[164] Apa atchula chilango chowapatsa anthu owononga, amene amafwamba anthu m’njira zawo. Anthu otere alandire zilango izi:- (a) Ngati akungopha oyenda m’njiramo popanda kuwatengera chuma chawo akawapha, iwo akagwidwa chiweruzo chawo nkuphedwa nawonso. (b) Ngati akupha ndi kulanda chuma, atagwidwa chiweruzo chawo nkuphedwa. Ndipo akaphedwa choncho awapachike pa mtanda kwamasiku atatu asanawaike m’manda. Kapena choyamba awaweruze kuti apachikidwe ali moyo. Ndipo akatsala pang’ono kufa, awatsitse ndi kuwamaliza. (c) Ngati amangolanda chuma chokha popanda kupha, akagwidwa chiweruzo chawo nkuti adulidwe dzanja lakudzanjadzanja aliyense ndi phazi lakumanzere. Kapena dzanja lamanzere ndi phazi ladzanjadzanja (d) Ngati saapha ndiponso salanda chuma, koma amangovutitsa anthu ndi kuwaopseza, chiweruzo chawo nkuwachotsa m’dzikomo kuwapititsa kwina nkuwapatsa ukaidi kumeneko, kapena kuwanjata m’dziko momwemo.