[244] Omasulira Qur’an adati Allah Mwini wake adalonjeza udindo woisunga Qur’an ndi kuiteteza kuti anthu asathe kuikapo manja awo posintha ndondomeko ya mawu ake kapena matanthandauzo ake, poonjezerapo malembo ena kapena kuchepetsa monga momwe zidachitikira ndi mabuku ena omwe Allah adawasiira anthu kuti awasunge ndi kuwateteza.
Qur’an yomwe tikuwerenga lero ndi yomweyo imene idalinso kuwerengedwa m’nthawi ya Mtumiki Muhammad (s.a.w). Palibe mawu oonjeza kapena kuchotsa.
[245] Allah akuti akadawatsekulira makomo akumwamba monga momwe adafunira nakwerako nkuona ufumu wa Allah ndi angelo ali yakaliyakali, sakadakhulupilirabe chifukwa chakuuma kwa mitima yawo. Chimene akadanena nkuti mitu yazungulira.