[60] Allah ndiyekhayo woti nkumpembedza. Palibe wina wompembedza mwa choonadi koma Iye basi. Padziko lonse lapansi ndi kumwamba palibe mwini mphamvu zoposa wogonjetsa chilichonse koma Iye Yekha basi. Iye ndiYemwe amadzetsa zabwino ndikubweretsa zoipa, osati wina aliyense. Iye Ngwamoyo wamuyaya, moyo wopanda chiyambi ndiponso wopanda malekezero. Iye Ngwachikhalire kuyendetsa zinthu za zolengedwa Zake. Thambo ndi nthaka adazikhazikitsa. Apa nkuti mneneri Isa (Yesu) asanamlenge. Choncho, Isa (Yesu) sali Mulungu koma ndimmodzi wa aneneri.
[61] Tanthauzo la ndime iyi nkuti yakuvumbulukira iwe Muhammad (s.a.w) iyi Qur’an mwa choonadi popanda chipeneko kuti idachokera kwa Allah. Yatsika kupyolera mkudziwa kwake kuti itsimikizire zimene zidali m’mabuku a patsogolo pake. Ndipo pa zimenezi angelo ndimboni.