِدۡهُمۡ دُعَآءِيٓ إِلَّا فِرَارٗا

“Kuitana kwanga sikudaonjezere (chilichonse) koma kuthawa basi (kuchikhulupiliro Chanu).” info
التفاسير:

external-link copy
7 : 71

وَإِنِّي كُلَّمَا دَعَوۡتُهُمۡ لِتَغۡفِرَ لَهُمۡ جَعَلُوٓاْ أَصَٰبِعَهُمۡ فِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَٱسۡتَغۡشَوۡاْ ثِيَابَهُمۡ وَأَصَرُّواْ وَٱسۡتَكۡبَرُواْ ٱسۡتِكۡبَارٗا

Ndipo ine nthawi iliyonse ndikawaitanira (ku chikhulupiliro Chanu) kuti mwakhululukire, akuika zala zawo m’makutu mwawo (kuti asamve uthenga Wanu), ndipo akudziphimba ndi nsalu zawo (kuti asaone nkhope yanga), ndipo akupitiriza kukana kwawo ndi kudzikweza kwakukulu. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 71

ثُمَّ إِنِّي دَعَوۡتُهُمۡ جِهَارٗا

Kenaka ine ndawaitanira (kwa Inu) ndi mawu ofuula, info
التفاسير:

external-link copy
9 : 71

ثُمَّ إِنِّيٓ أَعۡلَنتُ لَهُمۡ وَأَسۡرَرۡتُ لَهُمۡ إِسۡرَارٗا

Kenakanso (ine ndawaitanira) molengeza poyera ndiponso mwachinsinsi mobisa. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 71

فَقُلۡتُ ٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ إِنَّهُۥ كَانَ غَفَّارٗا

Choncho ndidati (kwa anthu anga): Pemphani kwa Mbuye wanu chikhululuko (pa kukana kwanu ndi kutonza kwanu), ndithu Iye ali Wokhululuka kwambiri. info
التفاسير: