[294] Apa Allah akuti kodi sukuona luso la Allah pa zopangapanga Zake ndi mphamvu Zake zoposa momwe amautambasulira mthunzi nthawi yamasana kuti munthu akhale pamthunzi ndikupeza mpumulo wabwino kuchoka mkutentha kwa dzuwa. Pakadapanda mthunzi ndiye kuti munthu akadatenthedwa ndi dzuwa ndikusowetsedwa mtendere pa moyo wake. Ndipo Allah akadafuna akadauleka mthunzi kuti ukhale pamalo amodzi. Koma Iye ndi mphamvu Zake zoposa adaupanga kukhala wosinthasintha.