Tradução dos significados do Nobre Qur’an. - Tradução para a língua chachio - Khalid Ibrahim Batyala

Número de página:close

external-link copy
89 : 11

وَيَٰقَوۡمِ لَا يَجۡرِمَنَّكُمۡ شِقَاقِيٓ أَن يُصِيبَكُم مِّثۡلُ مَآ أَصَابَ قَوۡمَ نُوحٍ أَوۡ قَوۡمَ هُودٍ أَوۡ قَوۡمَ صَٰلِحٖۚ وَمَا قَوۡمُ لُوطٖ مِّنكُم بِبَعِيدٖ

“Ndipo E inu anthu anga! Kutsutsana nane kusakuchimwitseni kuopera kuti chingakupezeni chonga chimene chidawapeza anthu a Nuh kapena anthu a Hûd kapenanso anthu a Swaleh; ndipo anthu a Luti sali kutali ndi inu.” info
التفاسير:

external-link copy
90 : 11

وَٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِۚ إِنَّ رَبِّي رَحِيمٞ وَدُودٞ

“Ndipo mpempheni chikhululuko Mbuye wanu ndipo lapani kwa Iye (posiya machimo ndikuchita zabwino). Ndithu Mbuye wanga Ngwachisoni Ngwachikondi chochuluka (kwa anthu Ake).” info
التفاسير:

external-link copy
91 : 11

قَالُواْ يَٰشُعَيۡبُ مَا نَفۡقَهُ كَثِيرٗا مِّمَّا تَقُولُ وَإِنَّا لَنَرَىٰكَ فِينَا ضَعِيفٗاۖ وَلَوۡلَا رَهۡطُكَ لَرَجَمۡنَٰكَۖ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡنَا بِعَزِيزٖ

(Iwo) adati: “E iwe Shuaib! Sitikumvetsa zambiri mwa zomwe ukunena. Ndipo ife tikukuona wofooka mwa ife. Pakadapanda akubanja lako, tikadakugenda ndi miyala. Ndipo ulibe ulemelero pa ife (koma tikusunga ulemu wa anthu akubanja lako).”[225] info

[225] Anthu ake ankamuuza izi zoti sakumvetsa zomwe iye anawauza mwachibwana, nawafanizira malangizo akewo monga malangizo a munthu wozunguzika.

التفاسير:

external-link copy
92 : 11

قَالَ يَٰقَوۡمِ أَرَهۡطِيٓ أَعَزُّ عَلَيۡكُم مِّنَ ٱللَّهِ وَٱتَّخَذۡتُمُوهُ وَرَآءَكُمۡ ظِهۡرِيًّاۖ إِنَّ رَبِّي بِمَا تَعۡمَلُونَ مُحِيطٞ

(Iye) adati: “E inu anthu anga! Kodi anthu akubanja kwanga ndiwo olemekezeka kwambiri kwa inu kuposa Allah? Ndipo mwamuyika Iye (Allah) kukhala kumbuyo kwa misana yanu. Ndithu Mbuye wanga zonse zimene mukuchita akuzidziwa bwinobwino.” info
التفاسير:

external-link copy
93 : 11

وَيَٰقَوۡمِ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنِّي عَٰمِلٞۖ سَوۡفَ تَعۡلَمُونَ مَن يَأۡتِيهِ عَذَابٞ يُخۡزِيهِ وَمَنۡ هُوَ كَٰذِبٞۖ وَٱرۡتَقِبُوٓاْ إِنِّي مَعَكُمۡ رَقِيبٞ

“Ndipo E anthu anga! Chitani (zimene mufuna) mmene mungathere; inenso ndichita chimodzimodzi (mmene ndingathere). Posachedwapa mudziwa ndani chimufike chilango chomsambula, ndipo ndani wabodza. Ndipo dikirani inenso ndidikira pamodzi ndi inu.” info
التفاسير:

external-link copy
94 : 11

وَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا نَجَّيۡنَا شُعَيۡبٗا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةٖ مِّنَّا وَأَخَذَتِ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ ٱلصَّيۡحَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دِيَٰرِهِمۡ جَٰثِمِينَ

Ndipo pamene lamulo Lathu lidadza, tidampulumutsa Shuaib pamodzi ndi amene adakhulupirira naye, mwachifundo Chathu. Ndipo amene adachita zoipa, phokoso lidawachotsa moyo, tero kudawachera m’nyumba zawo ali lambilambi (atafa). info
التفاسير:

external-link copy
95 : 11

كَأَن لَّمۡ يَغۡنَوۡاْ فِيهَآۗ أَلَا بُعۡدٗا لِّمَدۡيَنَ كَمَا بَعِدَتۡ ثَمُودُ

Ndiye ngati sadakhalemo. Tamverani! Adaonongeka (anthu) a ku Madiyan monga momwe adaonongekera Asamudu! info
التفاسير:

external-link copy
96 : 11

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَا وَسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٍ

Ndipo ndithu tidamtuma Mûsa pamodzi ndi zozizwitsa zathu ndi umboni woonekera. info
التفاسير:

external-link copy
97 : 11

إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَٱتَّبَعُوٓاْ أَمۡرَ فِرۡعَوۡنَۖ وَمَآ أَمۡرُ فِرۡعَوۡنَ بِرَشِيدٖ

Kwa Farawo ndi nduna zake. Koma iwo adatsata lamulo la Farawo, ndipo lamulo la Farawo siloongoka. info
التفاسير: